UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khalani Otsimikiza za Cikondi Cosasintha ca Yehova
Yehova amakuonani kuti ndinu amtengo wapatali. (Yes. 43:4) Yehova anakukokelani kwa iye komanso ku gulu lake. Ndipo pamene munadzipatulila na kubatizika, munakhala ake a Yehova. Iye adzakusamalilani monga cuma cake capadela ngakhale panthawi zovuta. Adzakuonetsani cikondi cake cosasintha kupitila m’gulu lake.—Sal. 25:10.
Kuona mmene gulu la Yehova lathandizila anthu ake pa matsoka a zacilengedwe m’zaka zaposacedwapa, kungatilimbikitse kuyamikila kwambili cikondi cake cosasintha.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI LIPOTI YA 2019 YA KOMITI YA OGWILIZANITSA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
Kodi Komiti ya Ogwilizanitsa inakonzekeletsa bwanji maofesi a nthambi padziko lonse kuti azicitapo kanthu mwamsanga pakacitika matsoka?
Kodi gulu la Yehova linapeleka bwanji thandizo pa nthawi ya tsoka ku Indonesia na ku Nigeria?
N’ciani cakufikani pamtima mukaganizila mmene gulu lacitila zinthu pa nthawi ya mlili wa COVID-19?