CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Sankhani Mwanzelu Munthu Womanga Naye Banja
Solomo anacita zinthu mopanda nzelu mwa kukwatila akazi opembedza mafano (1 Maf. 11:1, 2; w18.07 18 ¶7)
M’kupita kwa nthawi, akazi amene Solomo anakwatila anapatutsa mtima wake na kuucotsa kwa Yehova (1 Maf. 11:3-6; w19.01 15 ¶6)
Yehova anamukwiyila kwambili Solomo (1 Maf. 11:9, 10; w18.07 19 ¶9)
Mawu a Mulungu amalangiza Akhristu amene afuna kuloŵa m’banja kuti ayenela kukwatila “kokha mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Koma sikuti ngati munthu ni wobatizika, ndiye kuti basi angakhale mwamuna kapena mkazi woyenelela. Dzifunseni kuti, ‘Kodi munthuyu adzanithandiza kupitiliza kulambila Yehova na mtima wonse? Kodi waonetsa kwa utali wotani kuti amam’konda kwambili Yehova?’ Musanagwilizane zokwatilana na munthu, muyenela kukhala na nthawi yokwanila yomudziŵa bwino.