CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Asa Anacita Zinthu Molimba Mtima—Kodi Inunso Mumatelo?
Mokangalika, Asa anakhalila kumbuyo kulambila koona (1 Maf. 15:11, 12; w12 8/15 8 ¶4)
Asa anasonyeza kuti anali kuona kulambila Yehova kukhala kofunika kwambili kuposa mgwilizano wake na acibale (1 Maf. 15:13; w17.03 19 ¶7)
Asa analakwitsapo zinthu zina. Koma Yehova anamuonabe kuti anali wokhulupilika cifukwa ca makhalidwe ake abwino (1 Maf. 15:14, 23; it-1 184-185)
DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi kulambila koona nimakukondadi? Kodi nimaleka kugwilizana na aliyense amene wasiya Yehova, ngakhale amene ni wacibale wanga?’—2 Yoh. 9, 10.