CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Pemphelo Linasonkhezela Yehova Kucitapo Kanthu
Yehova anauza Hezekiya kuti sacila matenda ake (2 Maf. 20:1; ip-1 394 ¶23)
Mwacikhulupililo, Hezekiya anapempha Yehova kuti akumbukile kukhulupilika kwake (2 Maf. 20:2, 3; w17.03 21 ¶16)
Mapemphelo a Hezekiya anasonkhezela Yehova kucitapo kanthu (2 Maf. 20:4-6; g01 7/22 13 ¶4)
Mapemphelo athu angasonkhezele Yehova kucita zinthu zimene sakanacita tikanapanda kum’pempha. Kodi cocitika ici cakuphunzitsani ciyani pa nkhani yocondelela Yehova m’pemphelo?