LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 July masa. 3-16
  • “Kuteteza ndi Kukhazikitsa Mwalamulo” Nchito ya Uthenga Wabwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Kuteteza ndi Kukhazikitsa Mwalamulo” Nchito ya Uthenga Wabwino
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Kufuna-funa Nzelu mwa Kuŵelenga Baibo Tsiku Lililonse
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Lembani Mmene Mwapitila Patsogolo
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 July masa. 3-16
Zithunzi: 1. Gathie na Marie Barnett. 2. M’bale Kokkinakis na ena m’Khoti Lomenyela Ufulu wa Anthu ku Ulaya. 3. Mboni za Yehova m’Khoti lochedwa Rostov Regional Court ku Russia. 4. Gulu la abale lili panja pa Khoti lopanga malamulo ku South Korea.

Kokkinakis v. Greece: Droit réservé

Mozungulila, kucokela pamwamba kumanzele kupita ku lamanja: Mlandu wa West Virginia State Board of Education na Barnette; wa Kokkinakis na Greece; wa Taganrog LRO Komanso Ena na Russia; Wa Cha Komanso Ena na South Korea

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

“Kuteteza ndi Kukhazikitsa Mwalamulo” Nchito ya Uthenga Wabwino

Pamene otsutsa anayesa kuletsa Aisiraeli kumanga kacisi, omangawo anacita zonse zotheka kuti mwalamulo akhale na ufulu wopitiliza kumanga. (Ezara 5:11-16) Mofananamo, masiku ano Akhristu amacita zonse zotheka kuti akhalile kumbuyo nchito ya uthenga wabwino na kuikhazikitsa mwalamulo. (Afil. 1:7) Kuti izi zitheke, Dipatimenti ya Zamalamulo inakhazikitsidwa ku likulu mu 1936. Masiku ano, Dipatimenti ya Zamalamulo ku Likulu ndiyo imayang’anila nchito yoteteza mwalamulo zinthu za Ufumu padziko lonse. Kodi dipatimentiyi yathandiza bwanji pa nchito ya Ufumu? Nanga yawapindulila bwanji anthu a Mulungu?

ONELELANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE DIPATIMENTI YA ZAMALAMULO KU LIKULU IMACITA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi ni mavuto otani okhudza za malamulo amene Mboni za Yehova zakumanapo nawo?

  • Kodi tinapambanapo milandu iti? Pelekani citsanzo

  • Nanga n’ciyani cimene aliyense wa ife angacite pothandiza “kuteteza ndi kukhazikitsa mwalamulo” uthenga wabwino?

  • Pa webusaiti yathu, ni pa mbali iti maka-maka pamene tingapezepo nkhani za malamulo zokhudza anthu a Mulungu, komanso maina a Mboni za Yehova zimene zili m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo?

Ngati pamene mukulalikila, apolisi akuuzani kuti mukuphwanya lamulo, musayese kuthana nazo nokha mwa kuwauza kuti muli na ufulu wolalikila. M’malomwake, mwaulemu muyenela kuwamvela nthawi yomweyo. Ngati wakulamulani ni wapolisi kuti muleke kulalikila, mosamala tengani nambala ya baji yake komanso ya dela limene amaseŵenzela, ngati n’zotheka. Kenako, dziŵitsani akulu mwamsanga, ndipo iwo adzakambilana na ofesi ya nthambi kuti apemphe thandizo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani