LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 September tsa. 13
  • Thandizani Anthu Osapembedza Kudziŵa Mlengi Wawo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Thandizani Anthu Osapembedza Kudziŵa Mlengi Wawo
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Kulalikila Anthu Osapembedza Mowafika pa Mtima
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kuseŵenzetsa Mwaluso Zida Zophunzitsila za mu Thuboksi Yathu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Kuphunzitsa Coonadi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Pendani Umboni
    Galamuka!—2021
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 September tsa. 13
Mlongo akulalikila mzimayi wa ku Asia.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Thandizani Anthu Osapembedza Kudziŵa Mlengi Wawo

Kodi mumazengeleza kulalikila anthu osapembedza poganiza kuti sadzamvetsela uthenga wanu? Ngati n’conco, kumbukilani kuti anthu ambili osapembedza, kuphatikizapo osakhulupilila Mulungu, afika pokhala Mboni za Yehova. Nthawi zambili, iwo anali kungofunika kuwathandiza kupeza umboni wakuti Mulungu aliko.—Aroma 1:20; 10:14.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KUMBUKILANI—ANTHU OPANDA CIKHULUPILILO ANGAPEZE CIKHULUPILILO!—ANTHU OSAPEMBEDZA, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:

Kodi cocitika ca Tommaso cakuthandizani bwanji kukhala na maganizo oyenela pa nkhani yolalikila anthu osapembedza?

Mmene mungacitile zimenezi

Ngati munthu wakamba kuti sakhulupilila kuti Mulungu aliko, khalani wokoma mtima, wosamala, komanso onetsani cidwi ceniceni pa maganizo ake na mmene akumvela pa nkhaniyo. (2 Tim. 2:24) Kambilanani naye nkhani zimene zingamucititse cidwi. Kodi ni womasuka kukambilana naye umboni umene wathandiza ambili kukhulupilila Mlengi? Ngati n’conco, seŵenzetsani zofalitsa na mavidiyo amene anakonzedwela anthu otelo. Bulosha ya Chichewa yakuti Kodi Zamoyo Zinacita Kulengedwa? komanso yakuti Mmene Moyo Unayambila—Mafunso 5 Ofunika Kwambili, aikidwamo mu Thuboksi yathu n’colinga cakuti tisamavutike kuwapeza.

Poyamba, mwina mungacite mantha kukambilana za coonadi na munthu amene sakhulupilila kuti Mulungu aliko. Bwanji osapempha wofalitsa waluso kuti akuthandizeni? Kumbukilani kuti Yehova angatithandize kuwafika pa mtima anthu a maganizo abwino, ngakhale amene sakhulupilila kuti Mulungu aliko.—Mac. 13:48.

Bulosha ya Chichewa yakuti “Kodi Zamoyo Zinacita Kulengedwa?”
Bulosha yakuti “Mmene Moyo Unayambila—Mafunso 5 Ofunika Kwambili.”
    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani