Mungasankhe Mmene Tsogolo Lanu Lidzakhalile
Zaka pafupifupi 3,500 zapitazo, Yehova Mulungu anauza olambila ake zimene anayenela kucita kuti akhale na tsogolo labwino. Iye anati: “Ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi tembelelo pamaso panu. . . Conco inuyo ndi mbadwa zanu musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.”—Deuteronomo 30:19.
Kuti anthuwo akhale na tsogolo labwino, anafunika kusankha mwanzelu. N’zimenenso ife tiyenela kucita masiku ano. Baibo imatiuza mmene tingasankhile tsogolo labwino. Imati tiyenela ‘kukonda Yehova Mulungu wathu na kumvela mawu ake.’—Deuteronomo 30:20.
KODI TINGACITE CIANI KUTI TIZIKONDA YEHOVA NA KUMVELA MAWU AKE?
PHUNZILANI BAIBO: Kuti muzikonda Yehova, coyamba muyenela kuphunzila za iye m’Baibo. Pamene muphunzila, mudzaona kuti iye ni Mulungu wacikondi amene amakufunilani zabwino. Amakupemphani kuti muzipemphela kwa iye “cifukwa amakudelani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Baibo imati ngati muyesetsa kuyandikila Mulungu, “iyenso adzakuyandikilani.”—Yakobo 4:8.
MUZISEŴENZETSA ZIMENE MUMAPHUNZILA: Kumvela Mulungu kumatanthauza kumvela malangizo ake anzelu opezeka m’Baibo. Mukatelo, ‘mudzakhala ndi moyo wopambana, ndipo mudzacita zinthu mwanzelu.’—Yoswa 1:8.
a Maphunzilowa amapezeka m’zinenelo 7, kuphatikizapo ci Chinese Mandarin, ci Chinese Cantonese, komanso Cizungu.