NKHANI YOPHUNZLA 11
NYIMBO 57 Tilalikile kwa Anthu a Makhalidwe Onse
Tengelani Citsanzo ca Yesu ca Kulalikila Mokangalika
“Ambuye anasankha anthu ena . . . n’kuwatumiza awiliawili kuti atsogole kupita mumzinda ndi malo alionse kumene iye ankafunika kudzapitako.”—LUKA 10:1.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Njila zinayi zimene mungakhalile okangalika mu ulaliki ngati Yesu.
1. Ndi khalidwe liti limasiyanitsa anthu a Yehova ndi anthu amene amati naonso ndi Akhristu?
CIMODZI cimasiyanitsa atumiki a Yehova ndi anthu amene amati naonso ndi Akhristu, ndi kukangalikaa kwawo pogwila nchito yolalikila. (Tito 2:14) Komabe, nthawi zina zingakhale zovuta kuti mukhale osangalala pogwila nchito yolalikila. Mwina mungagwilizane ndi zimene mkulu wina wakhama ananena kuti, “Nthawi zina ndimakhala ndilibe cifuno cogwilako nchito yolalikila.”
2. Ndi zifukwa ziti zingacititse kuti nthawi zina zikhale zovuta kukhalabe okangalika polalikila?
2 N’kutheka kuti timasangalala kwambili kugwilako nchito zina polambila Yehova kuposa mmene timamvela tikamagwila nchito yolalikila. N’cifukwa ciyani? Cifukwa pamene tikumanga komanso kusamalila Nyumba za Ufumu, kapena pamene tikuthandiza abale athu akagweledwa tsoka kapenanso kuwalimbikitsa, tingaone zotulukapo zabwino mwamsanga ndipo tingamve bwino. Tikamagwila nchito ndi abale athu, timasangalala ndi mtendele ndipo timaonetsana cikondi. Timadziwanso kuti iwo amayamikila zimene timawacitila. Pomwe kumbali ina, tingakhale tikulalikila m’gawo kwa zaka, koma anthu amene akulandila uthenga wathu angakhale ocepa. Ndipo ena angakhale kuti akuukanilatu uthenga wathu. Tidziwanso kuti pamene mapeto akuyandikila, anthu azititsutsa kwambili. (Mat. 10:22) Ndiye n’ciyani cingatithandize kukhalabe okangalika komanso kuwonjezela cangu cathu pa nchito yolalikila?
3. Kodi Luka 13:6-9 itiphunzitsa ciyani za kukangalika kwa Yesu?
3 Kukambilana citsanzo ca Yesu kungatithandize kukhalabe okangalika pogwila nchito yolalikila. Yesu sanaleke kukhalabe wokangalika pocita utumiki wake. Ndipo pamene nthawi inali kupita, iye anawonjezela cangu cakeco. (Welengani Luka 13:6-9.) Yesu m’fanizo lake, anayelekezela nchito yake ndi munthu wosamalila munda wampesa yemwe anagwila nchito molimbika kwa zaka zitatu kusamalila mtengo wa mkuyu umene sunabeleke zipatso. Nayenso Yesu anatha zaka zitatu akulalikila kwa Ayuda, koma ambili a iwo sanalabadile uthenga wake. Wosamalila munda wampesa sanataye ciyembekezo cakuti tsiku lina mtengo wa mkuyuwo udzabeleka zipatso. Nayenso Yesu sanataye ciyembekezo pa anthu amene anali kuwalalikila cakuti angasinthe, ndipo sanacepetse cangu cake pa nchitoyo. M’malomwake, Yesu anawonjezela cangu cake kuti awafike pa mtima.
4. Tingatengele citsanzo ca Yesu pa mbali zinayi ziti?
4 M’nkhani ino, tikambilane mmene Yesu anaonetsela kukangalika kwake makamaka pa miyezi 6 yothela ya utumiki wake. (Luka 10:1) Tikamatsatila zimene anaphunzitsa ndi kutengela zimene anacita, ifenso tingakhale okangalika. Tiyeni tikambilane citsanzo ca Yesu pa mbali zinayi izi: (1) Anaika patsogolo kucita cifunilo ca Yehova, (2) analabadila maulosi a m’Baibulo, (3) anadalila thandizo la Yehova, ndipo (4) anakhalabe ndi cidalilo cakuti ena adzamvetsela uthenga wake.
ANAIKA PATSOGOLO KUCITA CIFUNILO CA YEHOVA
5. N’ciyani cionetsa kuti Yesu anaika patsogolo kucita cifunilo ca Mulungu?
5 Yesu analalikila mokangalika “uthenga wabwino wa Ufumu” podziwa kuti ndiyo nchito imene Mulungu anafuna kuti acite. (Luka 4:43) Kwa Yesu, nchitoyi inali yofunika kwambili kuposa cina ciliconse. Anali ‘kuyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi’ kukaphunzitsa ngakhale kumapeto kwenikweni kwa moyo wake. (Luka 13:22) Anaphunzitsanso anthu ena kuti azigwila nawo nchito yolalikila.—Luka 10:1.
6. Kodi nchito yolalikila imakhudzana motani ndi nchito zina zimene timagwila potumikila Yehova? (Onaninso cithunzi.)
6 Masiku anonso, Yehova ndi Yesu amafuna kuti tiziona nchito yolalikila kukhala yofunika kwambili mu umoyo wathu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Nchito iliyonse imene timagwila potumikila Yehova imakhudzana kwambili ndi nchito yolalikila. Timamanga malo olambilila kapena kutumikila pa Beteli kuti tipititse patsogolo nchito yolalikila. Timathandiza abale ndi alongo athu akagweledwa matsoka kuti ayambilenso kucita pulogilamu yawo yauzimu, imene imaphatikizapo kulalikila. Tikazindikila kufunika kwa nchito yolalikila komanso kukumbukila kuti ndiyo nchito yofunika imene Yehova afuna kuti ticite, tidzalimbikitsidwa kutengamo mbali nthawi zonse. Mkulu wina wa ku Hungary dzina lake János anafotokoza kuti, “Pa nchito zonse timagwilila Yehova, kulibe nchito ingalowe m’malo mwa nchito yolalikila. Nchitoyi ndiyo yofunika kwambili.”
Kulalikila uthenga wabwino ndiyo nchito yofunika kwambili imene Yehova ndi Yesu amafuna kuti tigwile masiku ano (Onani ndime 6)
7. N’cifukwa ciyani Yehova sakufuna kuti tisiye kulalikila? (1 Timoteyo 2:3, 4)
7 Tikamaona anthu mmene Yehova amawaonela, tidzawonjezela cangu cathu pa ulaliki. Iye akufuna kuti anthu ambili amvetsele uthenga wabwino ndi kucitapo kanthu. (Welengani 1 Timoteyo 2:3, 4.) Kuti zimenezi zitheke, iye amatiphunzitsa mokhalila alaliki ogwila mtima pofalitsa uthenga wopulumutsa moyo umenewu. Mwacitsanzo, bulosha lakuti Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila limafotokoza njila zimene tingayambile makambilano ndi colinga copanga ophunzila. Ngakhale anthu atati asalabadile uthenga wathu palipano, angadzakhale ndi mwayi womvetsela cisautso cacikulu cisanathe. Uthenga umene timaauza palipano ndi umene ungadzawasonkhezele kucitapo kanthu pa nthawiyo. Koma izi zingacitike kokha tikapitiliza kulalikila.
ANALABADILA MAULOSI A M’BAIBULO
8. Kodi kudziwa maulosi a m’Baibulo, kunamuthandiza bwanji Yesu kugwilitsa nchito nthawi yake mwanzelu?
8 Yesu anamvetsa mmene maulosi a m’Baibulo adzakwanilitsidwile. Anadziwa kuti adzacita utumiki wake kwa zaka zitatu ndi hafu. (Dan. 9:26, 27) Iye anadziwanso zimene maulosi ananena zokhudza imfa yake. (Luka 18:31-34) Popeza anali kudziwa zimene maulosi anali kunena, iye anagwilitsa nchito nthawi yake mwanzelu. Conco analalikila mokangalika kuti amalize nchito imene anapatsidwa.
9. Kodi kumvetsa maulosi a m’Baibulo kumatisonkhezela motani kulalikila mokangalika?
9 Timalalikila mokangalika cifukwa timamvetsa maulosi a m’Baibulo. Tikudziwa kuti nthawi yatsala yafupika. Timazindikila kuti zocitika za m’dzikoli komanso makhalidwe a anthu masiku ano, ndi umboni wakuti tili m’masiku otsiliza omwe Baibulo linakamba. Ulosi wa m’Baibulo umanenanso kuti mfumu yakum’mwela ndi mfumu yakumpoto zidzakankhana “mu nthawi yamapeto.” (Dan. 11:40) Timamvetsa kuti izi ziimila zimene zikucitika pakati pa ufumu wa padziko lonse wa Britain ndi America polimbana ndi Russia ndi maiko ogwilizana naye. Tidziwanso kuti mapazi a cifanizilo ofotokozedwa pa Danieli 2:43-45 akuimila ulamulilo wamphamvu wa padziko lonse wa Britain ndi America. Sitikaikila kuti monga anakambila maulosi a m’Baibulo, posacedwapa, inde posacedwapa, Ufumu wa Mulungu udzaphwanya maboma a anthu. Maulosi onsewa amavumbula pomwe tafika komanso kumene tikupita, ndipo amatilimbikitsa kulalikila mokangalika podziwa kuti kwatsala kanthawi kocepa.
10. Kodi maulosi a m’Baibulo angatilimbikitse kuti tizilalikila mokangalika m’njila zina ziti?
10 M’maulosi a m’Baibulo timapezamonso uthenga umene timafunitsitsa kuuzako ena. Mlongo wina yemwe akutumikila ku Dominican Republic dzina lake Carrie anati, “Ndikaganizila zinthu zabwino zimene Yehova watilonjeza, ndimalimbikitsidwa kuuzako ena zinthuzo.” Anawonjezela kuti: “Ndikaona mavuto amene anthu akukumana nawo masiku ano, ndimazindikila kuti nawonso ayenela kudziwa za malonjezo osangalatsa omwe Yehova watilonjeza.” Maulosi a m’Baibulo amatilimbikitsa kuti tisabwelele m’mbuyo cifukwa tidziwa kuti Yehova ndi amene akutithandiza kugwila nchito yolalikilayi. Leila yemwe akhala ku dziko la Hungary anati: “Yesaya 11:6-9 imandilimbikitsa kugawilako ena uthenga wabwino ngakhale aja amene amaoneka ngati sangaulandile. Ndipo ndidziwa kuti ndi thandizo la Yehova, wina aliyense angasinthe.” Christopher, m’bale wa ku Zambia anati: “Uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa pa dziko lonse monga inakambila Maliko 13:10. Ndimauona kukhala mwayi kukwanilitsako ulosi umenewu.” Nanga bwanji inu, ndi maulosi ati a m’Baibulo amene amakulimbikitsani kupitiliza kulalikila?
ANADALILA THANDIZO LA YEHOVA
11. N’cifukwa ciyani Yesu anafunika kudalila thandizo la Yehova kuti apitilize kulalikila mokangalika? (Luka 12:49, 53)
11 Yesu anadalila thandizo la Yehova kuti apitilize kulalikila mokangalika. Ngakhale kuti Yesu anali wosamala, iye anadziwa kuti uthenga wabwino wa Ufumu udzacititsa kuti anthu ambili akwiye komanso kuti amutsutse kwambili. (Welengani Luka 12:49, 53.) Atsogoleli acipembedzo sanakondwele ndi zimene Yesu anali kuphunzitsa. Conco mobwelezabweleza, anayesa kumupha. (Yoh. 8:59; 10:31, 39) Koma iye sanasiye kulalikila cifukwa anadziwa kuti Yehova anali naye. Yesu anati: “Iye sanandisiye ndekha cifukwa ndimacita zinthu zimene zimamusangalatsa nthawi zonse.”—Yoh. 8:29.
12. Kodi Yesu anawakonzekeletsa motani ophunzila ake kupitiliza kulalikila mokangalika akakumana ndi mazunzo?
12 Yesu anakumbutsa ophunzila ake kuti ayenela kudalila Yehova kuti awathandize. Mobwelezabweleza, iye anawatsimikizila kuti Yehova adzawathandiza ngakhale pamene akumana ndi mazunzo. (Mat. 10:18-20; Luka 12:11, 12) Mpake kuti anawalimbikitsa kukhala ocenjela pogwila nchito yolalikila. (Mat. 10:16; Luka 10:3) Iye anawalangiza kuti sayenela kukakamiza anthu kumvetsela uthenga wawo. (Luka 10:10, 11) Ndipo anawauzanso kuti ayenela kuthawa akakumana ndi mazunzo. (Mat. 10:23) Ngakhale kuti Yesu anali wokangalika komanso anadalila Yehova, sanaike mwadala moyo wake pa ciopsezo.—Yoh. 11:53, 54.
13. N’ciyani cingakupatseni cidalilo cakuti Yehova adzakuthandizani?
13 Nafenso timafunikila thandizo la Yehova kuti tipitilize kulalikila mokangalika pamene ena akutitsutsa. (Chiv. 12:17) N’ciyani cingakupatseni cidalilo cakuti Yehova adzakuthandizani? Timapeza yankho m’pemphelo la Yesu la mu Yohane caputala 17. M’pemphelo limenelo, iye anapempha Yehova kuti ayang’anile atumwi. Ndipo Yehova anatelodi. Buku la Machitidwe limaonetsa mmene Yehova anathandizila atumwi kupitiliza kulalikila mokangalika ngakhale kuti anali kuzunzidwa. Yesu m’pemphelo lake, anapemphanso Yehova kuti ayang’anilenso onse amene adzakhulupilila uthenga wa atumwi. Pa anthu amenewo, inunso mulipo. Pemphelo la Yesu likali kugwila nchito masiku ano. Yehova adzakuthandizani monga anathandizila atumwi.—Yoh. 17:11, 15, 20.
14. Tidziwa bwanji kuti n’zotheka kupitiliza kulalikila mokangalika? (Onaninso cithunzi.)
14 Pamene mapeto akuyandikila, zingakhale zovutilapo kwa ife kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Koma Yesu anatitsimikizila kuti tidzakhala ndi thandizo lofunikila kuti tipitilize kulalikila mokangalika. (Luka 21:12-15) Monga mmene Yesu ndi ophunzila ake anacitila, nafenso timalola anthu kusankha okha kaya kumvetsela uthenga wathu kapena ayi, ndipo timapewa kukangana nawo. Ngakhale pamene nchito yathu yaletsedwa, abale athu saleka kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu cifukwa amadalila Yehova, osati mphamvu zawo. M’nthawi ya atumwi, Yehova anapatsa atumiki ake mphamvu. Mofananamo, iye amatipatsa mphamvu masiku ano kuti “nchito yolalikila icitike mokwanila” mpaka iye atakhutila. (2 Tim. 4:17) Musakaikile zakuti mukadalila Yehova, mudzapitiliza kulalikila mokangalika.
Ngakhale pamene nchito yathu yaletsedwa, ofalitsa okangalika amapeza njila zouzilako ena cikhulupililo cawo mosamala (Onani ndime 14)b
ANAKHALABE NDI CIDALILO CAKUTI ENA ADZAMVETSELA UTHENGA WAKE
15. N’ciyani cionetsa kuti Yesu anali ndi cidalilo cakuti anthu adzamvetsela uthenga wake?
15 Yesu anakhalabe ndi cidalilo cakuti anthu adzamvetsela uthenga wake. Izi zinam’thandiza kupitiliza kugwila nchito yake mwakhama. Mwacitsanzo, cakumapeto kwa caka ca 30 C.E., Yesu anaona kuti anthu anali kufuna kumvetsela uthenga wake, ndipo iye anawayelekezela ndi munda umene zipatso zake zinali zitaca. (Yoh. 4:35) Patapita pafupifupi caka cimodzi, iye anauza ophunzila ake kuti: “Pali zinthu zambili zofunika kukolola.” (Mat. 9:37, 38) Patapita nthawi, iye anakambanso kuti: “Pali zinthu zambili zofunika kukolola . . . Pemphani Mwiniwake wa munda kuti atumize anchito kukakolola.” (Luka 10:2) Yesu anali ndi cidalilo cakuti anthu adzamvetsela uthenga wabwino, ndipo anasangalala anthuwo atatelo.—Luka 10:21.
16. Kodi mafanizo a Yesu anathandiza bwanji ophunzila ake kuona ulaliki wawo moyenela? (Luka 13:18-21) (Onaninso cithunzi.)
16 Yesu anauza ophunzila ake kuti aziona uthenga wawo moyenela, ndipo izi zinawalimbikitsa kukhalabe okangalika. Mwacitsanzo, ganizilani mafanizo awili amene iye anakamba. (Welengani Luka 13:18-21.) Yesu anagwilitsa nchito fanizo la kanjele kampilu poonetsa kuti uthenga wa Ufumu udzafalikila m’njila yapadela ndipo anthu ambili adzaulandila. Anagwilitsanso nchito fanizo la zofufumitsa poonetsa mmene uthenga wa Ufumu unali kudzafalikila ndi kucititsa anthu kupanga masinthidwe aakulu amene sangaonekele m’kanthawi kocepa. Pofotokoza mafanizowa, Yesu anathandiza ophunzila ake kuona kuti uthenga umene anali kulalikila udzathandiza anthu ambili.
Monga mmene Yesu anacitila, nafenso timakhalabe n’cidalilo cakuti ena adzamvetsela uthenga wathu (Onani ndime 16)
17. N’zifukwa ziti zimatipangitsa kusasiya kulalikila?
17 Timalimbikitsidwa kupitiliza kulalikila mokangalika tikaona mmene nchito yathu ikuthandizila anthu ambili padziko lonse. Caka ciliconse, anthu acidwi ofika m’mamiliyoni amapezeka pa Cikumbutso ndipo timaphunzila nawo Baibulo. Anthu masauzande ambilimbili amabatizika ndi kuyamba kugwilako nchito yolalikila. Sitikudziwa kuti ndi anthu angati adzamvetsela uthenga wathu, koma cimene tidziwa n’cakuti Yehova akusonkhanitsa a khamu lalikulu omwe adzapulumuke cisautso cacikulu cimene cikubwela. (Chiv. 7:9, 14) Mwiniwake wa zokolola akali kuonabe kuti m’munda mukali anthu ambili amene angamvetsele uthenga wathu. Conco, tili ndi zifukwa zabwino zopitilizila kulalikila.
18. Kodi timafuna kuti anthu azindikile ciyani akationa?
18 Ophunzila a Yesu akhala akudziwika kaamba ka khama lawo pa nchito yolalikila. Anthu ataona mmene atumwi anali kulankhulila molimba mtima, “anazindikila kuti ankayenda ndi Yesu.” (Mac. 4:13) Nafenso timafuna kuti anthu akationa mu utumiki, azitha kuona kuti tikutengela citsanzo ca Yesu ca kukhala okangalika.
NYIMBO 58 Kusakila Anthu Okonda Mtendele
a KUFOTOKOZELA MAWU ENA: M’nkhani ino, mawu akuti “kukangalika” komanso akuti “cangu” atanthauza mzimu wofunitsitsa umene Akhristu amakhala nawo polambila Yehova.
b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mosamala, m’bale akulalikila mwamuna pamalo omwetsela mafuta.