LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 March masa. 20-25
  • Musaleke Kuyenda mwa Cikhulupililo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Musaleke Kuyenda mwa Cikhulupililo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • POSANKHA NCHITO
  • POSANKHA WOMANGA NAYE BANJA
  • GULU LATHU LIKATIPATSA MALANGIZO
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Mmene Tingathetsele Zikaiko Zathu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Pangani Zisankho Zokondweletsa Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 March masa. 20-25

NKHANI YOPHUNZILA 12

NYIMBO 119 Tikhale na Cikhulupililo

Musaleke Kuyenda mwa Cikhulupililo

“Tikuyenda mwa cikhulupililo, osati mwa zooneka ndi maso.”​—2 AKOR. 5:7.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Zimene tingacite kuti tisaleke kuyenda mwa cikhulupililo popanga zisankho zofunika.

1. N’ciyani cinapangitsa mtumwi Paulo kukhala wokhutila ndi umoyo wake?

PA NTHAWI ina, mtumwi Paulo anadzazindikila kuti watsala pang’ono kuphedwa. Ngakhale n’telo, iye anali wokhutila ndi umoyo wake. Ataganizila za umoyo wake, iye anati: “Ndathamanga pa mpikisanowu mpaka pamapeto. Ndakhalabe ndi cikhulupililo.” (2 Tim. 4:​6-8) Paulo anapanga zisankho zanzelu pa umoyo wake wacikhristu, ndipo sanakayike konse kuti Yehova anali kukondwela naye. Ifenso timafuna kupanga zisankho zabwino kuti Mulungu azikondwela nafe. Koma tingacite bwanji zimenezi?

2. Kodi kuyenda mwa cikhulupililo kumatanthauzanji?

2 Ponena za iyemwini ndi Akhristu ena okhulupilika, Paulo anati: “Tikuyenda mwa cikhulupililo, osati mwa zooneka ndi maso.” (2 Akor. 5:7) Kodi Paulo anatanthauzanji pamenepa? M’Baibulo, mawu akuti “kuyenda,” nthawi zina amatanthauza mmene munthu amasankha kukhalila pa umoyo wake. Munthu akamayenda mwa zooneka ndi maso cabe, amapanga zisankho pongotengela zimene amaona, kumva, komanso mmene akumvela m’thupi mwake. Koma munthu akamayenda mwa cikhulupililo, amaganizila zimene Yehova Mulungu akufuna asanapange zisankho. Zocita zake zimaonetsa kuti sakaika konse kuti akatsatila malangizo a Yehova a m’Baibulo, adzapindula palipano ndipo m’tsogolo adzam’patsa mphoto yaikulu.​—Sal. 119:66; Aheb. 11:6.

3. Timapindula motani tikamayenda mwa cikhulupililo? (2 Akorinto 4:18)

3 Komabe, tonsefe nthawi zina timapanga zisankho potengela zimene tikuona, kumva, komanso mmene tikumvela. Koma tingakumane ndi mavuto ngati izi ndiye zinthu zokhazo zimene timayendela popanga zisankho pa nkhani zikuluzikulu. Cifukwa? Zimene timaona ndi kumva nthawi zina zingatipusitse. Tikamapanga zisankho pongotengela zimene tikuona, kumva, komanso mmene tikumvela, tingacite zinthu zosakondweletsa Yehova. (Mlal. 11:9; Mat. 24:​37-39) Koma tikamayenda mwa cikhulupililo, nthawi zambili tizipanga zisankho zomwe ndi ‘zovomelezeka kwa Ambuye.’ (Aef. 5:10) Tikamatsatila malangizo a Mulungu, tidzakhala ndi mtendele wa mumtima ndipo tidzakhaladi acimwemwe. (Sal. 16:​8, 9; Yes. 48:​17, 18) Ndipo ngati sitileka kuyenda mwa cikhulupililo, tidzapeza moyo wosatha m’tsogolo.​—Welengani 2 Akorinto 4:18.

4. Kodi munthu angadziwe bwanji kuti akuyenda mwa cikhulupililo kapena mwa zooneka ndi maso?

4 Tingadziwe bwanji kuti tikuyenda mwa cikhulupililo kapena mwa zooneka ndi maso? Tonsefe tiyenela kudzifunsa kuti: “Kodi ndimayang’ana ciyani ndikamapanga zisankho? Kodi ndimangoyendela zimene ndikuona? Kapena kodi ndimatsogoleledwa ndi malangizo a Yehova?” Tiyeni tione mmene tingayendele mwa cikhulupililo pa mbali zitatu za umoyo wathu: posankha nchito, posankha womanga naye banja, komanso gulu lathu likatipatsa malangizo. Pa mbali iliyonse, tione zimene tiyenela kuganizilapo kuti tipange zisankho zabwino.

POSANKHA NCHITO

5. Kodi tifunika kuyang’ana pa ciyani posankha nchito?

5 Tonsefe timafuna kukhala ndi nchito yotithandiza kuzipezela zosowa za pa umoyo komanso za banja lathu. (Mlal. 7:12; 1 Tim. 5:8) Nchito zina zili ndi malipilo apamwamba kuposa zina. Munthu akamagwila nchito ya malipilo apamwamba, amatha kusamalila zosowa zake za tsiku ndi tsiku, komanso kusungako kenakake pambali. Koma nchito zina zimakhala ndi malipilo ocepelapo moti munthu amangokwanitsa kupeza zofunikila za banja lake. Conco n’zomveka kuti tikamasankha nchito, nthawi zambili timaganizila malipilo ake. Koma ngati ici ndiye cinthu cokha cimene munthu amaganizila, ndiye kuti akuyenda mwa zooneka ndi maso.

6. Tingayende bwanji mwa cikhulupililo posankha nchito? (Aheberi13:5)

6 Tikamayenda mwa cikhulupililo, tidzaganizilanso mmene nchito yathu ingakhudzile ubwenzi wathu ndi Yehova. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi nchitoyi idzafuna kuti ndizicita zinthu zimene Yehova amadana nazo?’ (Miy. 6:​16-19) ‘Kodi idzasokoneza umoyo wanga wauzimu kapena kodi ndizikhalanso kutali ndi banja langa kwa nthawi yaitali?’ (Afil. 1:10) Ngati yankho pa mafunso monga amenewa ndi lakuti inde, cingakhale canzelu kusaivomela nchitoyo ngakhale kuti nchito n’zovuta kupeza. Cifukwa cakuti timayenda mwa cikhulupililo, timapanga zisankho zoonetsa kuti Yehova adzatisamalila pa zimene tikufunikila.​—Mat 6:33; welengani Aheberi 13:5.

7-8. Kodi m’bale wina wa ku South America anaonetsa bwanji kuti akuyenda mwa cikhulupililo? (Onaninso cithunzi.)

7 Onani mmene m’bale wina wa ku South America dzina lake Javier,a anaonetsela kuti kuyenda mwa cikhulupililo kunali kofunika kwa iye. Iye anati: “N’nafunsila nchito ya pamwamba pa kampani pomwe ndinali. Nchitoyi inali ya kumtima kwanga komanso inali ndi malipilo owilikiza kawili malipilo amene n’nali kulandila.” Komabe iye anali kufunitsitsa kutumikila monga mpainiya. Iye anapitiliza kunena kuti: “N’naitanidwa ku ma intavyu a nchitoyo. Ndisanakumane ndi wondifunsa mafunso, ndinapemphela kwa Yehova kuti andithandize, ndili ndi cidalilo cakuti iye ndiye anali kudziwa zimene zinali zabwino koposa kwa ine. Ndinali kuifunitsitsa nchitoyi, koma sindinafune kuti indisokoneze kukwanilitsa zolinga zanga zauzimu.”

8 Javier anakamba kuti: “Pondifunsa mafunso, bwanayo anandiuza kuti ndizigwila ovataimu nthawi zambili. Ndinamuuza mokoma mtima kuti sindingathe kutelo cifukwa ca utumiki wanga.” Javier anakana kukwezedwa pa nchitopo. Pambuyo pa milungu iwili, iye anayamba upainiya. Ndipo patapita nthawi caka comweco, anasiya nchito yake n’kuyamba ina ya malipilo ocepa. Iye anati: “Yehova anamva mapemphelo anga, ndipo anandithandiza kupeza nchito imene imandilola kucita upainiya. Ndine wokondwela kwambili kukhala ndi nchito imene imandipatsa mpata wokulilapo wotumikila Yehova komanso abale anga.”

M’bale ali m’zovala zakunchito ndipo wanyamula cisoti codzitetezela kumutu akuonetsedwa ofesi yatsopano ndi woyang’anila nchitoyo. Woyang’anilayo akumupatsa mwayi womukweza pa nchito.

Ngati mwauzidwa kuti mudzakwezedwa pa nchito, kodi cisankho canu cidzaonetsa kuti ndinu wotsimikiza kuti Yehova ndiye adziwa zabwino koposa kwa inu? (Onani ndime 7-8)


9. Kodi mwaphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila Trésor?

9 Tingacite ciyani tikazindikila kuti nchito imene tikugwila sikutilola kuyenda mwa cikhulupililo? Onani zimene zinacitikila Trésor wa ku Congo. Iye anati: “Kwa ine, kulandila nchitoyi unali mwayi wosaonekaoneka. Ndalama zimene ndinali kulandila zinali zowilikiza katatu ndalama zimene ndinali kulandila pa nchito yanga yakale, ndipo anthu anali kundiona kuti ndine munthu wofunika kwambili.” Komabe, Trésor anali kuphonya misonkhano kawilikawili cifukwa cogwila ovataimu. Nthawi zina iye anali kukakamizidwa kuti abise zacinyengo zimene kampani yawo yacita. Trésor anali kufuna kuleka nchitoyi, koma anali kuda nkhawa akaganizila zokhala pa ulova. N’ciyani cinamuthandiza kugonjetsa manthawo? Iye anati: “Habakuku 3:​17-19 inandithandiza kumvetsa kuti ngakhale nchito yanga itatha, Yehova adzapeza njila yondisamalila. Conco ndinaisiya.” Anawonjezelanso kuti: “Mabwana ambili amaganiza kuti munthu angalole kutaya ciliconse, kuphatikizapo banja lake ndi moyo wake wauzimu, kuti asunge nchito yake. Ndine wosangalala kuti ndinateteza ubwenzi wanga ndi Yehova. Patapita caka cimodzi, Yehova anandithandiza kupeza nchito ina imene imandithandiza kukhala umoyo wosalila zambili, komanso kukhala ndi nthawi yocita zauzimu. Tikaika Yehova patsogolo, n’kutheka tingavutike kwa kanthawi, koma Yehova adzatisamalila.” Inde, tikamadalila malangizo a Yehova ndi malonjezo ake, tidzapitiliza kuyenda mwa cikhulupililo ndipo adzatidalitsa.

POSANKHA WOMANGA NAYE BANJA

10. Ndi zinthu ziti zingacititse kuti tiziyenda mwa zooneka ndi maso posankha womanga naye banja?

10 Ukwati ndi mphatso yocokela kwa Yehova, ndipo n’cibadwa kufuna kulowa m’banja. Mlongo akafunsilidwa ndi m’bale, angaganizile za umunthu wa m’baleyo, maonekedwe ake, komanso mbili yake. Angaganizilenso za mmene m’baleyo amagwilitsila nchito ndalama, maudindo a m’banja omwe ali nawo, komanso mmene mlongoyo amamvela akakhala ndi m’baleyo.b N’zoona kuti zinthu zimenezo n’zofunika. Komabe, ngati mlongo angaganizile zinthu zokhazi posankha womanga naye banja, angakhale kuti akuyenda mwa zooneka ndi maso.

11. Tingayende bwanji mwa cikhulupililo posankha womanga naye banja? (1 Akorinto 7:39)

11 Yehova amawanyadila kwambili alongo ndi abale athu amene amatsatila malangizo ake posankha womanga naye banja. Mwacitsanzo, iwo amatsatila malangizo akuti ayenela kuyembekeza mpaka atadutsa “pacimake pa unyamata” asanayambe cibwenzi. (1 Akor. 7:36) Posankha womanga naye banja, iwo amaika kwambili maganizo awo pa makhalidwe omwe Yehova amati ndiwo amacititsa munthu kukhala mwamuna wabwino kapena mkazi wabwino. (Miy. 31:​10-13, 26-28; Aef. 5:33; 1 Tim. 5:8) Munthu amene si Mboni akakopeka nawo, amapewa kukhala naye pa cibwenzi potsatila malangizo akuti azikwatiwa kokha “mwa Ambuye,” malinga ndi 1 Akorinto 7:39. (Welengani.) Iwo amapitiliza kuyenda mwa cikhulupililo ali ndi cidalilo cakuti Yehova adzawasamalila ndi kuwalimbikitsa kuposa mmene wina aliyense angacitile.​—Sal. 55:22.

12. Kodi mwaphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila Rosa?

12 Mvani zinacitikila Rosa, mpainiya wa ku Colombia. Nchito yake inam’pangitsa kuti azikambilana kawilikawili ndi mwamuna winawake amene sanali Mboni amene pambuyo pake anayamba kumufuna. Rosa anakopeka naye. Iye anati: “Anali kuoneka ngati munthu wabwino kwambili. Iye anali kuthandiza anthu m’dela lawo, ndipo anali ndi makhalidwe abwino. Ndinali kukonda mmene anali kucitila nane. Anali ndi zonse zimene n’nali kufuna mwa munthu amene ndingakwatilane naye, kungoti sanali Mboni.” Anakambanso kuti: “Zinali zovuta kumukana cifukwa pa nthawiyo n’nali wosungulumwa, ndipo n’nali kufuna kukwatiwa. Koma n’nali n’sanapeze munthu m’coonadi.” Ngakhale n’telo, Rosa sanangoika maganizo ake pa zooneka ndi maso. Anaganizila mmene cisankho cake pa nkhaniyi cidzakhudzila ubwenzi wake ndi Yehova. Conco anasiyilatu kukamba ndi mwamunayo, ndipo anaika maganizo ake pa kucita zinthu zauzimu. Posapita nthawi, iye anaitanidwa kukalowa Sukulu ya Alengezi a Ufumu, ndipo pano tinena ndi mpainiya wapadela. Rosa anatinso: “Yehova wadzaza mtima wanga ndi cimwemwe.” Kuyenda mwa cikhulupililo pa nkhani zokhudzana ndi cinthu cimene tikufunitsitsa sikopepuka, koma kucita zimenezo kumabweletsa madalitso.

GULU LATHU LIKATIPATSA MALANGIZO

13. N’ciyani cingatipangitse kuyenda mwa zooneka ndi maso gulu lathu likatipatsa malangizo?

13 Nthawi zambili gulu lathu limatipatsa malangizo otitsogolela pa kulambila kwathu. Malangizowo angacokele kwa akulu, oyang’anila dela, ofesi ya nthambi kapena Bungwe Lolamulila. Koma bwanji ngati pa nthawi ina sitinamvetse cifukwa cake abale atipatsa malangizo enaake? Tingayambe kukaikila ngati malangizowo adzakhala othandizadi. Tingafike ngakhale poika maganizo athu pa zophophonya za abale amene atipatsa malangizowo.

14. N’ciyani cingatithandize kuyenda mwa cikhulupililo gulu lathu likatipatsa malangizo? (Aheberi 13:17)

14 Tikamakhala ndi cikhulupililo, timakhala ndi cidalilo cakuti Yehova ndiye akuyendetsa zonse ndipo akudziwa mmene zinthu zilili. Cifukwa ca zimenezi, timamvela mwamsanga komanso mosanyinyilika. (Welengani Aheberi 13:17.) Timazindikilanso kuti kukhala womvela kumagwilizanitsa mpingo. (Aef. 4:​2, 3) Timadalilanso kuti ngakhale kuti abale amene akutitsogolela ndi opanda ungwilo, Yehova adzatidalitsa tikamawamvela. (1 Sam. 15:22) Ndipo ngati pali malangizo amene ayeneladi kusinthidwa, Yehova adzaonetsetsa kuti asinthidwa pa nthawi yake.​—Mika 7:7.

15-16. N’ciyani cinathandiza m’bale wina kuyenda mwa cikhulupililo ngakhale kuti anali kukaikila malangizo amene anapatsidwa? (Onaninso cithunzi.)

15 Tiyeni tikambilane cocitika coonetsa phindu limene limabwela tikamayenda mwa cikhulupililo. Ngakhale kuti ci Spanish ndi cofala ku Peru, anthu ambili amalankhula zinenelo za kumeneko. Cimodzi mwa zinenelo zimenezo ndi ci Quechua. Kwa zaka zingapo, abale olankhula cineneloci anali kufunafuna anthu olankhula cineneloci m’gawo. Komabe, pofuna kutsatila malamulo a boma, panapangidwa masinthidwe pa nkhani ya mmene ofalitsa angafikile anthu. (Aroma 13:1) Zotsatilapo zake zinali zakuti ena anadzifunsa ngati malangizowo adzakhaladi othandiza. Komabe, cifukwa coti abalewa anatsatila malangizowo, Yehova anadalitsa khama lawo pofufuza anthu olankhula ci Quechua.

16 Kevin, mkulu mumpingo wa ci Quechua, anali mmodzi wa anthu amene anali ndi nkhawa. Iye anakamba kuti: “N’nadzifunsa kuti, ‘Kodi tsopano tidzawapeza bwanji anthu olankhula ci Quechua?’” Kodi Kevin anacita bwanji? Iye anati: “N’nakumbukila lemba la Miyambo 3:5. Ndipo n’naganizila citsanzo ca Mose. Iye anafunika kutulutsa Aisiraeli mu Iguputo ndi kuwatsogolela ku Nyanja Yofiila kumene kunaoneka ngati kumalo kumene Aiguputo akanawapeza mosavuta. Ngakhale n’telo, iye anamvelabe, ndipo Yehova anamudalitsa m’njila yapadela cifukwa ca kumvela kwake.” (Eks. 14:​1, 2, 9-11, 21, 22) Kevin anali wokonzeka kusintha ndi kuyamba kugwilitsila nchito njila yatsopano ya kulalikila. Panakhala zotsatilapo zotani? Iye anakamba kuti: “N’nacita cidwi ndi mmene Yehova anatidalitsila. Kale, tinali kuyenda kwambili polalikila, ndipo tinali kupeza munthu mmodzi kapena awili cabe olankhula ci Quechua. Koma tsopano timangopita kukalalikila ku magawo kumene kuli anthu oculuka olankhula ci Quechua. Zotsatilapo zake zakhala zakuti timakambilana ndi anthu oculukilapo, tili ndi maulendo obwelelako oculuka, komanso maphunzilo a Baibulo. Ciwelengelo ca opezeka pa msonkhano cawonjezeka.” Inde, tikamayenda mwa cikhulupililo, Yehova amatidalitsa nthawi zonse.

Mwamuna wolankhula ci Quechua akukamba na banja limene lili mu ulaliki. Akuwalatila khomo la munthu winanso wolankhula ci Quechua.

Anthu ambili anali kuuza abale kumene angapeze anthu olankhula ci Quechua (Onani ndime 15-16)


17. Kodi mwaphunzilanji m’nkhani ino?

17 Takambilana zimene tingacite kuti tisaleke kuyenda mwa cikhulupililo m’mbali zitatu za umoyo wathu. Koma tiyenela kupitiliza kuyenda mwa cikhulupililo m’mbali zonse za umoyo wathu monga posankha zosangalatsa, popanga zisankho pa nkhani ya maphunzilo, kapena mmene tingalelele ana. Kaya tikupanga zisankho zotani, tisatsogoleledwe ndi zooneka ndi maso zokha. Tiyenelanso kutsogoleledwa ndi malangizo a Yehova, lonjezo lake lakuti adzatisamalila, komanso ubale wathu ndi iye. Tikatelo, tidzatha kuyenda “m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.”​—Mika 4:5.

TINGAYENDE BWANJI MWA CIKHULUPILILO . . .

  • posankha nchito?

  • posankha womanga naye banja?

  • gulu lathu likatipatsa malangizo?

NYIMBO 156 Mwa Cikhulupililo

a Maina ena asinthidwa.

b M’ndimeyi, taonetsa kuti mlongo ndiye akufuna mwamuna womanga naye banja. Komabe, malangizowa agwilanso nchito kwa m’bale amene akufuna mkazi.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani