LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 July masa. 2-7
  • N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kufunsila Ulangizi?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kufunsila Ulangizi?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KODI NDI KHALIDWE LITI LIMENE NDIYENELA KUKHALA NALO?
  • NDANI ANGANDIPATSE ULANGIZI WANZELU?
  • KODI NDINGAKHALE BWANJI WOKONZEKA KULANDILA UPANGILI?
  • KODI NDIYENELA KUPEMPHA ANTHU ENA KUMANDIPANGILA ZISANKHO?
  • MUSALEKE KUFUNSILA UPANGILI
  • Kupeleka Ulangizi Wabwino
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Zimene Tiphunzilapo pa Mawu Othela Omwe Amuna Okhulupilika Anakamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 July masa. 2-7

NKHANI YOPHUNZILA 28

NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu

N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kufunsila Ulangizi?

“Anthu amene amapempha malangizo amakhala ndi nzelu.”​—MIY. 13:10.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Zimene tiyenela kucita kuti tipindule mokwanila ndi ulangizi umene tingapatsidwe.

1. Kodi tingapange bwanji zisankho zanzelu kuti mapulani athu azikwanilitsika? (Miyambo 13:10; 15:22)

TONSEFE timafuna kupanga zisankho zanzelu. Timafunanso kuti mapulani athu akwanilitsike. Kuti zimenezi zitheke, Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kufunsila ulangizi.​—Welengani Miyambo 13:10; 15:22.

2. Kodi Yehova akutilonjeza kuticitila ciyani?

2 Mwacidziwikile, Munthu wabwino koposa amene tingafunsileko nzelu komanso ulangizi ndi Atate wathu Yehova. Iye akutilonjeza kuti: “Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anila.” (Sal. 32:8) Mawu amenewa akusonyeza kuti Yehova samangotipatsa upangili, koma amationetsanso cidwi aliyense payekhapayekha, ndipo amatithandiza kugwilitsa nchito uphungu wake.a

3. Tikambilana ciyani m’nkhani ino?

3 Mu nkhani ino, Mawu a Mulungu atithandiza kuyankha mafunso anayi awa: (1) Kodi ndi khalidwe liti limene ndiyenela kukhala nalo kuti ndipindule ndi ulangizi wanzelu? (2) Nanga ndani angandipatse upangili wanzelu? (3) Ndingacite ciyani poonetsa kuti ndine wokonzeka kulandila ulangizi? (4) N’cifukwa ciyani ndiyenela kupewa kupempha ena kuti azindipangila zisankho?

KODI NDI KHALIDWE LITI LIMENE NDIYENELA KUKHALA NALO?

4. Kodi tiyenela kukhala ndi khalidwe liti kuti tipindule ndi upangili wanzelu?

4 Tiyenela kukhala odzicepetsa kuti tipindule ndi ulangizi wanzelu. Tiyenela kudziwa kuti si nthawi zonse pamene tingakhale ndi cidziwitso cokwanila kuti tipange cisankho canzelu patokha. Conco ngati sindife odzicepetsa, Yehova sadzatithandiza, ndipo uphungu uliwonse umene tingawelenge m’Mawu ake udzangotelelapo pa ife ngati mmene madzi amacitila pa galasi. (Mika 6:8; 1 Pet. 5:5) Koma ngati ndife odzicepetsa, sitidzacedwa kulandila uphungu wa m’Baibo ndi kuugwilitsa nchito.

5. Kodi Davide anacita zinthu zotani zimene zikanam’pangitsa kukhala wodzikuza?

5 Onani zimene tingaphunzilepo pa citsanzo ca Mfumu Davide. Zimene anacita zikanam’pangitsa kukhala wonyada. Zaka zambili iye asanakhale mfumu, anachuka cifukwa ca luso loimba. Iye anafika ngakhale poimbila mfumu. (1 Sam. 16:​18, 19) Davide atadzozedwa kukhala mfumu, Yehova anam’patsa mzimu woyela umene unam’patsa mphamvu. (1 Sam. 16:​11-13) Anthu anali kum’tamanda cifukwa ca kupha adani awo, kuphatikizapo Goliyati, Mfilisiti amene anali ciphona. (1 Sam. 17:​37, 50; 18:7) Kwa munthu wodzikuza, zinthu ngati izi zikanam’pangitsa kuganiza kuti sayenela kumvetsela ulangizi wocokela kwa ena. Koma Davide anali wodzicepetsa.

6. Kodi tidziwa bwanji kuti Davide anali kulandila uphungu? (Onaninso pa cikuto.)

6 Davide atakhala mfumu, anasankha mabwenzi amene akanamupatsa uphungu. (1 Mbiri 27:​32-34) Izi n’zosadabwitsa cifukwa ngakhale asanakhale mfumu, Davide anali ndi cizolowezi comvetsela uphungu wanzelu. Sanali kulandila uphungu kwa amuna okha. Analandilanso uphungu wocokela kwa mayi wina dzina lake Abigayeli. Abigayeli anali mkazi wa Nabala, mwamuna amene anali wopanda ulemu, wosayamika, komanso wodzimva. Modzicepetsa, Davide anamvela uphungu wanzelu wa Abigayeli, ndipo izi zinam’thandiza kuti asacite colakwa cacikulu.​—1 Sam. 25:​2, 3, 21-25, 32-34.

Mfumu Davide akumvetsela mwachelu kwa Abigayeli, yemwe wakhala pansi kumucondelela.

Modzicepetsa, Mfumu Davide anamvela uphungu wa Abigayeli ndi kuugwilitsa nchito (Onani ndime 6)


7. Kodi titengapo maphunzilo anji pa citsanzo ca Davide? (Mlaliki 4:13) (Onaninso zithunzi.)

7 Pali zimene tingaphunzilepo pa citsanzo ca Davide. Mwacitsanzo, tingakhale ndi luso linalake kapena ulamulilo pa ena. Ngakhale n’telo, tisayese n’komwe kuganiza kuti tidziwa zonse kapena kuti sitikufunikila upangili. Monga anacitila Davide, ifenso tiyenela kukhala okonzeka kumvetsela ulangizi wanzelu mosasamala kanthu za amene akutipatsa ulangiziwo. (Welengani Mlaliki 4:13.) Tikatelo, tidzapewa kucita zolakwa zikuluzikulu zimene zingabweletse mavuto kwa ife kapena kwa ena.

Zithunzi: 1. Akulu anayi ali pa miting’i. Mmodzi wa akuluwo akulankhula mwaukali. 2. Pambuyo pake, mkulu wacinyamata amene analipo pa miting’iyo ali m’galimoto pamodzi ndi mkulu amene analankhula mwaukali, ndipo akulankhula naye ali kwaokha.

Tiyenela kukhala okonzeka kumvela ulangizi mosasamala kanthu kuti n’ndani waupeleka (Onani ndime 7)d


NDANI ANGANDIPATSE ULANGIZI WANZELU?

8. N’cifukwa ciyani Yonatani anali woyenela kupatsa Davide upangili?

8 Ganizilani phunzilo linanso limene tingatengepo pa citsanzo ca Davide. Iye anagwilitsa nchito ulangizi wa anthu amene anali pa ubale wabwino ndi Yehova, amenenso anali kumvetsa bwino vuto limene iye wakumana nalo. Mwacitsanzo, pamene anafuna kudziwa ngati angayanjanenso ndi Mfumu Sauli, Davide anamvetsela upangili wa Yonatani, mwana wa Sauli. N’cifukwa ciyani tingati Yonatani anali woyenela kupatsa Davide upangili? Cifukwa Yonatani anali pa ubale wabwino ndi Yehova, ndipo anali kudziwa bwino mocitila naye Sauli. (1 Sam. 20:​9-13) Kodi ifeyo tiphunzilapo ciyani?

9. Kodi tiyenela kufunsila kwa ndani tikafunika ulangizi? Fotokozani. (Miyambo 13:20)

9 Tikafunikila ulangizi, ndi bwino kufunsila kwa munthu amene ali pa ubale wabwino ndi Yehova, komanso amene akuidziwa bwino nkhani imene tikufunapo thandizo.b (Welengani Miyambo 13:20.) Mwacitsanzo, tinene kuti m’bale wacinyamata akufuna kupeza munthu woyenelela kudzamanga naye banja. Kodi ndani angam’patse ulangizi wabwino? N’zoona kuti mnzake amene sali pa banja angam’patse ulangizi wothandiza ngati ungazikike pa mfundo za m’Baibo. Koma m’bale wacinyamatayo angalandile ulangizi wothandiza koposa ngati angafunsile kwa okwatilana okhwima kuuzimu amenenso amamudziwa bwino, komanso amene akhala acimwemwe mu ukwati wawo kwa zaka ndithu.

10. Kodi tsopano tikambilana ciyani?

10 Takambilana za khalidwe lofunikila, komanso amene angatipatse upangili wabwino. Tsopano tiyeni tikambilane cifukwa cake tiyenela kukhala okonzeka kulandila upangili. Tionenso ngati kuli koyenela kumapempha ena kutipangila zisankho.

KODI NDINGAKHALE BWANJI WOKONZEKA KULANDILA UPANGILI?

11-12. (a) Kodi tiyenela kupewa kucita ciyani? (b) Kodi Mfumu Rehobowamu anacita ciyani pamene anafunika kupanga cisankho cofunika?

11 Nthawi zina, munthu angaoneke ngati akupempha ulangizi, koma m’ceniceni akungofuna kuti ena avomeleze cisankho cimene wacipanga kale. Munthu wotelo sakhala kuti akufunadi ulangizi wocokela kwa ena. Iye ayenela kutengapo phunzilo pa zimene zinacitikila Mfumu Rehobowamu.

12 Rehobowamu ndiye analowa m’malo Mfumu Solomo monga wolamulila wa dziko la Isiraeli. Pa nthawi imene Rehobowamu anayamba kulamulila, dzikolo linali lotukuka, koma anthu anaona kuti Mfumu Solomo anali kuwagwilitsa nchito yolemetsa. Conco, anthuwo anapita kwa Rehobowamu kukam’pempha kuti awapeputsileko goli. Rehobowamu anawauza kuti amupatse nthawi kuti aganizilepo pa nkhaniyo. Poyamba, iye anacita bwino mwa kufunsila upangili kwa amuna acikulile omwe anali kuthandiza Solomo. (1 Maf. 12:​2-7) Komabe iye anakana ulangizi umene amuna amenewo anam’patsa. N’cifukwa ciyani anacita zimenezi? Kodi n’kutheka kuti Rehobowamu anali atapanga kale cisankho, ndipo anali kungofuna ena omwe angagwilizane naye maganizo? Ngati n’telo, iye anawapezadi anthu amene anagwilizana naye maganizo. Anthuwo anali acinyamata anzake. (1 Maf. 12:​8-14) Rehobowamu anayankha anthu ake mogwilizana ndi ulangizi umene anzake anamuuza. Zotsatilapo zake, mtunduwo unagawikana, ndipo kuyambila nthawiyo, Mfumu Rehobowamu anakhala ndi mavuto motsatizanatsatizana.​—1 Maf. 12:​16-19.

13. Tingadziwe bwanji ngati ndife okonzeka kulandila upangili ndi kuugwilitsa nchito?

13 Tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Rehobowamu? Tikafunsila upangili, tizikhalanso okonzeka kuulandila ndi kuugwilitsa nchito. Tingadziwe bwanji ngati timacita zimenezi? Tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Ndikafunsila ulangizi, kodi nthawi yomweyo ndimaukana cifukwa ndauzidwa zimene sin’nali kufuna?’ Tiyeni tioneko citsanzo.

14. Kodi tiyenela kukumbukila ciyani tikapatsidwa uphungu? Fotokozani citsanzo. (Onaninso cithunzi.)

14 Tinene kuti m’bale wapeza nchito ya malipilo abwino. Koma asanalowe nchitoyo, iye akupempha nzelu kwa mkulu mu mpingo. M’baleyo akufotokozela mkuluyo kuti nchitoyo izimupangitsa kuti azikhala kutali ndi banja lake kwa nthawi yaitali. Mkuluyo akukumbutsa m’baleyo mfundo ya m’Baibo yakuti udindo wake waukulu ndi kusamalila zosowa zauzimu za banja lake. (Aef. 6:4; 1 Tim. 5:8) Ndiye tinene kuti m’baleyo sanagwilizane ndi mawu a mkuluyo. Conco akupita kukafunsilanso za nkhaniyo kwa abale ena mpaka atapeza m’bale amene akumuuza zimene iye akufuna kumva. Kodi m’baleyo akufunsiladi nzelu kapena anapanga kale cisankho, ndipo akungofuna winawake amene angagwilizane ndi zimene anasankha kale? Tiyenela kukumbukila kuti mtima wathu ndi wonyenga. (Yer. 17:9) Nthawi zina, uphungu umene sitingakonde kwenikweni kuulandila ndiye ungakhale wabwino koposa.

Mlongo akufunsila ulangizi kwa abale ndi alongo osiyanasiyana. Koma iye sakukhutila ndi mayankho amene aliyense wa iwo wamuuza. Conco akucokapo.

Kodi tikufunadi kufunsila ulangizi wanzelu kapena tingofuna winawake amene angagwilizane ndi cisankho cimene tapanga kale? (Onani ndime 14)e


KODI NDIYENELA KUPEMPHA ANTHU ENA KUMANDIPANGILA ZISANKHO?

15. Kodi tiyenela kupewa kucita ciyani? Ndipo cifukwa ciyani?

15 Aliyense wa ife ali ndi udindo wodzipangila yekha zisankho. (Agal. 6:​4, 5) Monga takambila kale, munthu wanzelu amafunsila ulangizi kucokela m’Mawu a Mulungu, komanso kwa Akhristu okhwima kuuzimu asanapange cisankho. Komabe tiyenela kukhala osamala kuti tisapemphe ena kutipangila cisankho. Ena angacite zimenezi mwacindunji pofunsa munthu amene amamulemekeza kuti, “Mukanakhala inu mukanacita bwanji?” Koma ena angacite zimenezi mwa njila yosakhala yacindunji, mwa kungotengela zimene munthu wina wacita popanda iwo kuganizilapo mozama pa nkhaniyo.

16. Kodi ku Korinto kunabuka nkhani yotani yokhudzana ndi nyama zopelekedwa nsembe ku mafano? Nanga ndani anali ndi udindo wosankha kudya nyamazo kapena kusadya? (1 Akorinto 8:7; 10:​25, 26)

16 Ganizilani nkhani imene inabuka mu mpingo wa ku Korinto wa m’zaka za zana loyamba. Nkhaniyo inali yokhudza kudya nyama zopelekedwa nsembe ku mafano. Ponena za nkhaniyo, Paulo anawalembela kuti: “Timadziwa kuti fano si kanthu ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.” (1 Akor. 8:4) Cifukwa ca mfundoyi, ena mu mpingo anaona kuti panalibe vuto kudya nyama zimene zinali kupezeka pa msika pambuyo pakuti zapelekedwa nsembe ku mafano. Koma ena anasankha kusadya nyama zaconco kuopela kuti zingavutitse cikumbumtima cawo. (Welengani 1 Akorinto 8:​7, 10:​25, 26.) Cimeneci cinali cisankho ca munthu mwini. Paulo sanalangize anthu a ku Korinto kuti azipangila ena zisankho kapena kutengela zocita za ena. Aliyense wa iwo anafunika ‘kuyankha yekha kwa Mulungu.’​—Aroma 14:​10-12.

17. Kodi cingacitike n’ciyani tikamangotengela ena popanga zisankho? Pelekani citsanzo. (Onaninso zithunzi.)

17 Kodi zofanana ndi zimenezi zingacitikenso masiku ano? Ganizilani za nkhani ya tuzigawo tung’onotung’ono twa magazi. Mkhristu aliyense ali ndi udindo wosankha kulandila tuzigawotu kapena kukana.c Ngakhale kuti nkhaniyi ingakhale yovuta kuimvetsa mofikapo, aliyense wa ife ayenelabe kudzipangila cisankho pa nkhani imeneyi. (Aroma 14:4) Ngati tingapange cisankho potengela zimene wina anasankha, tingafooketse cikumbumtima cathu. Tingaphunzitse cikumbumtima cathu kokha mwa kucigwilitsa nchito. (Aheb. 5:14) Conco, ndi pa nthawi iti pamene tingafunsile nzelu kwa Mkhristu wokhwima kuuzimu? Tingacite zimenezo pambuyo pakuti tafufuza pa ife eni, koma tikufunikilabe thandizo kuti timvetse mmene mfundo za m’Baibo zingagwilile nchito pa cisankho cimene tikufuna kupanga.

Zithunzi: 1. M’bale akugwilitsa nchito Baibo, phunzilo 39 m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, ndi vidiyo yakuti “Kupanga Cisankho pa Cithandizo ca Cipatala Cofuna Magazi,” kuti zimuthandize kudzadza khadi ya DPA. 2. Pambuyo pake, iye akumvetsela kwa m’bale wokhwima amene akukambilana naye lemba.

Tingafunsileko nzelu kwa ena kokha pambuyo pakuti ife eni tafufuza (Onani ndime 17)


MUSALEKE KUFUNSILA UPANGILI

18. Kodi Yehova waticitila zotani?

18 Yehova waonetsa kuti amatidalila kwambili potipatsa ufulu woti tizidzipangila zisankho. Iye anatipatsa Mawu ake Baibo. Ndipo anatipatsanso mabwenzi anzelu amene angatithandize kumvetsa bwino mmene tingasewezetsele mfundo za m’Baibo. Pocita zimenezi, iye waonetsa kuti ndi Tate wacikondi. (Miy. 3:​21-23) Tingacite ciyani poonetsa kuti timamuyamikila?

19. Tingacite ciyani kuti tipitilize kukondweletsa Yehova?

19 Makolo amakondwela kwambili kuona ana awo akukula ndi kukhala atumiki a Yehova oganiza bwino. Mofananamo, Yehova amakondwela kutiona tikupitiliza kukula kuuzimu, kufunsila ulangizi, komanso kupanga zisankho zimene zimamulemekeza.

KUTI NDIPINDULE NDI ULANGIZI WANZELU, N’CIFUKWA CIYANI NDIYENELA . . .

  • kukhala wodzicepetsa?

  • kukhala wokonzeka kulandila ulangizi?

  • kupanga ndekha zisankho?

NYIMBO 127 Mtundu wa Munthu Amene Niyenela Kukhala

a Nthawi zina m’Malemba, mawu akuti “uphungu” komanso akuti “nzelu” amatanthauza cinthu cimodzi. M’nkhani ino ndi yotsatila, mawuwa komanso mawu akuti “ulangizi” komanso “upangili” tidzawagwilitsa nchito mosinthanitsa.

b Nthawi zina, cingakhale canzelu kwa Akhristu kufunsilako kwa ena amene satumikila Yehova pa nkhani zokhudzana ndi ndalama, cithandizo ca mankhwala, komanso pa nkhani zina.

c Kuti mumvetse zowonjezeleka pa nkhaniyi, onani phunzilo 39 mfundo 5 ndi mbali yakuti “Fufuzani” m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mkulu akupatsa uphungu mkulu mnzake cifukwa ca mmene mkuluyo anakambila pa miting’i yaposacedwa.

e MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo akufunsila ulangizi kwa abale ndi alongo osiyanasiyana. Koma iye sakukhutila ndi mayankho amene aliyense wa iwo wamuuza. Conco akucokapo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani