NKHANI YOPHUNZILA 29
NYIMBO 87 Bwelani Mutsitsimulidwe!
Kupeleka Ulangizi Wabwino
“Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyangʼanila.”—SAL. 32:8.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Mmene tingapelekele ulangizi wothandiza.
1. Ndani ayenela kupatsa ena uphungu? Fotokozani.
MUKAGANIZILA zopatsa ena uphungu, kodi mumamva bwanji? Kwa ena, kucita zimenezi n’kosavuta. Koma ena amazengeleza kupeleka uphungu kapena ulangizi, ndipo cimakhala cowavuta kuupeleka. Mulimonsemo, aliyense wa ife ayenela kupeleka uphungu nthawi ndi nthawi. Cifukwa ciyani? Cifukwa Yesu anakamba kuti ophunzila oona amadziwika kaamba ka cikondi cimene amaonetsana wina ndi mnzake. (Yoh. 13:35) Njila imodzi imene timaonetsela kuti timakondana ndi kupeleka uphungu kwa abale ndi alongo athu pakafunikila kutelo. Mawu a Mulungu amati “mnzako wabwino” ndi uja amene amakupatsa “malangizo mosapita m’mbali.”—Miy. 27:9.
2. Kodi akulu ayenela kumacita ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani? (Onaninso mbali yakuti “Uphungu pa Msonkhano wa Mkati mwa Mlungu.”)
2 Akulu makamaka, ayenela kumapeleka ulangizi wofika pa mtima. Zili conco cifukwa Yehova kupitila mwa Yesu ndiye waika amuna amenewa kuti awete mpingo wake. (1 Pet. 5:2, 3) Njila imodzi imene amawetela mpingo ndi kupeleka uphungu wa m’Baibo akamakamba nkhani mu mpingo. Ayenelanso kupeleka uphungu kwa nkhosa iliyonse payokhapayokha, kuphatikizapo zija zimene zinapatuka pa nkhosa zinzake. Ndi motani mmene akulu, kuphatikizapo tonsefe, tingapelekele ulangizi wabwino?
3. (a) Tingakhale bwanji mlangizi wabwino? (Yesaya 9:6; onaninso danga lakuti “Tengelani Citsanzo ca Yesu Popeleka Ulangizi.”) (b) Tikambilana ciyani m’nkhani ino?
3 Tingaphunzile zambili za mmene tingakhalile mlangizi wabwino poona zitsanzo za anthu a m’Baibo, makamaka Yesu. Limodzi mwa maina ake audindo ndi lakuti “Mlangizi Wodabwitsa.” (Welengani Yesaya 9:6.) M’nkhani ino, tikambilana zimene tiyenela kucita tikapemphedwa kupeleka uphungu komanso pamene sitinapemphedwe. Tikambilananso kufunika kopeleka uphungu pa nthawi yoyenela komanso m’njila yoyenela.
TIKAPEMPHEDWA KUPELEKA ULANGIZI
4-5. Wina akafunsila nzelu kwa ife, tiyenela kudzifunsa funso liti? Pelekani citsanzo.
4 Wina akafunsila nzelu kwa ife, kodi tiyenela kutani? Mwina tingamve bwino ndipo tingafune kuthandiza nthawi yomweyo. Koma coyamba tidzifunse kuti, ‘Kodi ndine woyenelela kupeleka ulangizi pa nkhani imeneyi?’ Nthawi zina, njila yabwino kwambili si kupeleka ulangizi, koma kumuthandiza kupeza munthu amene amaidziwa bwino nkhaniyo kuti am’patse ulangizi.
5 Ganizilani citsanzo ici. Tiyelekeze kuti mnzanu wadwala kwambili. Wakuuzani kuti wayamba kale kufufuza njila za cithandizo ca mankhwala zimene zilipo. Kenako akukupemphani kuti mumuuze njila imene inu muona kuti ndiyo yabwino kwambili pa njilazo. N’kutheka mungakondepo njila imodzi, ngakhale kuti sindinu dokotala ndipo simunaphunzile mocitila ndi matendawo. Komabe, njila yabwino koposa ingakhale kumuthandiza mnzanuyo kuti apeze munthu woyenelela amene angamuthandize.
6. N’cifukwa ciyani tingacite bwino kuyembekeza tisanapeleke ulangizi?
6 Ngakhale pamene tikuona kuti ndife oyenelela kupeleka ulangizi winawake, tingacite bwino kuyembekeza pang’ono tisanamuyankhe. Cifukwa ciyani? Miyambo 15:28 imati ‘wolungama amayamba waganiza asanayankhe.’ Nanga bwanji ngati tiona kuti tingapeleke ulangizi wothandiza? Tingafunikilebe nthawi kuti tifufuze, tipemphele, komanso kuti tisinkhesinkhepo. Tikatelo tingakhale ndi cidalilo cakuti upangili wathu ndi wogwilizana ndi kaganizidwe ka Yehova pa nkhaniyo. Ganizilani citsanzo ca mneneli Natani.
7. Kodi muphunzilapo ciyani pa citsanzo ca mneneli Natani?
7 Mfumu Davide anauza mneneli Natani kuti anali kufuna kumangila Yehova kacisi. Natani anafulumila kuuza Davide kuti anali woyenela kumanga kacisi. Koma Natani akanacita bwino coyamba akanafunsila kwa Yehova. Cifukwa ciyani? Cifukwa Yehova sanasankhe Davide kuti amumangile kacisi. (1 Mbiri 17:1-4) Nkhaniyi itiphunzitsa kuti ena akafunsila ulangizi kwa ife, ndi bwino ‘kuganiza kaye tisanalankhule.’—Yak. 1:19.
8. Kodi n’cifukwa cina citi cimene tiyenela kukhalila osamala popatsa ena ulangizi?
8 Cifukwa cina cimene tiyenela kukhalila osamala popatsa ena ulangizi n’cakuti: Ifenso tingakhale olakwa ngati tingapatse munthu ulangizi umene ungamubweletsele mavuto. Conco m’pofunika kwambili kuti tiziganizilapo mozama tisanapatse wina ulangizi.
KUPELEKA UPHUNGU PAMENE SITINAPEMPHEDWE
9. Akulu asanapeleke uphungu, kodi ayenela kutsimikiza ciyani? (Agalatiya 6:1)
9 Nthawi ndi nthawi, akulu ayenela kupeleka uphungu kwa munthu amene wapatuka n’kuyamba kulowela “njila yolakwika.” (Welengani Agalatiya 6:1.) Munthuyo angakhale kuti akupanga zisankho zolakwika zimene pambuyo pake zingacititse kuti acite chimo lalikulu. Colinga ca akulu popeleka uphungu ndi kuthandiza munthuyo kukhalabe pa njila yotsogolela ku moyo wosatha. (Yak. 5:19, 20) Kuti uphungu wawo ukhale wothandiza, akulu coyamba ayenela kutsimikizila kuti munthuyo watengadi njila yolakwika. Yehova amalola tonsefe kupanga zisankho pogwilitsa nchito cikumbumtima cathu. (Aroma 14:1-4) Nanga bwanji ngati m’bale watengadi njila yolakwika ndipo akulu aona kuti m’poyeneladi kumupatsa uphungu?
10-12. Popeleka uphungu umene sanawapemphe, kodi akulu ayenela kucita ciyani? Pelekani citsanzo. (Onaninso zithunzi.)
10 Si copepuka kwa akulu kupeleka uphungu kwa munthu amene sanawapemphe. N’cifukwa ciyani? Mtumwi Paulo anakamba kuti munthu angatenge njila yolakwika popanda kuzindikila. Conco, akulu asanapatse munthuyo ulangizi, pali zinthu zina zimene ayenela kucita zimene zingathandize munthuyo kuti aulandile mosavuta uphungu wawo.
11 Kupeleka uphungu umene sitinapemphedwe tingakufananitse ndi zimene mlimi amacita akafuna kubyala mbewu pa nthaka youma. Asanabyale, amakonzekeletsa nthaka, kenako amabyala mbewu, ndipo amathilila kuti mbewuzo zikule. Mofananamo, mkulu asanapeleke ulangizi kwa m’bale, afunika kucita zinthu zina zimene zingapangitse m’baleyo kumvetsela mosavuta ulangizi wake, komwe kuli ngati kukonzekeletsa nthaka. Mwacitsanzo, mkuluyo amayembekezela nthawi yoyenela ndipo amauza m’baleyo kuti amasamala kwambili za iye, ndi kuti pali zina zimene afuna kukambilana naye. Ngati phunguyo amadziwika kuti ndi wacikondi komanso wokoma mtima, cidzakhala cosavuta kwa ena kumvetsela uphungu wake.
12 Pokambilana, mkuluyo angathandize m’baleyo kupitiliza kumvetsela uphungu wake mwa kumuuza kuti aliyense amalakwitsa ndipo tonsefe timafunikila uphungu. Kucita izi, kuli ngati kufewetsa nthaka. (Aroma 3:23) Ndi mawu ofatsa komanso aulemu kwambili, mkuluyo angaonetse m’baleyo kucokela m’Malemba kuti anatenga njila yolakwika. M’baleyo akamvetsa kuti analoweladi njila yolakwika, mkuluyo angamufotokozele m’mawu osavuta pomuonetsa zimene ayenela kucita kuti akonze zolakwikazo. Kucita izi kungakhale ngati akubyala mbewu tsopano. Cothela, mkuluyo angayamikile m’baleyo mocokela pansi pa mtima ndi kupemphela naye. Kucita izi kungakhale ngati akuthilila mbewuyo tsopano.—Yak. 5:15.
Popeleka uphungu umene sanapemphedwe, akulu amaonetsa cikondi ndipo amacita zimenezo mosamala (Onani ndime 10-12)
13. Kodi akulu angatsimikize bwanji ngati munthu wamvetsa uphungu umene wapatsidwa?
13 Nthawi zina, zimacitika kuti zimene phungu wakamba n’zosiyana ndi zimene wolandila uphunguwo wamva. Kodi akulu angatani kuti zimenezi zisacitike? Iwo angathandize munthuyo kumvetsa mfundo zimene akukambilana mwa kumufunsa mafunso aluso komanso mwaulemu. (Mlal. 12:11) Mayankho a munthuyo adzathandiza phunguyo kuona ngati munthuyo wamvetsa uphungu umene wapatsidwa.
KUPELEKA ULANGIZI PA NTHAWI YOYENELA KOMANSO M’NJILA YOYENELA
14. Kodi tiyenela kupeleka ulangizi pamene tili okwiya? Fotokozani.
14 Tonsefe ndife opanda ungwilo. Conco, nthawi zina tingakambe kapena kucita zinthu zimene zingakhumudwitse ena. (Akol. 3:13) Mawu a Mulungu amaonetsa kuti ena angatikwiyitse. (Aef. 4:26) Koma tiyenela kudziletsa kuti tisapeleke uphungu pamene tili okwiya. Cifukwa ciyani? “Cifukwa munthu amene wakwiya sacita zinthu mogwilizana ndi cilungamo ca Mulungu.” (Yak. 1:20) Kupeleka uphungu tili okwiya, kungacititse kuti zinthu ziipileko. Koma mfundoyi siikutiletsa kufotokoza maganizo athu kapena mmene tinamvela kwa munthu amene anatikhumudwitsa. Komabe, tiyenela kuyembekezela mpaka mtima wathu utakhala pansi tisanalankhule ndi munthuyo. Tiyeni tione mmene Elihu anapelekela ulangizi wabwino kwa Yobu.
15. Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Elihu? (Onaninso cithunzi.)
15 Elihu anakhala masiku angapo akumvetsela pomwe Yobu anali kudziikila kumbuyo pamene anzake atatu abodza anali kumuneneza. Iye anamumvela cifundo Yobu. Komabe, Elihu anakwiyila kwambili Yobu cifukwa sananene zoona zokhudza Yehova ndipo anaika kwambili maganizo pa iyemwini. Ngakhale n’telo, Elihu anayembekezela nthawi yabwino kuti alankhule ndipo iye analankhula mofatsa komanso mwaulemu kwambili popeleka ulangizi kwa Yobu. (Yobu 32:2; 33:1-7) Citsanzo ca Elihu citiphunzitsa mfundo yofunika iyi: Ulangizi umakhala wabwino kwambili ukapelekedwa pa nthawi yoyenela komanso m’njila yoyenela. Ndipo uyenela kupelekedwa mwacikondi komanso mwaulemu kwambili.—Mlal. 3:1, 7.
Ngakhale kuti poyamba Elihu anakwiya kwambili, iye anapeleka uphungu mofatsa komanso mwaulemu kwambili (Onani ndime 15)
PITILIZANI KUPELEKA ULANGIZI KOMANSO KUULANDILA
16. Kodi muphunzilapo ciyani pa Salimo 32:8?
16 Lemba limene latsogolela nkhani ino limati ‘Yehova amatipatsa malangizo ndi kutiyang’anila.’ (Welengani Salimo 32:8.) Mfundoyi ionetsa kuti Yehova sadzaleka kutithandiza. Iye samangotipatsa upangili koma amatithandizanso kuugwilitsa nchito. Tiyenela kutengela citsanzo ca Yehova pa nkhaniyi. Tikafunikila kupatsa ena ulangizi, tingacite bwino kutengela citsanzo ca Yehova mwa kupitiliza kuwalimbikitsa ndi kuwathandiza kuti apange zisankho zanzelu.
17. Akulu akapeleka uphungu wosapita m’mbali komanso wozikika m’Baibo, kodi amaonetsa ciyani? Fotokozani. (Yesaya 32:1, 2)
17 Kuposa n’kale lonse, tiyenela kupeleka ulangizi wabwino komanso kuulandila. (2 Tim. 3:1) Akulu amene amapeleka ulangizi wosapita m’mbali wozikika m’Baibo ali “ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi.” (Welengani Yesaya 32:1, 2.) Mabwenzi amene amadziwa zimene tikufuna kumva tikafunsila ulangizi kwa iwo, koma n’kutiuza zimene tikufunikiladi kumva, amatipatsa mphatso yamtengo wapatali ngati “zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” (Miy. 25:11) Conco, tiyeni tonsefe tipitilize kukulitsa nzelu imene ingatithandize kupeleka uphungu wabwino komanso kuulandila.
NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse