Mary_Ukraine/stock.adobe.com
KHALANIBE MASO!
Anthu Ambili Aleka Kukhulupilila Atsogoleli a Ndale—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Kuposa caka cina cilisonse, caka cino ca 2024 m’maiko ambili mucitika masankho. Komabe, anthu ambili aleka kuwakhulupilila atsogoleli a ndale.
Pa kafukufuku wina umene unacitika, anthu ambili ku America anakamba kuti “atsogoleli ambili a ndale ali na zolinga za dyela,” osati kuthandiza anthu amene amawalamulila.a—Linatelo bungwe la akatswili lochedwa Pew Research Center, pa September 19, 2023.
Acinyamata ambili nawonso sawakhulupilila atsogoleli a ndale.
“Nthawi zambili acinyamata amaona kuti kupeza njila yothetsela mavuto n’kofunika kwambili. Koma amakamba kuti atsogoleli a ndale alephela kupeza njila yothetsela mavuto.”—Inatelo nyuzipepala ya The New York Times, pa January 29, 2024.
“Pa kafukufuku wina anapeza kuti acinyamata ambili amadalila kwambili anthu amene amaika mavidiyo pa intaneti kapena anthu ochuka a pa soshomidiya kuposa atsogoleli a ndale.”—Inatelo nyuzipepala ya The Korea Times, pa January 22, 2024.
Kodi tingakhale na cidalilo cakuti atsogoleli a ndale adzathetsa mavuto kutsogolo? Nanga n’ndani amene tingamudalile?
Musamangokhulupilila aliyense
Anthu amene amapewa kukhulupilila aliyense amacita bwino. Baibo imanena kuti “munthu amene sadziwa zambili amakhulupilila mawu alionse. Koma wocenjela amaganizila zotsatila za zimene akufuna kucita.”—Miyambo 14:15.
Kuti mupeze mfundo zimene zingakuthandizeni kudziŵa ngati zimene mwamva n’zoona kapena ayi, ŵelengani nkhani yakuti “Samalani Kuti Musamapusitsike Ndi Nkhani Zabodza.”
Kuwonjezela apo, ngakhale atsogoleli a ndale oona mtima komanso a zolinga zabwino, sangakwanitse kucita zonse zimene amafuna. Ndiye cifukwa cake Baibo imaticenjeza kuti:
“Musamadalile mafumu, anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.”—Salimo 146:3, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero.
Mtsogoleli amene mungam’khulupilile
Baibo imanena kuti Mulungu anasankha Yesu Khristu amene ni mtsogoleli wamphamvu ndiponso wokhulupilika kwambili. (Luka 1:32, 33) Yesu ni mfumu ya Ufumu wa Mulungu womwe ni boma la kumwamba limene likulamulila.—Mateyu 6:10.
Onani cifukwa cake mungamukhulupilile Yesu. Onaninso zimene adzacita kuti adzathetse mavuto amene timakumana nawo. Ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu Ndani?” komanso yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzacita Zotani?”
a Pew Research Center, “Americans’ Dismal Views of the Nation’s Politics,” September 2023.