Comstock Images/Stockbyte via Getty Images
Andale a Katangale—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzacitapo Ciyani?
Anthu amafuna atsogoleli a boma amene angawadalile, cifukwa atopa nawo atsogoleli a boma a katangale na ziphuphu. Kafukufuku amene anatuluka mu 2023, anaonetsa kuti ngati pali atsogoleli omwe anthu ambili sawakhulupilila m’pang’ono pomwe ni atsogoleli a boma.a
Koma Baibo imakamba za boma limene Mtsogoleli wake ni wodalilika kwenikweni komanso woona mtima, wosacita zakatangale ngakhale pang’ono pokha. Bomalo ni Ufumu wa Mulungu, ndipo Mtsogoleli wake ni Yesu Khristu.—Yesaya 9:7.
Mwa zocita zake, Yesu anaonetsa kuti amawadela nkhawa anthu. (Mateyu 9:35, 36) Monga Wolamulila mu Ufumu wa Mulungu, iye adzabweletsa cilungamo na mtendele kwa anthu onse omumvela.—Salimo 72:12-14.
a 2023 Edelman Trust Barometer Global Report.