Sondo, October 12
[Yehova] adzakupatsani mphamvu, adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupilika komanso adzakulimbitsani.—1 Pet. 5:10.
Nthawi zambili Mawu a Mulungu amachula anthu okhulupilika kuti ni amphamvu. Koma ngakhale aja amene anali amphamvu kwambili si nthawi zonse pamene anali kudzimva telo. Nthawi zina Mfumu Davide anali kudzimva “wamphamvu ngati phili,” koma nthawi zina anali kudzimva wofooka ndipo anali “kucita mantha.” (Sal. 30:7) Ngakhale kuti Samisoni anali na mphamvu zapadela pamene mzimu wa Mulungu unali kugwila nchito pa iye, iye anazindikila kuti popanda mphamvu zocokela kwa Mulungu ‘angafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.’ (Ower. 14:5, 6; 16:17) Amuna okhulupilika amenewa anali olimba cifukwa Yehova ndiye anawapatsa mphamvu. Mtumwi Paulo anadziŵa kuti nayenso anafunikila mphamvu zocokela kwa Yehova. (2 Akor. 12:9, 10) Monga ambili a ife, mtumwi Paulo nayenso anali kulimbana na mavuto a thanzi. (Agal. 4:13, 14) Nthawi zina, zinalinso zovuta kuti acite coyenela. (Aroma 7:18, 19) Analinso kukhala na nkhawa pa zimene zidzamucitikila. (2 Akor. 1:8, 9) Komabe, pamene anali wofooka, m’pamene anali kukhala wamphamvu. Motani? Cifukwa Yehova anam’patsa mphamvu zimene anali kufunikila kuti apilile mavuto ake. w23.10 12 ¶1-2
Mande, October 13
Yehova amaona mumtima.—1 Sam. 16:7.
Ngati nafenso nthawi zina timavutika na maganizo odziona wacabe-cabe, tizikumbukila kuti Yehova anatikokela kwa iye mwa kufuna kwake. (Yoh. 6:44) Amaona zabwino mwa ife, zimene ife sitingaone. Ndipo amaudziŵa bwino mtima wathu. (2 Mbiri 6:30) Conco tiyenela kukhulupilila akatiuza kuti ndife a mtengo wapatali. (1 Yoh. 3:19, 20) Ena a ife tisanaphunzile coonadi, tinacitapo zinthu zimene ngakhale pali pano timadziimba nazo mlandu. (1 Pet. 4:3) Ngakhale Akhristu okhulupilika amalimbanabe na zifooko. Kodi mtima wanu umakuimbani mlandu? Ngati n’telo, pezani cilimbikitso podziŵa kuti atumiki okhulupilika a Yehova amakumananso na vuto limeneli. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anadziona wolephela atakumbukila zophophonya zake. (Aroma 7:24) N’zoona kuti iye anali atalapa macimo ake na kubatizika. Ngakhale n’telo, ponena za iye mwini, anati anali “wamng’ono kwambili pa atumwi onse,” komanso kuti anali “wocimwa kwambili.”—1 Akor. 15:9; 1 Tim. 1:15. w24.03 27 ¶5-6
Ciŵili, October 14
Iwo anasiya nyumba ya Yehova.—2 Mbiri 24:18.
Phunzilo limodzi limene tingatengepo pa cisankho coipa ca Mfumu Yehoasi n’lakuti tiyenela kusankha mabwenzi amene amakonda Yehova, komanso amene amafuna kumukondweletsa. Mabwenzi aconco angatithandize kucita zinthu mwanzelu. Sitiyenela kusankha anthu a msinkhu wathu okha-okha kukhala mabwenzi athu. Kumbukilani kuti Yehoasi anali wamng’ono kwambili poyelekezela na mnzake Yehoyada. Ponena za mabwenzi anu, dzifunseni kuti: ‘Kodi amanithandiza kulimbikitsa cikhulupililo canga mwa Yehova? Kodi amanilimbikitsa kutsatila miyeso ya Yehova? Kodi amakonda kukamba za Yehova na coonadi cake ca mtengo wapatali? Kodi amalemekeza miyeso ya Mulungu? Kodi amangoniuza zonikomela m’khutu, kapena amalimba mtima na kuniwongolela nikalakwitsa?’ (Miy. 27:5, 6, 17) Kunena zoona, ngati mabwenzi anu sakonda Yehova, pezani ena. Koma ngati amakonda Yehova, akangamileni—cifukwa adzakuthandizani ngako!—Miy. 13:20. w23.09 9-10 ¶6-7