Mande, October 13
Yehova amaona mumtima.—1 Sam. 16:7.
Ngati nafenso nthawi zina timavutika na maganizo odziona wacabe-cabe, tizikumbukila kuti Yehova anatikokela kwa iye mwa kufuna kwake. (Yoh. 6:44) Amaona zabwino mwa ife, zimene ife sitingaone. Ndipo amaudziŵa bwino mtima wathu. (2 Mbiri 6:30) Conco tiyenela kukhulupilila akatiuza kuti ndife a mtengo wapatali. (1 Yoh. 3:19, 20) Ena a ife tisanaphunzile coonadi, tinacitapo zinthu zimene ngakhale pali pano timadziimba nazo mlandu. (1 Pet. 4:3) Ngakhale Akhristu okhulupilika amalimbanabe na zifooko. Kodi mtima wanu umakuimbani mlandu? Ngati n’telo, pezani cilimbikitso podziŵa kuti atumiki okhulupilika a Yehova amakumananso na vuto limeneli. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anadziona wolephela atakumbukila zophophonya zake. (Aroma 7:24) N’zoona kuti iye anali atalapa macimo ake na kubatizika. Ngakhale n’telo, ponena za iye mwini, anati anali “wamng’ono kwambili pa atumwi onse,” komanso kuti anali “wocimwa kwambili.”—1 Akor. 15:9; 1 Tim. 1:15. w24.03 27 ¶5-6
Ciŵili, October 14
Iwo anasiya nyumba ya Yehova.—2 Mbiri 24:18.
Phunzilo limodzi limene tingatengepo pa cisankho coipa ca Mfumu Yehoasi n’lakuti tiyenela kusankha mabwenzi amene amakonda Yehova, komanso amene amafuna kumukondweletsa. Mabwenzi aconco angatithandize kucita zinthu mwanzelu. Sitiyenela kusankha anthu a msinkhu wathu okha-okha kukhala mabwenzi athu. Kumbukilani kuti Yehoasi anali wamng’ono kwambili poyelekezela na mnzake Yehoyada. Ponena za mabwenzi anu, dzifunseni kuti: ‘Kodi amanithandiza kulimbikitsa cikhulupililo canga mwa Yehova? Kodi amanilimbikitsa kutsatila miyeso ya Yehova? Kodi amakonda kukamba za Yehova na coonadi cake ca mtengo wapatali? Kodi amalemekeza miyeso ya Mulungu? Kodi amangoniuza zonikomela m’khutu, kapena amalimba mtima na kuniwongolela nikalakwitsa?’ (Miy. 27:5, 6, 17) Kunena zoona, ngati mabwenzi anu sakonda Yehova, pezani ena. Koma ngati amakonda Yehova, akangamileni—cifukwa adzakuthandizani ngako!—Miy. 13:20. w23.09 9-10 ¶6-7
Citatu, October 15
Ine ndine Alefa ndi Omega.—Chiv. 1:8
Cilembo ca Alefa n’coyamba mu alifabeti ya Cigiriki, pamene cilembo ca Omega n’cothela. Podzifotokoza kuti iye ni “Alefa komanso Omega,” Yehova akumveketsa mfundo yakuti akayamba kucita cinacake amapitilizabe mpaka atacimalizitsa. Yehova atalenga Adamu na Hava, anawauza kuti: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile.” (Gen. 1:28) Pa nthawi imeneyo, zinali ngati Yehova akunena kuti “Alefa.” Anafotokoza colinga cake momveka bwino. Nthawi inali kudzafika pamene ana angwilo komanso omvela a Adamu na Hava anali kudzadzaza dziko lapansi na kulisandutsa kukhala Paradaiso. Pa nthawi yam’tsogolo imeneyo, tinganene kuti Yehova adzati “Omega.” Atamaliza kulenga “kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse za mmenemo,” Yehova anapeleka citsimikizo. Yehova anatsimikizila kuti adzakwanilitsa colinga cake kwa mtundu wa anthu komanso dziko lapansi. Colinga cake cinali kudzakwanilitsidwa kumapeto kwa tsiku la 7.—Gen. 2:1-3. w23.11 5 ¶13-14