LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso vitundu vina: Betsimisaraka (Northern), Betsimisaraka (Southern), Konkomba, Matses, Mi'kmaq
  • Lelo

Ciŵili, October 14

Iwo anasiya nyumba ya Yehova.​—2 Mbiri 24:18.

Phunzilo limodzi limene tingatengepo pa cisankho coipa ca Mfumu Yehoasi n’lakuti tiyenela kusankha mabwenzi amene amakonda Yehova, komanso amene amafuna kumukondweletsa. Mabwenzi aconco angatithandize kucita zinthu mwanzelu. Sitiyenela kusankha anthu a msinkhu wathu okha-okha kukhala mabwenzi athu. Kumbukilani kuti Yehoasi anali wamng’ono kwambili poyelekezela na mnzake Yehoyada. Ponena za mabwenzi anu, dzifunseni kuti: ‘Kodi amanithandiza kulimbikitsa cikhulupililo canga mwa Yehova? Kodi amanilimbikitsa kutsatila miyeso ya Yehova? Kodi amakonda kukamba za Yehova na coonadi cake ca mtengo wapatali? Kodi amalemekeza miyeso ya Mulungu? Kodi amangoniuza zonikomela m’khutu, kapena amalimba mtima na kuniwongolela nikalakwitsa?’ (Miy. 27:5, 6, 17) Kunena zoona, ngati mabwenzi anu sakonda Yehova, pezani ena. Koma ngati amakonda Yehova, akangamileni​—cifukwa adzakuthandizani ngako!​—Miy. 13:20. w23.09 9-10 ¶6-7

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Citatu, October 15

Ine ndine Alefa ndi Omega.​—Chiv. 1:8

Cilembo ca Alefa n’coyamba mu alifabeti ya Cigiriki, pamene cilembo ca Omega n’cothela. Podzifotokoza kuti iye ni “Alefa komanso Omega,” Yehova akumveketsa mfundo yakuti akayamba kucita cinacake amapitilizabe mpaka atacimalizitsa. Yehova atalenga Adamu na Hava, anawauza kuti: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile.” (Gen. 1:28) Pa nthawi imeneyo, zinali ngati Yehova akunena kuti “Alefa.” Anafotokoza colinga cake momveka bwino. Nthawi inali kudzafika pamene ana angwilo komanso omvela a Adamu na Hava anali kudzadzaza dziko lapansi na kulisandutsa kukhala Paradaiso. Pa nthawi yam’tsogolo imeneyo, tinganene kuti Yehova adzati “Omega.” Atamaliza kulenga “kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse za mmenemo,” Yehova anapeleka citsimikizo. Yehova anatsimikizila kuti adzakwanilitsa colinga cake kwa mtundu wa anthu komanso dziko lapansi. Colinga cake cinali kudzakwanilitsidwa kumapeto kwa tsiku la 7.​—Gen. 2:1-3. w23.11 5 ¶13-14

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cinayi, October 16

Konzani njila ya Yehova! Mulungu wathu mukonzeleni msewu wowongoka wodutsa mʼcipululu.​—Yes. 40:3.

Ulendo wocoka ku Babulo kupita ku Isiraeli unali kutenga miyezi inayi. Ulendowo unali na zovuta zake, koma Yehova analonjeza kuti adzacotsa zovutazo zimene zikanawalepheletsa kubwelela kwawo. Ayuda okhulupilika anadziŵa kuti akabwelela ku Isiraeli, adzapeza madalitso oculuka kuposa zimene angasiye ku Babulo. Dalitso lalikulu kwambili linali lokhudza kulambila kwawo. Kunalibe kacisi wa Yehova ku Babulo. Kunalibenso guwa la nsembe limene Aisiraeli akanapelekelapo nsembe malinga na Cilamulo ca Mose. Komanso kunalibe ansembe olinganizidwa owathandiza kupeleka nsembezo. Kuwonjezela apo, anthu a Yehova anali kukhala pakati pa anthu ambili amene sanali kulemekeza Yehova kapena miyeso yake. Conco, Ayuda masauzande amene anali kuopa Yehova, anali kuyembekezela mwacidwi kubwelela ku dziko lawo kuti akabwezeletse kulambila koyela. w23.05 14-15 ¶3-4

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani