Citatu, October 15
Ine ndine Alefa ndi Omega.—Chiv. 1:8
Cilembo ca Alefa n’coyamba mu alifabeti ya Cigiriki, pamene cilembo ca Omega n’cothela. Podzifotokoza kuti iye ni “Alefa komanso Omega,” Yehova akumveketsa mfundo yakuti akayamba kucita cinacake amapitilizabe mpaka atacimalizitsa. Yehova atalenga Adamu na Hava, anawauza kuti: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile.” (Gen. 1:28) Pa nthawi imeneyo, zinali ngati Yehova akunena kuti “Alefa.” Anafotokoza colinga cake momveka bwino. Nthawi inali kudzafika pamene ana angwilo komanso omvela a Adamu na Hava anali kudzadzaza dziko lapansi na kulisandutsa kukhala Paradaiso. Pa nthawi yam’tsogolo imeneyo, tinganene kuti Yehova adzati “Omega.” Atamaliza kulenga “kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse za mmenemo,” Yehova anapeleka citsimikizo. Yehova anatsimikizila kuti adzakwanilitsa colinga cake kwa mtundu wa anthu komanso dziko lapansi. Colinga cake cinali kudzakwanilitsidwa kumapeto kwa tsiku la 7.—Gen. 2:1-3. w23.11 5 ¶13-14
Cinayi, October 16
Konzani njila ya Yehova! Mulungu wathu mukonzeleni msewu wowongoka wodutsa mʼcipululu.—Yes. 40:3.
Ulendo wocoka ku Babulo kupita ku Isiraeli unali kutenga miyezi inayi. Ulendowo unali na zovuta zake, koma Yehova analonjeza kuti adzacotsa zovutazo zimene zikanawalepheletsa kubwelela kwawo. Ayuda okhulupilika anadziŵa kuti akabwelela ku Isiraeli, adzapeza madalitso oculuka kuposa zimene angasiye ku Babulo. Dalitso lalikulu kwambili linali lokhudza kulambila kwawo. Kunalibe kacisi wa Yehova ku Babulo. Kunalibenso guwa la nsembe limene Aisiraeli akanapelekelapo nsembe malinga na Cilamulo ca Mose. Komanso kunalibe ansembe olinganizidwa owathandiza kupeleka nsembezo. Kuwonjezela apo, anthu a Yehova anali kukhala pakati pa anthu ambili amene sanali kulemekeza Yehova kapena miyeso yake. Conco, Ayuda masauzande amene anali kuopa Yehova, anali kuyembekezela mwacidwi kubwelela ku dziko lawo kuti akabwezeletse kulambila koyela. w23.05 14-15 ¶3-4
Cisanu, October 17
Pitilizani kuyenda ngati ana a kuwala.—Aef. 5:8.
Timafunikila thandizo la mzimu wa Mulungu kuti tipitilize kucita zinthu “ngati ana a kuwala.” Cifukwa ciyani? Cifukwa si copepuka kukhalabe woyela m’dziko lino lodzala na makhalidwe oipa. (1 Ates. 4:3-5, 7, 8) Mzimu woyela ungatithandize kugonjetsa maganizo a m’dzikoli amene amasemphana na kaganizidwe ka Mulungu. Mzimuwo ungatithandizenso kubala cipatso “ciliconse cabwino ndi ciliconse colungama.” (Aef. 5:9) Njila imodzi imene tingalandile mzimu woyela ni kuupempha. Yesu ananena kuti Yehova “adzapeleka mowolowa manja mzimu woyela kwa amene akumupempha.” (Luka 11:13) Timalandilanso mzimu woyela tikamatamanda Yehova capamodzi pa misonkhano yathu. (Aef. 5:19, 20) Cisonkhezelo cabwino cimene mzimu woyela umakhala naco pa ife cimatithandiza kukhala na umoyo wokondweletsa Mulungu. w24.03 23-24 ¶13-15