LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso vitundu vina: Betsimisaraka (Northern), Betsimisaraka (Southern), Konkomba, Matses, Mi'kmaq
  • Lelo

Cinayi, October 16

Konzani njila ya Yehova! Mulungu wathu mukonzeleni msewu wowongoka wodutsa mʼcipululu.​—Yes. 40:3.

Ulendo wocoka ku Babulo kupita ku Isiraeli unali kutenga miyezi inayi. Ulendowo unali na zovuta zake, koma Yehova analonjeza kuti adzacotsa zovutazo zimene zikanawalepheletsa kubwelela kwawo. Ayuda okhulupilika anadziŵa kuti akabwelela ku Isiraeli, adzapeza madalitso oculuka kuposa zimene angasiye ku Babulo. Dalitso lalikulu kwambili linali lokhudza kulambila kwawo. Kunalibe kacisi wa Yehova ku Babulo. Kunalibenso guwa la nsembe limene Aisiraeli akanapelekelapo nsembe malinga na Cilamulo ca Mose. Komanso kunalibe ansembe olinganizidwa owathandiza kupeleka nsembezo. Kuwonjezela apo, anthu a Yehova anali kukhala pakati pa anthu ambili amene sanali kulemekeza Yehova kapena miyeso yake. Conco, Ayuda masauzande amene anali kuopa Yehova, anali kuyembekezela mwacidwi kubwelela ku dziko lawo kuti akabwezeletse kulambila koyela. w23.05 14-15 ¶3-4

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cisanu, October 17

Pitilizani kuyenda ngati ana a kuwala.​—Aef. 5:8.

Timafunikila thandizo la mzimu wa Mulungu kuti tipitilize kucita zinthu “ngati ana a kuwala.” Cifukwa ciyani? Cifukwa si copepuka kukhalabe woyela m’dziko lino lodzala na makhalidwe oipa. (1 Ates. 4:3-5, 7, 8) Mzimu woyela ungatithandize kugonjetsa maganizo a m’dzikoli amene amasemphana na kaganizidwe ka Mulungu. Mzimuwo ungatithandizenso kubala cipatso “ciliconse cabwino ndi ciliconse colungama.” (Aef. 5:9) Njila imodzi imene tingalandile mzimu woyela ni kuupempha. Yesu ananena kuti Yehova “adzapeleka mowolowa manja mzimu woyela kwa amene akumupempha.” (Luka 11:13) Timalandilanso mzimu woyela tikamatamanda Yehova capamodzi pa misonkhano yathu. (Aef. 5:19, 20) Cisonkhezelo cabwino cimene mzimu woyela umakhala naco pa ife cimatithandiza kukhala na umoyo wokondweletsa Mulungu. w24.03 23-24 ¶13-15

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵelu, October 18

Pitilizani kupempha ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitilizani kugogoda ndipo adzakutsegulilani.​—Luka 11:9.

Kodi mufunika kukulitsa kuleza mtima? Ngati n’telo, ipempheleleni nkhaniyo. Kuleza mtima ni cipatso cimene mzimu woyela umabala. (Agal. 5:22, 23) Conco, tiyenela kupempha mzimu woyela wa Yehova kuti utithandize kukulitsa cipatso cimeneci. Kuleza mtima kwathu kukakhala pa mayeso, ‘tidzapemphabe’ mzimu woyela kuti utithandize kukhala oleza mtima. (Luka 11:13) Tingapemphenso Yehova kuti atithandize kuona zinthu mmene iye amazionela. Pambuyo popemphela, tiyenela kuyesetsa kukhala oleza mtima tsiku lililonse. Tikamapemphela kwambili kuti tikhale oleza mtima, na kuyesetsa kukhala otelo, khalidweli lidzazika mizu mumtima mwathu. Ndipo lidzakhala umunthu wathu. Zingakhalenso zothandiza kusinkhasinkha zitsanzo za m’Baibo. M’Baibo muli zitsanzo zambili za anthu amene anali oleza mtima. Tikamasinkhasinkha zitsanzo zimenezo, tidzaphunzila mmene tingaonetsele kuleza mtima. w23.08 22 ¶10-11

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani