LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso vitundu vina: Betsimisaraka (Northern), Betsimisaraka (Southern), Konkomba, Matses, Mi'kmaq
  • Lelo

Ciŵelu, October 18

Pitilizani kupempha ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitilizani kugogoda ndipo adzakutsegulilani.​—Luka 11:9.

Kodi mufunika kukulitsa kuleza mtima? Ngati n’telo, ipempheleleni nkhaniyo. Kuleza mtima ni cipatso cimene mzimu woyela umabala. (Agal. 5:22, 23) Conco, tiyenela kupempha mzimu woyela wa Yehova kuti utithandize kukulitsa cipatso cimeneci. Kuleza mtima kwathu kukakhala pa mayeso, ‘tidzapemphabe’ mzimu woyela kuti utithandize kukhala oleza mtima. (Luka 11:13) Tingapemphenso Yehova kuti atithandize kuona zinthu mmene iye amazionela. Pambuyo popemphela, tiyenela kuyesetsa kukhala oleza mtima tsiku lililonse. Tikamapemphela kwambili kuti tikhale oleza mtima, na kuyesetsa kukhala otelo, khalidweli lidzazika mizu mumtima mwathu. Ndipo lidzakhala umunthu wathu. Zingakhalenso zothandiza kusinkhasinkha zitsanzo za m’Baibo. M’Baibo muli zitsanzo zambili za anthu amene anali oleza mtima. Tikamasinkhasinkha zitsanzo zimenezo, tidzaphunzila mmene tingaonetsele kuleza mtima. w23.08 22 ¶10-11

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Sondo, October 19

Muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.​—Luka 5:4.

Yesu anam’tsimikizila mtumwi Petulo kuti Yehova adzam’thandiza. Iye ataukitsidwa, anacitanso cozizwitsa kwa Petulo na atumwi anzake powathandiza kupha nsomba. (Yoh. 21:4-6) Mosakayikila, cozizwitsa cimeneci cinatsimikizila Petulo kuti Yehova adzasamalila zosoŵa zake zakuthupi. N’kutheka kuti mtumwiyu anakumbukila mawu a Yesu akuti Yehova adzasamalila anthu amene ‘apitiliza kufuna-funa Ufumu coyamba.’ (Mat. 6:33) Izi zinapangitsa Petulo kuika utumikila patsogolo m’malo mwa nchito yake ya usodzi. Iye molimba mtima analalikila pa Pentekosite mu 33 C.E., ndipo anthu masauzande analabadila uthenga wabwino. (Mac. 2:14, 37-41) Pambuyo pake, iye anathandiza Asamariya na anthu amitundu ina kuphunzila za Khristu na kum’tsatila. (Mac. 8:14-17; 10:44-48) Zoonadi, Yehova anam’gwilitsa nchito kwambili pokoka anthu a mitundu yonse kuti abwele mu mpingo. w23.09 20 ¶1; 23 ¶11

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Mande, October 20

Ngati simundiuza zimene ndalota nʼkundimasulila, ndikudulani nthulinthuli.​—Dan. 2:5.

Patapita zaka pafupifupi ziŵili Ababulo atawononga Yerusalemu, Mfumu Nebukadinezara ya Babulo inalota maloto othetsa nzelu okhudza cifanizilo cacikulu. Inaopseza kuti idzapha amuna onse anzelu, kuphatikizapo Danieli, akalephela kuiuza zimene yalota komanso kumasulila kwake. (Dan. 2:3-5) Danieli anacitapo kanthu mwamsanga, cifukwa anthu ambili akanaphedwa. Iye “anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulile maloto ake.” (Dan. 2:16) Izi zinafuna kulimba mtima na cikhulupililo. Baibo siionetsa kuti Danieli anamasulilapo maloto m’mbuyomo. Iye anapempha anzake atatu, kuti “apemphele kwa Mulungu wakumwamba kuti awacitile cifundo ndi kuwaululila cinsinsi cimeneci.” (Dan. 2:18) Yehova anayankha mapemphelo awo, moti anathandiza Danieli kumasulila maloto a Nebukadinezara. Conco, Danieli na anzakewo sanaphedwe. w23.08 3 ¶4

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani