Sondo, October 19
Muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.—Luka 5:4.
Yesu anam’tsimikizila mtumwi Petulo kuti Yehova adzam’thandiza. Iye ataukitsidwa, anacitanso cozizwitsa kwa Petulo na atumwi anzake powathandiza kupha nsomba. (Yoh. 21:4-6) Mosakayikila, cozizwitsa cimeneci cinatsimikizila Petulo kuti Yehova adzasamalila zosoŵa zake zakuthupi. N’kutheka kuti mtumwiyu anakumbukila mawu a Yesu akuti Yehova adzasamalila anthu amene ‘apitiliza kufuna-funa Ufumu coyamba.’ (Mat. 6:33) Izi zinapangitsa Petulo kuika utumikila patsogolo m’malo mwa nchito yake ya usodzi. Iye molimba mtima analalikila pa Pentekosite mu 33 C.E., ndipo anthu masauzande analabadila uthenga wabwino. (Mac. 2:14, 37-41) Pambuyo pake, iye anathandiza Asamariya na anthu amitundu ina kuphunzila za Khristu na kum’tsatila. (Mac. 8:14-17; 10:44-48) Zoonadi, Yehova anam’gwilitsa nchito kwambili pokoka anthu a mitundu yonse kuti abwele mu mpingo. w23.09 20 ¶1; 23 ¶11
Mande, October 20
Ngati simundiuza zimene ndalota nʼkundimasulila, ndikudulani nthulinthuli.—Dan. 2:5.
Patapita zaka pafupifupi ziŵili Ababulo atawononga Yerusalemu, Mfumu Nebukadinezara ya Babulo inalota maloto othetsa nzelu okhudza cifanizilo cacikulu. Inaopseza kuti idzapha amuna onse anzelu, kuphatikizapo Danieli, akalephela kuiuza zimene yalota komanso kumasulila kwake. (Dan. 2:3-5) Danieli anacitapo kanthu mwamsanga, cifukwa anthu ambili akanaphedwa. Iye “anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulile maloto ake.” (Dan. 2:16) Izi zinafuna kulimba mtima na cikhulupililo. Baibo siionetsa kuti Danieli anamasulilapo maloto m’mbuyomo. Iye anapempha anzake atatu, kuti “apemphele kwa Mulungu wakumwamba kuti awacitile cifundo ndi kuwaululila cinsinsi cimeneci.” (Dan. 2:18) Yehova anayankha mapemphelo awo, moti anathandiza Danieli kumasulila maloto a Nebukadinezara. Conco, Danieli na anzakewo sanaphedwe. w23.08 3 ¶4
Ciŵili, October 21
Amene adzapilile mpaka pamapeto ndi amene adzapulumuke.—Mat. 24:13.
Mapindu a kuleza mtima. Tikakhala oleza mtima, timakhala acimwemwe komanso odekha. Izi zimathandiza kuti tikhale na thanzi labwinopo. Tikamalezela mtima anthu ena, timakhala nawo pa ubale wabwino. Mpingo umakhala wogwilizana kwambili. Ndipo wina akatikhumudwitsa, kusakwiya msanga kumatithandiza kupewa kuikulitsa nkhaniyo. (Sal. 37:8; Miy. 14:29) Koma coposa zonse, timatengela Atate wathu wakumwamba, ndipo timamuyandikila kwambili. Kuleza mtima ni khalidwe labwino zedi! Ngakhale kuti nthawi zina kuleza mtima kumavuta, Yehova angatithandize kukulitsa khalidwe limeneli. Ndipo pamene tikuyembekezela moleza mtima dziko latsopano, sitikayikila olo pang’ono kuti “diso la Yehova limayangʼana anthu amene amamuopa, amene amayembekezela cikondi cake cokhulupilika.” (Sal. 33:18) Conde, tisaleke kuvala kuleza mtima. w23.08 22 ¶7; 25 ¶16-17