Mande, October 20
Ngati simundiuza zimene ndalota nʼkundimasulila, ndikudulani nthulinthuli.—Dan. 2:5.
Patapita zaka pafupifupi ziŵili Ababulo atawononga Yerusalemu, Mfumu Nebukadinezara ya Babulo inalota maloto othetsa nzelu okhudza cifanizilo cacikulu. Inaopseza kuti idzapha amuna onse anzelu, kuphatikizapo Danieli, akalephela kuiuza zimene yalota komanso kumasulila kwake. (Dan. 2:3-5) Danieli anacitapo kanthu mwamsanga, cifukwa anthu ambili akanaphedwa. Iye “anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulile maloto ake.” (Dan. 2:16) Izi zinafuna kulimba mtima na cikhulupililo. Baibo siionetsa kuti Danieli anamasulilapo maloto m’mbuyomo. Iye anapempha anzake atatu, kuti “apemphele kwa Mulungu wakumwamba kuti awacitile cifundo ndi kuwaululila cinsinsi cimeneci.” (Dan. 2:18) Yehova anayankha mapemphelo awo, moti anathandiza Danieli kumasulila maloto a Nebukadinezara. Conco, Danieli na anzakewo sanaphedwe. w23.08 3 ¶4
Ciŵili, October 21
Amene adzapilile mpaka pamapeto ndi amene adzapulumuke.—Mat. 24:13.
Mapindu a kuleza mtima. Tikakhala oleza mtima, timakhala acimwemwe komanso odekha. Izi zimathandiza kuti tikhale na thanzi labwinopo. Tikamalezela mtima anthu ena, timakhala nawo pa ubale wabwino. Mpingo umakhala wogwilizana kwambili. Ndipo wina akatikhumudwitsa, kusakwiya msanga kumatithandiza kupewa kuikulitsa nkhaniyo. (Sal. 37:8; Miy. 14:29) Koma coposa zonse, timatengela Atate wathu wakumwamba, ndipo timamuyandikila kwambili. Kuleza mtima ni khalidwe labwino zedi! Ngakhale kuti nthawi zina kuleza mtima kumavuta, Yehova angatithandize kukulitsa khalidwe limeneli. Ndipo pamene tikuyembekezela moleza mtima dziko latsopano, sitikayikila olo pang’ono kuti “diso la Yehova limayangʼana anthu amene amamuopa, amene amayembekezela cikondi cake cokhulupilika.” (Sal. 33:18) Conde, tisaleke kuvala kuleza mtima. w23.08 22 ¶7; 25 ¶16-17
Citatu, October 22
Cikhulupililo pacokha, ngati cilibe nchito zake, ndi cakufa.—Yak. 2:17.
Yakobo anafotokoza kuti munthu angakambe kuti ali na cikhulupililo. Koma kodi nchito zake zigwilizana na cikhulupililoco? (Yak. 2:1-5, 9) Yakobo anachulanso za munthu yemwe anaona “m’bale kapena mlongo ali waumphawi ndipo alibe cakudya cokwanila pa tsikulo,” koma sanapeleke thandizo lofunikila. Munthuyo angakambe kuti ali na cikhulupililo, koma cifukwa cakuti sanacionetse na zocita zake, cikhoza kukhala copanda pake. (Yak. 2:14-16) Yakobo anaseŵenzetsa Rahabi monga citsanzo ca munthu amene anaonetsa cikhulupililo mwa nchito zake. (Yakobo 2:25, 26) Iye anamva za Yehova, ndipo anadziŵa kuti anali kuthandizila Aisiraeli. (Yos. 2:9-11) Anaonetsa cikhulupililo mwa nchito zake—anateteza azondi aŵili aciisiraeli amene miyoyo yawo inali pa ciopsezo. Mwa izi, mkazi wopanda ungwilo ameneyu, komanso yemwe sanali Mwisiraeli n’komwe, anaonedwa kukhala wolungama monga zinalili kwa Abulahamu. Nkhani ya Rahabi itionetsa kufunika kokhala na cikhulupililo coonetsedwa na nchito zake. w23.12 5-6 ¶12-13