LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso vitundu vina: Betsimisaraka (Northern), Betsimisaraka (Southern), Konkomba, Matses, Mi'kmaq
  • Lelo

Ciŵili, October 21

Amene adzapilile mpaka pamapeto ndi amene adzapulumuke.​—Mat. 24:13.

Mapindu a kuleza mtima. Tikakhala oleza mtima, timakhala acimwemwe komanso odekha. Izi zimathandiza kuti tikhale na thanzi labwinopo. Tikamalezela mtima anthu ena, timakhala nawo pa ubale wabwino. Mpingo umakhala wogwilizana kwambili. Ndipo wina akatikhumudwitsa, kusakwiya msanga kumatithandiza kupewa kuikulitsa nkhaniyo. (Sal. 37:8; Miy. 14:29) Koma coposa zonse, timatengela Atate wathu wakumwamba, ndipo timamuyandikila kwambili. Kuleza mtima ni khalidwe labwino zedi! Ngakhale kuti nthawi zina kuleza mtima kumavuta, Yehova angatithandize kukulitsa khalidwe limeneli. Ndipo pamene tikuyembekezela moleza mtima dziko latsopano, sitikayikila olo pang’ono kuti “diso la Yehova limayangʼana anthu amene amamuopa, amene amayembekezela cikondi cake cokhulupilika.” (Sal. 33:18) Conde, tisaleke kuvala kuleza mtima. w23.08 22 ¶7; 25 ¶16-17

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Citatu, October 22

Cikhulupililo pacokha, ngati cilibe nchito zake, ndi cakufa.​—Yak. 2:17.

Yakobo anafotokoza kuti munthu angakambe kuti ali na cikhulupililo. Koma kodi nchito zake zigwilizana na cikhulupililoco? (Yak. 2:1-5, 9) Yakobo anachulanso za munthu yemwe anaona “m’bale kapena mlongo ali waumphawi ndipo alibe cakudya cokwanila pa tsikulo,” koma sanapeleke thandizo lofunikila. Munthuyo angakambe kuti ali na cikhulupililo, koma cifukwa cakuti sanacionetse na zocita zake, cikhoza kukhala copanda pake. (Yak. 2:14-16) Yakobo anaseŵenzetsa Rahabi monga citsanzo ca munthu amene anaonetsa cikhulupililo mwa nchito zake. (Yakobo 2:25, 26) Iye anamva za Yehova, ndipo anadziŵa kuti anali kuthandizila Aisiraeli. (Yos. 2:9-11) Anaonetsa cikhulupililo mwa nchito zake​—anateteza azondi aŵili aciisiraeli amene miyoyo yawo inali pa ciopsezo. Mwa izi, mkazi wopanda ungwilo ameneyu, komanso yemwe sanali Mwisiraeli n’komwe, anaonedwa kukhala wolungama monga zinalili kwa Abulahamu. Nkhani ya Rahabi itionetsa kufunika kokhala na cikhulupililo coonetsedwa na nchito zake. w23.12 5-6 ¶12-13

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cinayi, October 23

Muzike mizu ndiponso mukhale okhazikika pamaziko.​—Aef. 3:17.

Kwa ife Akhristu kungomvetsa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo si kokwanila. Mwathandizo la mzimu woyela, ndife ofunitsitsa kudziŵa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:9, 10) Pa phunzilo la inu mwini, bwanji osadziikila colinga cophunzila mfudo zozama za mawu a Mulungu kuti mumuyandikile kwambili Yehova? Mwacitsanzo, mungafufuze mmene Yehova anaonetsela cikondi kwa atumiki ake akale na kuona mmene izi zionetsela kuti amakukondani. Mungafufuze za dongosolo la kulambila Yehova m’nthawi ya Aisiraeli na kuliyelekezela na dongosolo la masiku ano. Kapena mungaŵelenge mozama maulosi amene Yesu anakwanilitsa ali padziko lapansi. Mungapeze cimwemwe pophunzila nkhani zimenezi poseŵenzetsa Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova. Kucita phunzilo la Baibo la inu mwini mozama kudzalimbikitsa cikhulupililo canu na kukuthandizani ‘kum’dziŵadi Mulungu.’ Miy. 2:4, 5. w23.10 18-19 ¶3-5

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani