Citatu, October 22
Cikhulupililo pacokha, ngati cilibe nchito zake, ndi cakufa.—Yak. 2:17.
Yakobo anafotokoza kuti munthu angakambe kuti ali na cikhulupililo. Koma kodi nchito zake zigwilizana na cikhulupililoco? (Yak. 2:1-5, 9) Yakobo anachulanso za munthu yemwe anaona “m’bale kapena mlongo ali waumphawi ndipo alibe cakudya cokwanila pa tsikulo,” koma sanapeleke thandizo lofunikila. Munthuyo angakambe kuti ali na cikhulupililo, koma cifukwa cakuti sanacionetse na zocita zake, cikhoza kukhala copanda pake. (Yak. 2:14-16) Yakobo anaseŵenzetsa Rahabi monga citsanzo ca munthu amene anaonetsa cikhulupililo mwa nchito zake. (Yakobo 2:25, 26) Iye anamva za Yehova, ndipo anadziŵa kuti anali kuthandizila Aisiraeli. (Yos. 2:9-11) Anaonetsa cikhulupililo mwa nchito zake—anateteza azondi aŵili aciisiraeli amene miyoyo yawo inali pa ciopsezo. Mwa izi, mkazi wopanda ungwilo ameneyu, komanso yemwe sanali Mwisiraeli n’komwe, anaonedwa kukhala wolungama monga zinalili kwa Abulahamu. Nkhani ya Rahabi itionetsa kufunika kokhala na cikhulupililo coonetsedwa na nchito zake. w23.12 5-6 ¶12-13
Cinayi, October 23
Muzike mizu ndiponso mukhale okhazikika pamaziko.—Aef. 3:17.
Kwa ife Akhristu kungomvetsa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo si kokwanila. Mwathandizo la mzimu woyela, ndife ofunitsitsa kudziŵa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:9, 10) Pa phunzilo la inu mwini, bwanji osadziikila colinga cophunzila mfudo zozama za mawu a Mulungu kuti mumuyandikile kwambili Yehova? Mwacitsanzo, mungafufuze mmene Yehova anaonetsela cikondi kwa atumiki ake akale na kuona mmene izi zionetsela kuti amakukondani. Mungafufuze za dongosolo la kulambila Yehova m’nthawi ya Aisiraeli na kuliyelekezela na dongosolo la masiku ano. Kapena mungaŵelenge mozama maulosi amene Yesu anakwanilitsa ali padziko lapansi. Mungapeze cimwemwe pophunzila nkhani zimenezi poseŵenzetsa Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova. Kucita phunzilo la Baibo la inu mwini mozama kudzalimbikitsa cikhulupililo canu na kukuthandizani ‘kum’dziŵadi Mulungu.’ Miy. 2:4, 5. w23.10 18-19 ¶3-5
Cisanu, October 24
Muzikondana kwambili cifukwa cikondi cimakwilila macimo oculuka.—1 Pet. 4:8.
Mawu amene mtumwi Petulo anaseŵenzetsa akuti “kwambili” amatanthauza “kufutukula.” Mbali yaciŵili ya vesiyi ionetsa zimene zingacitike ngati timakondana kwambili. Timatha kukwilila macimo a abale. Tiyelekeze motele: Timagwila cikondi na manja aŵili monga nsalu imene ingatambasuke. Timaitambasula mpaka itaphimba, osati imodzi kapena aŵili, koma “macimo oculuka.” “Kuphimba” kutanthauza kukhululuka. Monga momwe nsalu ingaphimbile kusaoneka bwino kwa zinthu, cikondi naconso cimaphimba zifooko komanso kupanda ungwilo kwa ena. Cikondi cathu pa ena ciyenela kukhala cacikulu kuti tikwanitse kukhululukila zophophonya za okhulupilila anzathu, ngakhale kuti nthawi zina sicopepuka kutelo. (Akol. 3:13) Tikakwanitsa kukhululukila ena timaonetsa kuti cikondi cathu pa iwo n’colimba, ndiponso kuti tifuna kukondweletsa Yehova. w23.11 11-12 ¶13-15