LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso citundu cina: Betsileo
  • Lelo

Cinayi, October 23

Muzike mizu ndiponso mukhale okhazikika pamaziko.​—Aef. 3:17.

Kwa ife Akhristu kungomvetsa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo si kokwanila. Mwathandizo la mzimu woyela, ndife ofunitsitsa kudziŵa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:9, 10) Pa phunzilo la inu mwini, bwanji osadziikila colinga cophunzila mfudo zozama za mawu a Mulungu kuti mumuyandikile kwambili Yehova? Mwacitsanzo, mungafufuze mmene Yehova anaonetsela cikondi kwa atumiki ake akale na kuona mmene izi zionetsela kuti amakukondani. Mungafufuze za dongosolo la kulambila Yehova m’nthawi ya Aisiraeli na kuliyelekezela na dongosolo la masiku ano. Kapena mungaŵelenge mozama maulosi amene Yesu anakwanilitsa ali padziko lapansi. Mungapeze cimwemwe pophunzila nkhani zimenezi poseŵenzetsa Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova. Kucita phunzilo la Baibo la inu mwini mozama kudzalimbikitsa cikhulupililo canu na kukuthandizani ‘kum’dziŵadi Mulungu.’ Miy. 2:4, 5. w23.10 18-19 ¶3-5

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cisanu, October 24

Muzikondana kwambili cifukwa cikondi cimakwilila macimo oculuka.​—1 Pet. 4:8.

Mawu amene mtumwi Petulo anaseŵenzetsa akuti “kwambili” amatanthauza “kufutukula.” Mbali yaciŵili ya vesiyi ionetsa zimene zingacitike ngati timakondana kwambili. Timatha kukwilila macimo a abale. Tiyelekeze motele: Timagwila cikondi na manja aŵili monga nsalu imene ingatambasuke. Timaitambasula mpaka itaphimba, osati imodzi kapena aŵili, koma “macimo oculuka.” “Kuphimba” kutanthauza kukhululuka. Monga momwe nsalu ingaphimbile kusaoneka bwino kwa zinthu, cikondi naconso cimaphimba zifooko komanso kupanda ungwilo kwa ena. Cikondi cathu pa ena ciyenela kukhala cacikulu kuti tikwanitse kukhululukila zophophonya za okhulupilila anzathu, ngakhale kuti nthawi zina sicopepuka kutelo. (Akol. 3:13) Tikakwanitsa kukhululukila ena timaonetsa kuti cikondi cathu pa iwo n’colimba, ndiponso kuti tifuna kukondweletsa Yehova. w23.11 11-12 ¶13-15

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵelu, October 25

Safani anayamba kuŵelengela mfumu bukulo.​—2 Mbiri 34:18.

Atakula, Mfumu Yosiya anayamba nchito yokonzanso kacisi. Nchitoyo ili mkati, “anapeza buku la Cilamulo ca Yehova lopelekedwa kudzela mwa Mose.” Atamva bukulo likuŵelengedwa, Yosiya anacitapo kanthu mwa kuyamba kutsatila zimene anali kuŵelenga m’bukulo. (2 Mbiri 34:14, 19-21) Kodi mumafuna kuŵelenga Baibo tsiku lililonse? Ngati munayamba kale, kodi zikuyenda bwanji? Kodi mumasungako mavesi ena amene angakuthandizeni pacanu? Ali na zaka ngati 39, Yosiya anapanga cisankho colakwika cimene cinam’tayitsa moyo wake. Anadzidalila m’malo modalila Yehova kuti amutsogolele. (2 Mbiri 35:20-25) Tiphunzilapo ciyani? Kaya tili na zaka zingati, kapena takhala tikuphunzila Baibo kwa nthawi yaitali bwanji, sitiyenela kuleka kumufuna-funa Yehova. Izi ziphatikizapo kupempha citsogozo cake nthawi zonse, kuphunzila Mawu ake, na kugwilitsa nchito ulangizi wa Akhristu okhwima. Tikamatelo, tidzapewa kupanga zisankho zolakwika, ndipo tidzakhala osangalala.​—Yak. 1:25. w23.09 12 ¶15-16

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani