Cisanu, October 24
Muzikondana kwambili cifukwa cikondi cimakwilila macimo oculuka.—1 Pet. 4:8.
Mawu amene mtumwi Petulo anaseŵenzetsa akuti “kwambili” amatanthauza “kufutukula.” Mbali yaciŵili ya vesiyi ionetsa zimene zingacitike ngati timakondana kwambili. Timatha kukwilila macimo a abale. Tiyelekeze motele: Timagwila cikondi na manja aŵili monga nsalu imene ingatambasuke. Timaitambasula mpaka itaphimba, osati imodzi kapena aŵili, koma “macimo oculuka.” “Kuphimba” kutanthauza kukhululuka. Monga momwe nsalu ingaphimbile kusaoneka bwino kwa zinthu, cikondi naconso cimaphimba zifooko komanso kupanda ungwilo kwa ena. Cikondi cathu pa ena ciyenela kukhala cacikulu kuti tikwanitse kukhululukila zophophonya za okhulupilila anzathu, ngakhale kuti nthawi zina sicopepuka kutelo. (Akol. 3:13) Tikakwanitsa kukhululukila ena timaonetsa kuti cikondi cathu pa iwo n’colimba, ndiponso kuti tifuna kukondweletsa Yehova. w23.11 11-12 ¶13-15
Ciŵelu, October 25
Safani anayamba kuŵelengela mfumu bukulo.—2 Mbiri 34:18.
Atakula, Mfumu Yosiya anayamba nchito yokonzanso kacisi. Nchitoyo ili mkati, “anapeza buku la Cilamulo ca Yehova lopelekedwa kudzela mwa Mose.” Atamva bukulo likuŵelengedwa, Yosiya anacitapo kanthu mwa kuyamba kutsatila zimene anali kuŵelenga m’bukulo. (2 Mbiri 34:14, 19-21) Kodi mumafuna kuŵelenga Baibo tsiku lililonse? Ngati munayamba kale, kodi zikuyenda bwanji? Kodi mumasungako mavesi ena amene angakuthandizeni pacanu? Ali na zaka ngati 39, Yosiya anapanga cisankho colakwika cimene cinam’tayitsa moyo wake. Anadzidalila m’malo modalila Yehova kuti amutsogolele. (2 Mbiri 35:20-25) Tiphunzilapo ciyani? Kaya tili na zaka zingati, kapena takhala tikuphunzila Baibo kwa nthawi yaitali bwanji, sitiyenela kuleka kumufuna-funa Yehova. Izi ziphatikizapo kupempha citsogozo cake nthawi zonse, kuphunzila Mawu ake, na kugwilitsa nchito ulangizi wa Akhristu okhwima. Tikamatelo, tidzapewa kupanga zisankho zolakwika, ndipo tidzakhala osangalala.—Yak. 1:25. w23.09 12 ¶15-16
Sondo, October 26
Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzicepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.—Yak. 4:6.
Baibo imachula akazi ambili amene anali kum’konda Yehova na kum’tumikila. Iwo anali “ocita zinthu mosapitilila malile” komanso “okhulupilika m’zinthu zonse.” (1 Tim. 3:11) Kuwonjezela apo, alongo acitsikana angapeze zitsanzo zabwino za alongo okhwima mwauzimu zimene angatengele mumpingo mwawo. Inu alongo acitsikana, ganizilani zitsanzo za alongo okhwima mwauzimu amene mungatengeleko. Onani makhalidwe osililika amene ali nawo ndiyeno ganizilani mmene mungayaonetsele. Kudzicepetsa ni khalidwe lofunika kuti munthu akhale Mkhristu wokhwima. Mkazi akakhala wodzicepetsa, amasangalala na ubwenzi wabwino na Yehova komanso na anthu ena. Mwacitsanzo, mkazi wokonda Yehova amasankha kucilikiza lamulo la umutu limene Atate wake wakumwamba anakhazikitsa. (1 Akor. 11:3) Mfundo imeneyi imagwila nchito mumpingo komanso m’banja. w23.12 18-19 ¶3-5