Sondo, October 26
Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzicepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.—Yak. 4:6.
Baibo imachula akazi ambili amene anali kum’konda Yehova na kum’tumikila. Iwo anali “ocita zinthu mosapitilila malile” komanso “okhulupilika m’zinthu zonse.” (1 Tim. 3:11) Kuwonjezela apo, alongo acitsikana angapeze zitsanzo zabwino za alongo okhwima mwauzimu zimene angatengele mumpingo mwawo. Inu alongo acitsikana, ganizilani zitsanzo za alongo okhwima mwauzimu amene mungatengeleko. Onani makhalidwe osililika amene ali nawo ndiyeno ganizilani mmene mungayaonetsele. Kudzicepetsa ni khalidwe lofunika kuti munthu akhale Mkhristu wokhwima. Mkazi akakhala wodzicepetsa, amasangalala na ubwenzi wabwino na Yehova komanso na anthu ena. Mwacitsanzo, mkazi wokonda Yehova amasankha kucilikiza lamulo la umutu limene Atate wake wakumwamba anakhazikitsa. (1 Akor. 11:3) Mfundo imeneyi imagwila nchito mumpingo komanso m’banja. w23.12 18-19 ¶3-5
Mande, October 27
Amuna azikonda akazi awo ngati mmene amakondela matupi awo.—Aef. 5:28.
Yehova amayembekezela mwamuna kumukonda mkazi wake na kumusamalila kuthupi komanso kuuzimu. Kukhala oganiza bwino, kulemekeza akazi, komanso kukhala wodalilika, kungakuthandizeni mukadzakwatila. Mukakwatila, mungakhale tate. Mungaphunzile ciyani kwa Yehova pa nkhani yokhala tate wabwino? (Aef. 6:4) Yehova anauza mwana wake Yesu pa anthu kuti amamukonda komanso kuti amakondwela naye. (Mat. 3:17) Mukadzakhala tate muzikaonetsetsa kuti nthawi na nthawi mukuwatsimikizila ana anu kuti mumawakonda. Muzikawayamikila moona mtima pa zimene azikacita bwino. Atate amene amatengela citsanzo ca Yehova amathandiza ana awo kukhala Akhristu okhwima. Mungakonzekele pali pano udindo umenewu mwa kusamalila ena mwacikondi m’banja na mu mpingo komanso mwa kuwayamikila.—Yoh. 15:9. w23.12 28-29 ¶17-18
Ciŵili, October 28
Mʼmasiku anu, [Yehova] adzacititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.—Yes. 33:6.
Ngakhale kuti ndife atumiki okhulupilika a Yehova, nafenso timakumana na zovuta, komanso kudwala monga mmene zilili na anthu ena. Kuwonjezela apo, timafunikanso kupilila citsutso kapena mazunzo ocokela kwa anthu amene amadana na anthu a Mulungu. Ngakhale kuti Yehova satiteteza ku mavutowa, iye analonjeza kuti adzatithandiza. (Yes. 41:10) Na thandizo lake, tingakhalebe acimwemwe, kupanga zisankho zanzelu, komanso kukhalabe okhulupilika kwa iye ngakhale pomwe tikukumana na zinthu zovuta. Yehova analonjeza kutipatsa cimene Baibo imacha “mtendele wa Mulungu.” (Afil. 4:6, 7) Mtendele umenewu umatithandiza kukhala odekha, komanso a bata mu mtima cifukwa cokhala pa ubale wa mtengo wapatali na iye. Mtendele umenewu “anthu sangathe kuumvetsa”; ndipo ni wapadela kwambili kuposa mmene tingaganizile. Kodi munakhalapo wodekha pambuyo popemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima? Munamva conco cifukwa iye anakupatsani “mtendele wa Mulungu.” w24.01 20 ¶2; 21 ¶4