Ciŵili, October 28
Mʼmasiku anu, [Yehova] adzacititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.—Yes. 33:6.
Ngakhale kuti ndife atumiki okhulupilika a Yehova, nafenso timakumana na zovuta, komanso kudwala monga mmene zilili na anthu ena. Kuwonjezela apo, timafunikanso kupilila citsutso kapena mazunzo ocokela kwa anthu amene amadana na anthu a Mulungu. Ngakhale kuti Yehova satiteteza ku mavutowa, iye analonjeza kuti adzatithandiza. (Yes. 41:10) Na thandizo lake, tingakhalebe acimwemwe, kupanga zisankho zanzelu, komanso kukhalabe okhulupilika kwa iye ngakhale pomwe tikukumana na zinthu zovuta. Yehova analonjeza kutipatsa cimene Baibo imacha “mtendele wa Mulungu.” (Afil. 4:6, 7) Mtendele umenewu umatithandiza kukhala odekha, komanso a bata mu mtima cifukwa cokhala pa ubale wa mtengo wapatali na iye. Mtendele umenewu “anthu sangathe kuumvetsa”; ndipo ni wapadela kwambili kuposa mmene tingaganizile. Kodi munakhalapo wodekha pambuyo popemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima? Munamva conco cifukwa iye anakupatsani “mtendele wa Mulungu.” w24.01 20 ¶2; 21 ¶4
Citatu, October 29
Moyo wanga utamande Yehova. Ciliconse ca mkati mwanga, citamande dzina lake loyela.—Sal. 103:1.
Kukonda Mulungu kumasonkhezela anthu okhulupilika kulemekeza dzina lake na mtima wonse. Mfumu Davide anadziŵa kuti kutamanda dzina la Yehova kunali kutamanda Yehova iye mwini. Dzina la Yehova limaphatikizapo mbili yake. Limatikumbutsa za makhalidwe ake abwino, komanso zocita zake zocititsa cidwi. Davide anaona dzina la Atate wake kukhala loyela, ndipo analitamanda. Anacita zimenezi na ‘ciliconse ca mkati mwake’—kutanthauza kuti na mtima wake wonse. Mofananamo, Alevi anatsogolela pa nchito yotamanda Yehova. Iwo anavomeleza modzicepetsa kuti mawu awo sakanakwanitsa kupeleka citamando coyenela kupatulika kwa dzinalo. (Neh. 9:5) Mosakaikila, mawu odzicepetsa acitamando amenewa, anakondweletsa mtima wa Yehova. w24.02 9 ¶6
Cinayi, October 30
Mulimonse mmene tapitila patsogolo, tiyeni tipitilize kupita patsogolo pocita zomwe tikucitazo.—Afil. 3:16.
Mukalephela kukwanilitsa colinga cimene simukanacikwanitsa, Yehova sadzakuonani kuti ndinu wolephela. (2 Akor. 8:12) Mukalephelako nthawi zina, tengam’poni phunzilo Baibo imati: “Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu.” (Aheb. 6:10) Conco inunso musamaiŵale. Muziganizila zimene mwakwanilitsapo kale, monga kupalana ubwenzi na Yehova, kuuzako ena za iye, kapena kubatizika. Ngati munakwanilitsa zolinga zanu zauzimu kumbuyoku, n’zotheka kukwanilitsanso zolinga zimene muli nazo palipano. Mwa thandizo la Yehova, n’zotheka kukwanilitsa zolinga zanu. Pamene muyesetsa kukwanilitsa zolinga zanu, muzisangalala poona mmene Yehova akukuthandizilani kukwanilitsa colinga canu. (2 Akor. 4:7) Mukapanda kutopa, mudzalandila madalitso osaneneka.—Agal. 6:9. w23.05 31 ¶16-18