LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Citatu, October 29

Moyo wanga utamande Yehova. Ciliconse ca mkati mwanga, citamande dzina lake loyela.​—Sal. 103:1.

Kukonda Mulungu kumasonkhezela anthu okhulupilika kulemekeza dzina lake na mtima wonse. Mfumu Davide anadziŵa kuti kutamanda dzina la Yehova kunali kutamanda Yehova iye mwini. Dzina la Yehova limaphatikizapo mbili yake. Limatikumbutsa za makhalidwe ake abwino, komanso zocita zake zocititsa cidwi. Davide anaona dzina la Atate wake kukhala loyela, ndipo analitamanda. Anacita zimenezi na ‘ciliconse ca mkati mwake’​—kutanthauza kuti na mtima wake wonse. Mofananamo, Alevi anatsogolela pa nchito yotamanda Yehova. Iwo anavomeleza modzicepetsa kuti mawu awo sakanakwanitsa kupeleka citamando coyenela kupatulika kwa dzinalo. (Neh. 9:5) Mosakaikila, mawu odzicepetsa acitamando amenewa, anakondweletsa mtima wa Yehova. w24.02 9 ¶6

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cinayi, October 30

Mulimonse mmene tapitila patsogolo, tiyeni tipitilize kupita patsogolo pocita zomwe tikucitazo.​—Afil. 3:16.

Mukalephela kukwanilitsa colinga cimene simukanacikwanitsa, Yehova sadzakuonani kuti ndinu wolephela. (2 Akor. 8:12) Mukalephelako nthawi zina, tengam’poni phunzilo Baibo imati: “Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu.” (Aheb. 6:10) Conco inunso musamaiŵale. Muziganizila zimene mwakwanilitsapo kale, monga kupalana ubwenzi na Yehova, kuuzako ena za iye, kapena kubatizika. Ngati munakwanilitsa zolinga zanu zauzimu kumbuyoku, n’zotheka kukwanilitsanso zolinga zimene muli nazo palipano. Mwa thandizo la Yehova, n’zotheka kukwanilitsa zolinga zanu. Pamene muyesetsa kukwanilitsa zolinga zanu, muzisangalala poona mmene Yehova akukuthandizilani kukwanilitsa colinga canu. (2 Akor. 4:7) Mukapanda kutopa, mudzalandila madalitso osaneneka.​—Agal. 6:9. w23.05 31 ¶16-18

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cisanu, October 31

Atatewo amakukondani cifukwa munandikonda ndipo mwakhulupilila kuti ine ndinabwela monga nthumwi ya Mulungu.​—Yoh 16:27.

Yehova amafuna-funa mipata yoonetsa anthu kuti amawakonda, komanso kuti amakondwela nawo. Malemba amakamba nthawi ziŵili pomwe Iye anauza Yesu kuti ni Mwana wake wokondedwa, ndiponso kuti amakondwela naye. (Mat. 3:17; 17:5) Kodi mungakonde kumva Yehova akukuuzani kuti amakondwela nanu? Yehova sakamba nafe mwacindunji masiku ano, koma amatelo kupitila m’Mawu ake. Timamva mawu a Yehova otitsimikizila kuti amakondwela nafe tikaŵelenga mawu a Yesu opezeka m’Mauthenga Abwino. Yesu anatengela bwino kwambili makhalidwe a Atate wake. Cotelo, tikamaŵelenga mawu a Yesu oonetsa kuti anali kuwakonda otsatila ake opanda ungwilo koma okhulupilika, zimakhala ngati tikumumva Yehova akutiuza mawu amenewo. (Yoh. 15:9, 15) Kukumana na mavuto si umboni wakuti Mulungu analeka kukondwela nafe. M’malo mwake, kumatipatsa mwayi woonetsa kuzama kwa cikondi cathu pa Mulungu, komanso kukula kwa cidalilo cathu mwa iye.​—Yak. 1:12. w24.03 28 ¶10-11

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani