Ciŵelu, November 1
Mwacititsa kuti mʼkamwa mwa ana ndi mwa makanda mutuluke mawu otamanda.—Mat. 21:16.
Ngati ndinu kholo, thandizani ana anu kukonzekela ndemanga malinga na msinkhu wawo. Nthawi zina, timakambilana nkhani zikulu-zikulu monga zokhudza mavuto a m’banja kapena ciyelo ca mpingo. Koma pamakhalabe ndime imodzi kapena ziŵili zimene ana angapelekepo ndemanga. Cina, fotokozelani ana anu kuti si nthawi zonse pomwe angapatsidwe mwayi woyankhapo akakweza dzanja. Kucita izi kudzawathandiza kuti asamakhumudwe mwayi woyankhapo ukapatsidwa kwa ena. (1 Tim. 6:18) Tonsefe tingakonzekele ndemanga zogwila mtima zimene zimalemekeza Yehova, na kulimbikitsa Akhristu anzathu. (Miy. 25:11) Ngakhale kuti nthawi zina tingafunike kufotokoza mwacidule zocitika pa umoyo wathu, tiyenela kupewa kukamba kwambili za ife eni. (Miy. 27:2; 2 Akor. 10:18) M’malo mwake, tiziika kwambili maganizo athu pa Yehova, Mawu ake, komanso anthu ake.—Chiv. 4:11. w23.04 24-25 ¶17-18
Sondo, November 2
Tisapitilize kugona ngati mmene ena onse akucitila, koma tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.—1 Ates. 5:6.
Cikondi n’cofunika kwambili kuti tikhalebe maso komanso oganiza bwino. (Mat. 22:37-39) Kukonda Mulungu kumatithandiza kupilila mavuto amene tingakumane nawo tikamalalikila. (2 Tim. 1:7, 8) Popeza timakondanso anthu amene satumikila Mulungu, timapitilizabe kulalikila pafoni na m’makalata. Timakhala na ciyembekezo cakuti tsiku lina, iwo adzasintha umoyo wawo na kuyamba kucita zabwino. (Ezek. 18:27, 28) Timakondanso Akhristu anzathu. Ndipo timaonetsana cikondi cimeneco mwa “kutonthozana ndi kulimbikitsana.” (1 Ates. 5:11) Monga asilikali amene amaseŵenzela pamodzi pa nkhondo, timalimbikitsana. Sitingakhumudwitse abale na alongo athu mwadala, kapena kubwezela coipa pa coipa. (1 Ates. 5:13, 15) Timaonetsanso cikondi cathu polemekeza abale amene akutsogolela mu mpingo.—1 Ates. 5:12. w23.06 10 ¶6; 11 ¶10-11
Mande, November 3
[Yehova] akanena kanthu, kodi angalephele kucita?—Num. 23:19.
Njila imodzi imene tingalimbitsile cikhulupililo cathu, ni kusinkhasinkha za dipo. Dipo limatitsimikizila kuti malonjezo a Mulungu adzakwanitsidwa. Tikamasinkhasinkha mosamala cifukwa cake dipo linapelekedwa, komanso zimene Mulungu anadzimana, timalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti lonjezo la moyo wosatha m’dziko latsopano ndithu lidzakwanilitsidwa. N’cifukwa ciyani tikutelo? Kodi kupeleka dipo kunaloŵetsamo ciyani? Yehova anatuma Mwana wake woyamba kubadwa komanso wokondeka, kuti acoke kumwamba n’kudzabadwa monga munthu wangwilo. Ali padziko lapansi, Yesu anapilila mazunzo a mtundu uliwonse. Ndipo anavutika mpaka kufa imfa yoŵaŵa. Umenewu unali mtengo waukulu cotani nanga umene Yehova analipila! Mulungu wathu wacikondi sakanalola Mwana wake kuvutika mpaka kufa, kuti tingokhala na umoyo wabwinopo palipano kwa nthawi yocepa. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 1:18, 19) Cifukwa analipila mtengo wokwela kwambili, Yehova adzaonetsetsa kuti lonjezo lake la moyo wamuyaya m’dziko latsopano lakwanilitsidwa. w23.04 27 ¶8-9