Sondo, November 2
Tisapitilize kugona ngati mmene ena onse akucitila, koma tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.—1 Ates. 5:6.
Cikondi n’cofunika kwambili kuti tikhalebe maso komanso oganiza bwino. (Mat. 22:37-39) Kukonda Mulungu kumatithandiza kupilila mavuto amene tingakumane nawo tikamalalikila. (2 Tim. 1:7, 8) Popeza timakondanso anthu amene satumikila Mulungu, timapitilizabe kulalikila pafoni na m’makalata. Timakhala na ciyembekezo cakuti tsiku lina, iwo adzasintha umoyo wawo na kuyamba kucita zabwino. (Ezek. 18:27, 28) Timakondanso Akhristu anzathu. Ndipo timaonetsana cikondi cimeneco mwa “kutonthozana ndi kulimbikitsana.” (1 Ates. 5:11) Monga asilikali amene amaseŵenzela pamodzi pa nkhondo, timalimbikitsana. Sitingakhumudwitse abale na alongo athu mwadala, kapena kubwezela coipa pa coipa. (1 Ates. 5:13, 15) Timaonetsanso cikondi cathu polemekeza abale amene akutsogolela mu mpingo.—1 Ates. 5:12. w23.06 10 ¶6; 11 ¶10-11
Mande, November 3
[Yehova] akanena kanthu, kodi angalephele kucita?—Num. 23:19.
Njila imodzi imene tingalimbitsile cikhulupililo cathu, ni kusinkhasinkha za dipo. Dipo limatitsimikizila kuti malonjezo a Mulungu adzakwanitsidwa. Tikamasinkhasinkha mosamala cifukwa cake dipo linapelekedwa, komanso zimene Mulungu anadzimana, timalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti lonjezo la moyo wosatha m’dziko latsopano ndithu lidzakwanilitsidwa. N’cifukwa ciyani tikutelo? Kodi kupeleka dipo kunaloŵetsamo ciyani? Yehova anatuma Mwana wake woyamba kubadwa komanso wokondeka, kuti acoke kumwamba n’kudzabadwa monga munthu wangwilo. Ali padziko lapansi, Yesu anapilila mazunzo a mtundu uliwonse. Ndipo anavutika mpaka kufa imfa yoŵaŵa. Umenewu unali mtengo waukulu cotani nanga umene Yehova analipila! Mulungu wathu wacikondi sakanalola Mwana wake kuvutika mpaka kufa, kuti tingokhala na umoyo wabwinopo palipano kwa nthawi yocepa. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 1:18, 19) Cifukwa analipila mtengo wokwela kwambili, Yehova adzaonetsetsa kuti lonjezo lake la moyo wamuyaya m’dziko latsopano lakwanilitsidwa. w23.04 27 ¶8-9
Ciŵili, November 4
Iwe Imfa amene umabweletsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?—Hos. 13:14.
Kodi Yehova alidi na cifuno coukitsa akufa? Indedi. Iye anauzila olemba Baibo ambili kulemba lonjezo lake lakuti kutsogoloku adzaukitsa akufa. (Yes. 26:19; Chiv. 20:11-13) Ndipo Yehova akalonjeza, nthawi zonse amakwanilitsa lonjezo lake. (Yos. 23:14) Yehova ni wofunitsitsa kuukitsa akufa. Ganizilani mawu a Yobu. Iye anali wotsimikiza kuti ngakhale atafa, Yehova adzalakalaka kumuonanso. (Yobu 14:14, 15) Yehova amalakalakanso kuukitsa alambili ake onse amene anamwalila. Amafunitsitsa kudzawaukitsa kuti akakhale na moyo wathanzi komanso wacimwemwe. Nanga bwanji za mabiliyoni amene anamwalila asanakhale na mwayi wophunzila coonadi cokhudza Yehova? Mulungu wathu wacikondi amafuna kuwaukitsa nawonso. (Mac. 24:15) Amafuna kuti akawapatse mwayi wokhala mabwenzi ake, komanso kuti akakhale na moyo kwamuyaya padziko lapansi.—Yoh. 3:16. w23.04 9 ¶5-6