Mande, November 3
[Yehova] akanena kanthu, kodi angalephele kucita?—Num. 23:19.
Njila imodzi imene tingalimbitsile cikhulupililo cathu, ni kusinkhasinkha za dipo. Dipo limatitsimikizila kuti malonjezo a Mulungu adzakwanitsidwa. Tikamasinkhasinkha mosamala cifukwa cake dipo linapelekedwa, komanso zimene Mulungu anadzimana, timalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti lonjezo la moyo wosatha m’dziko latsopano ndithu lidzakwanilitsidwa. N’cifukwa ciyani tikutelo? Kodi kupeleka dipo kunaloŵetsamo ciyani? Yehova anatuma Mwana wake woyamba kubadwa komanso wokondeka, kuti acoke kumwamba n’kudzabadwa monga munthu wangwilo. Ali padziko lapansi, Yesu anapilila mazunzo a mtundu uliwonse. Ndipo anavutika mpaka kufa imfa yoŵaŵa. Umenewu unali mtengo waukulu cotani nanga umene Yehova analipila! Mulungu wathu wacikondi sakanalola Mwana wake kuvutika mpaka kufa, kuti tingokhala na umoyo wabwinopo palipano kwa nthawi yocepa. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 1:18, 19) Cifukwa analipila mtengo wokwela kwambili, Yehova adzaonetsetsa kuti lonjezo lake la moyo wamuyaya m’dziko latsopano lakwanilitsidwa. w23.04 27 ¶8-9
Ciŵili, November 4
Iwe Imfa amene umabweletsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?—Hos. 13:14.
Kodi Yehova alidi na cifuno coukitsa akufa? Indedi. Iye anauzila olemba Baibo ambili kulemba lonjezo lake lakuti kutsogoloku adzaukitsa akufa. (Yes. 26:19; Chiv. 20:11-13) Ndipo Yehova akalonjeza, nthawi zonse amakwanilitsa lonjezo lake. (Yos. 23:14) Yehova ni wofunitsitsa kuukitsa akufa. Ganizilani mawu a Yobu. Iye anali wotsimikiza kuti ngakhale atafa, Yehova adzalakalaka kumuonanso. (Yobu 14:14, 15) Yehova amalakalakanso kuukitsa alambili ake onse amene anamwalila. Amafunitsitsa kudzawaukitsa kuti akakhale na moyo wathanzi komanso wacimwemwe. Nanga bwanji za mabiliyoni amene anamwalila asanakhale na mwayi wophunzila coonadi cokhudza Yehova? Mulungu wathu wacikondi amafuna kuwaukitsa nawonso. (Mac. 24:15) Amafuna kuti akawapatse mwayi wokhala mabwenzi ake, komanso kuti akakhale na moyo kwamuyaya padziko lapansi.—Yoh. 3:16. w23.04 9 ¶5-6
Citatu, November 5
Mulungu adzatipatsa mphamvu.—Sal. 108:13.
Kodi mungalimbikitse bwanji ciyembekezo canu? Mwacitsanzo, ngati muli na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya padziko lapansi, muziŵelenga Malemba amene amafotokoza mmene Paradaiso adzakhalile na kuwasinkhasinkha. (Yes. 25:8; 32:16-18) Muziganizila mmene umoyo udzakhalile m’dziko latsopano. Yelekezelani kuti muli m’dzikolo. Tikamaganizila kwambili za ciyembekezo cathu ca dziko latsopano tidzaona mavuto athu kuti ni “akanthawi ndipo ndi opepuka.” (2 Akor. 4:17) Yehova adzakupatsani mphamvu kupitila mu ciyembekezo cimene wakupatsani. Wapeleka zonse zofunika kuti mulandile mphamvu zocokela kwa iye. Conco, mukafuna thandizo kuti mucite utumiki wina wake, kupilila mayeso, kapena kukhalabe na cimwemwe, mufikileni Yehova m’pemphelo mocokela pansi pa mtima, na kufuna-funa citsogozo cake mwa kucita phunzilo la munthu mwini. Cina landilani cilimbikitso kucokela kwa Akhristu anzanu. Komanso sungani ciyembekezo canu cili cowala. Citani zimenezi kuti “mulandile mphamvu zazikulu mogwilizana ndi mphamvu zake zocititsa mantha, nʼcolinga coti muthe kupilila zinthu zonse moleza mtima ndiponso mwacimwemwe.”—Akol. 1:11. w23.10 17 ¶19-20