Cisanu, August 29
Ine ndacititsa kuti iwo adziŵe dzina lanu.—Yoh. 17:26
Yesu anacita zambili kuposa kungouza anthu kuti dzina la Mulungu ni Yehova. Ayuda omwe Yesu anali kuphunzitsa anali kulidziŵa kale dzina la Mulungu. Koma Yesu anakhala patsogolo ‘kuwafotokozela za Mulungu.’ (Yoh. 1:17, 18) Mwa citsanzo, Malemba a Ciheberi amaonetsa kuti Yehova ni wacifundo, komanso wacisomo. (Eks. 34:5-7) Yesu anafotokoza coonadi cimeneci momveka bwino pomwe anakamba za fanizo la mwana woloŵelela. Bambo wa m’fanizoli ataona mwana wake wolapa “ali capatali ndithu,” anathamangila mwanayo, kumukumbatila na kum’khululukila na mtima wonse. Zimenezi zimatithandiza kumvetsa bwino cifundo ca Yehova na cisomo cake. (Luka 15:11-32) Yesu anathandiza ena kumvetsa kuti Yehova ni Tate wotani kwenikweni. w24.02 10 ¶8-9
Ciŵelu, August 30
[Tonthozani ena] . . . cifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.—2 Akor. 1:4.
Yehova amatsitsimula komanso kutonthoza opsinjika maganizo. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova ca kumvela ena cifundo komanso kuwatonthoza? Njila imodzi imene tingacitile zimenezi ni kukulitsa makhalidwe abwino mu mtima mwathu amene angatithandize kutonthoza ena. Kodi ena mwa makhalidwe amenewa ni ati? N’ciyani cingatithandize kukhalabe na cikondi kuti “tipitilize kutonthozana” tsiku na tsiku? (1 Ates. 4:18)Tiyenela kukhala na makhalidwe monga kumvela ena cisoni, kukonda abale, komanso kukhala okoma mtima. (Akol. 3:12; 1 Pet. 3:8) Kodi makhalidwewa adzatithandiza bwanji? Ngati tipanga cifundo na makhalidwe ena otelo kukhala mbali ya umunthu wathu, sicidzakhala covuta kutonthoza amene akuvutika. Yesu anakamba kuti, “pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’cuma cake cabwino.” (Mat. 12:34, 35) Kutonthoza abale na alongo amene akukumana na zovuta ni njila yaikulu imene timaonetsela kuti timawakonda. w23.11 10 ¶10-11
Sondo, August 31
Anthu ozindikila adzawamvetsetsa.—Dan. 12:10.
Tiyenela kupempha thandizo kuti timvetse maulosi a m’Baibo. Nali fanizo. Yelekezani kuti mwapita ku malo acilendo, koma mnzanu amene mwapita naye amawadziŵa bwino malowo. Akudziŵa bwino pamene muli komanso kumene misewu ikupita. Mosakayika konse, mudzakondwela kwambili kuti mnzanuyo wakupelekezani. Inde, paja amati kuyenda aŵili si mantha! Mofananamo, Yehova akudziŵa bwino pomwe tafika na kumene tikupita. Conco, kuti timvetse maulosi a m’Baibo tiyenela kupempha thandizo la Yehova modzicepetsa. (Dan. 2:28; 2 Pet. 1:19, 20) Molingana na kholo lililonse labwino, Yehova amafuna kuti ana ake akhale na tsogolo lacimwemwe. (Yer. 29:11) Koma mosiyana na makolo aumunthu, Yehova amakambilatu zakutsogolo, ndipo saphonyetsa ngakhale pang’ono. Iye anaikamo maulosi m’Baibo kuti tidziŵiletu pasadakhale zocitika zofunika kwambili.—Yes. 46:10. w23.08 8 ¶3-4