LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Ciŵelu, August 30

[Tonthozani ena] . . . cifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.​—2 Akor. 1:4.

Yehova amatsitsimula komanso kutonthoza opsinjika maganizo. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova ca kumvela ena cifundo komanso kuwatonthoza? Njila imodzi imene tingacitile zimenezi ni kukulitsa makhalidwe abwino mu mtima mwathu amene angatithandize kutonthoza ena. Kodi ena mwa makhalidwe amenewa ni ati? N’ciyani cingatithandize kukhalabe na cikondi kuti “tipitilize kutonthozana” tsiku na tsiku? (1 Ates. 4:18)Tiyenela kukhala na makhalidwe monga kumvela ena cisoni, kukonda abale, komanso kukhala okoma mtima. (Akol. 3:12; 1 Pet. 3:8) Kodi makhalidwewa adzatithandiza bwanji? Ngati tipanga cifundo na makhalidwe ena otelo kukhala mbali ya umunthu wathu, sicidzakhala covuta kutonthoza amene akuvutika. Yesu anakamba kuti, “pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’cuma cake cabwino.” (Mat. 12:34, 35) Kutonthoza abale na alongo amene akukumana na zovuta ni njila yaikulu imene timaonetsela kuti timawakonda. w23.11 10 ¶10-11

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Sondo, August 31

Anthu ozindikila adzawamvetsetsa.​—Dan. 12:10.

Tiyenela kupempha thandizo kuti timvetse maulosi a m’Baibo. Nali fanizo. Yelekezani kuti mwapita ku malo acilendo, koma mnzanu amene mwapita naye amawadziŵa bwino malowo. Akudziŵa bwino pamene muli komanso kumene misewu ikupita. Mosakayika konse, mudzakondwela kwambili kuti mnzanuyo wakupelekezani. Inde, paja amati kuyenda aŵili si mantha! Mofananamo, Yehova akudziŵa bwino pomwe tafika na kumene tikupita. Conco, kuti timvetse maulosi a m’Baibo tiyenela kupempha thandizo la Yehova modzicepetsa. (Dan. 2:28; 2 Pet. 1:19, 20) Molingana na kholo lililonse labwino, Yehova amafuna kuti ana ake akhale na tsogolo lacimwemwe. (Yer. 29:11) Koma mosiyana na makolo aumunthu, Yehova amakambilatu zakutsogolo, ndipo saphonyetsa ngakhale pang’ono. Iye anaikamo maulosi m’Baibo kuti tidziŵiletu pasadakhale zocitika zofunika kwambili.​—Yes. 46:10. w23.08 8 ¶3-4

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Mande, September 1

Kuwala kwa m’mawa kudzatifikila kucokela kumwamba.​—Luka 1:78.

Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zocotsapo mavuto onse a anthu. Mwa zozizwitsa zake, Yesu anaonetsa kuti ali na mphamvu zocotsapo mavuto onse omwe pa ife tokha sitingathe kuwacotsapo. Mwacitsanzo, iye ali na mphamvu zotimasula ku zonse zotibweletsela mavuto​—ucimo, matenda, na imfa. (Mat. 9:1-6; Aroma 5:12, 18, 19) Zozizwitsa zake zinaonetsa kuti angathe kucilitsa “matenda amtundu uliwonse,” ngakhale kuukitsa akufa. (Mat. 4:23; Yoh. 11:43, 44) Cina, ali na mphamvu zolamulila mphepo zoopsa komanso kumasula anthu ku mizimu yoipa. (Maliko 4:37-39; Luka 8:2) N’zolimbikitsa zedi kudziŵa kuti Yehova anapatsa Mwana wake mphamvu zimenezi! Tingakhale na cidalilo conse kuti Ufumu wa Mulungu udzabweletsadi madalitso kutsogoloku. Zozizwitsa zimene Yesu anacita monga munthu padziko lapansi, zitiphunzitsa kuti kutsogoloku adzacita zambili monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. w23.04 3 ¶5-7

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani