LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es25 masa. 88-97
  • September

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • September
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
  • Tumitu
  • Mande, September 1
  • Ciŵili, September 2
  • Citatu, September 3
  • Cinayi, September 4
  • Cisanu, September 5
  • Ciŵelu, September 6
  • Sondo, September 7
  • Mande, September 8
  • Ciŵili, September 9
  • Citatu, September 10
  • Cinayi, September 11
  • Cisanu, September 12
  • Ciŵelu, September 13
  • Sondo, September 14
  • Mande, September 15
  • Ciŵili, September 16
  • Citatu, September 17
  • Cinayi, September 18
  • Cisanu, September 19
  • Ciŵelu, September 20
  • Sondo, September 21
  • Mande, September 22
  • Ciŵili, September 23
  • Citatu, September 24
  • Cinayi, September 25
  • Cisanu, September 26
  • Ciŵelu, September 27
  • Sondo, September 28
  • Mande, September 29
  • Ciŵili, September 30
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
es25 masa. 88-97

September

Mande, September 1

Kuwala kwa m’mawa kudzatifikila kucokela kumwamba.​—Luka 1:78.

Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zocotsapo mavuto onse a anthu. Mwa zozizwitsa zake, Yesu anaonetsa kuti ali na mphamvu zocotsapo mavuto onse omwe pa ife tokha sitingathe kuwacotsapo. Mwacitsanzo, iye ali na mphamvu zotimasula ku zonse zotibweletsela mavuto​—ucimo, matenda, na imfa. (Mat. 9:1-6; Aroma 5:12, 18, 19) Zozizwitsa zake zinaonetsa kuti angathe kucilitsa “matenda amtundu uliwonse,” ngakhale kuukitsa akufa. (Mat. 4:23; Yoh. 11:43, 44) Cina, ali na mphamvu zolamulila mphepo zoopsa komanso kumasula anthu ku mizimu yoipa. (Maliko 4:37-39; Luka 8:2) N’zolimbikitsa zedi kudziŵa kuti Yehova anapatsa Mwana wake mphamvu zimenezi! Tingakhale na cidalilo conse kuti Ufumu wa Mulungu udzabweletsadi madalitso kutsogoloku. Zozizwitsa zimene Yesu anacita monga munthu padziko lapansi, zitiphunzitsa kuti kutsogoloku adzacita zambili monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. w23.04 3 ¶5-7

Ciŵili, September 2

Mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.​—1 Akor. 2:10.

Ngati muli mumpingo waukulu ndipo nthawi zambili mumaona kuti simupatsidwa mwayi wopelekapo ndemanga, mungaganize zongoleka kupelekapo ndemanga. Koma conde musaleke. Muzikonzekela ndemanga zingapo pa msonkhano uliwonse. Ngati sanakupatseni mwayi wopeleka ndemanga kumayambililo kwa msonkhano, mudzakhalabe na mipata ina yopelekapo ndemanga pamene msonkhanowo ukupitiliza. Mukamakonzekela Nsanja ya Mlonda, muziganizila mmene ndime iliyonse ikugwilizanila na mfundo yaikulu ya nkhaniyo. Mukatelo, mudzakhala na ndemanga zabwino zimene mungapeleke pa phunzilo lonselo. Kuwonjezela apo, mungakonzekele kukapeleka ndemanga pa ndime zokamba pa ziphunzitso zozama za m’Baibo zovuta kuzifotokoza. Cifukwa ciyani? Cifukwa ni anthu ocepa angakweze manja kuti apeleke ndemanga. Nanga bwanji ngati pambuyo pa misonkhano ingapo sanakupatsenibe mwayi wopeleka ndemanga? Msonkhano usanayambe, uzani wotsogoza ndime imene mwakonzekela kupeleka ndemanga. w23.04 21-22 ¶9-10

Citatu, September 3

Yosefe . . . [anacita] mogwilizana ndi zimene mngelo wa Yehova anamuuza. Anatenga mkazi wake nʼkupita naye kunyumba.​—Mat. 1:24.

Mofunitsitsa Yosefe anatsatila citsogozo ca Yehova. Mwa ici, anakhala mwamuna wabwino. Katatu konse, Mulungu anam’patsa malangizo okhudza banja lake. Pa nthawi zonsezo, anatsatila malangizowo ngakhale pamene zinali zovuta kutelo. (Mat. 1:20; 2:13-15, 19-21) Cifukwa cotsatila malangizo a Mulungu, Yosefe anateteza Mariya, kum’thandiza, komanso kum’samalila. Izi zinapangitsa Mariya kuti azim’konda Yosefe na kum’lemekeza. Inu amuna, mungatengele citsanzo ca Yosefe mwa kutsatila ulangizi wa m’Baibo posamalila banja lanu. Mukatelo, ngakhale pamene n’zovuta, mumaonetsa kuti mumam’konda mkazi wanu, ndipo mumalimbitsa ukwati wanu. Mlongo wina ku Vanuatu, amene wakhala m’banja zaka zoposa 20 anati: “Mwamuna wanga akamafufuza na kutsatila malangizo a m’Baibo, nimam’lemekeza kwambili. Nimamva kukhala wotetezeka, ndipo sinimakayikila zisankho zake.” w23.05 21 ¶5

Cinayi, September 4

Kumeneko kudzakhala msewu waukulu inde msewu umene udzachedwa Msewu Wopatulika.​—Yes. 35:8.

Ayuda obwelela kwawo anali kudzakhala “anthu oyela” kwa Mulungu wawo. (Deut. 7:6) Komabe, izi sizinatanthauze kuti sanafunike kupanga masinthidwe kuti Yehova awayanje. Ayuda ambili anabadwila ku Babulo, ndipo n’kutheka kuti anatengela maganizo na cikhalidwe ca Ababulo. Patapita zaka zambili Ayuda oyamba atabwelela ku Isiraeli, Bwanamkubwa Nehemiya anadabwa ataona kuti ana obadwila ku Isiraeli sanali kudziŵa cinenelo ca Ayuda. (Deut. 6:6, 7; Neh. 13:23, 24) Popeza mbali yaikulu ya Mawu a Mulungu inali m’Ciheberi, kodi anawo akanaphunzila bwanji kukonda Yehova na kum’lambila? (Ezara 10:3, 44) Conco, Ayudawo anafunika kupanga masinthidwe aakulu. Koma cikanakhala copepuka kwa iwo kucita zimenezo ku Isiraeli komwe kulambila koona kunali kubwezeletsedwa mwapang’ono-pang’ono.​—Neh. 8:8, 9. w23.05 15 ¶6-7

Cisanu, September 5

Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pangʼono kugwa ndipo amadzutsa onse amene aŵelama cifukwa ca mavuto.​—Sal. 145:14.

Ngakhale titakhala na cikhumbo kapena odziletsa, nthawi zina tingalepheleko ndithu. Mwacitsanzo, “zinthu zosayembekezeleka” zingatilande nthawi yokwanilitsa zolinga zathu. (Mlal. 9:11) Tingakumane na vuto lalikulu limene lingatilefule na kutilanda mphamvu. (Miy. 24:10) Ndipo cifukwa ca kupanda ungwilo, tingalakwitse zinazake. Izi zingatilepheletse kukwanilitsa colinga cathu. (Aroma 7:23) Cina, tingafike potopa nazo. (Mat. 26:43) N’ciyani cingatithandize kugonjetsa zobweza kumbuyo zimenezi? Kumbukilani kuti dzedzele-dzedzele si kugwa. Baibo imati tingakumane na mavuto mobweleza-bweleza. Koma imakambanso kuti tinganyamukenso. Inde, mukamayesetsa kukwanilitsa zolinga zanu olo kuti mumalephelako nthawi zina, mumaonetsa Yehova kuti mukufuna kum’kondweletsa. Yehova amakondwela kwambili akakuonani mukuyesetsa kukwanilitsa colinga canu. w23.05 30 ¶14-15

Ciŵelu, September 6

Muzipeleka citsanzo cabwino kwa gulu la nkhosa.​—1 Pet. 5:3.

Upainiya umathandiza wacinyamata kuphunzila kuseŵenza bwino na anthu osiyana-siyana. Umam’thandizanso kupanga bajeti yabwino na kuitsatila. (Afil. 4:11-13) Ciyambi cabwino coyamba utumiki wa nthawi zonse ni kucita upainiya wothandiza umene umawathandiza kuti ayambe upainiya wa nthawi zonse. Upainiya wa nthawi zonse umatsegula mipata ku mautumiki ena a nthawi zonse osiyana-siyana, monga kutumikila m’dipatimenti ya zamamangidwe kapena pa Beteli. Amuna acikhristu ayenela kukhala na colinga cokwanilitsa ziyeneletso kuti atumikile abale na alongo awo mu mpingo monga akulu. Baibo imati amuna amene akuyesetsa kuti akhale oyang’anila “akufuna nchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Coyamba, m’bale afunika kuyenelela kukhala mtumiki wothandiza. Atumiki othandiza amathandiza akulu m’njila zosiyana-siyana. Akulu na atumiki othandiza amatumikila abale na alongo awo modzicepetsa ndipo amalalikila mokangalika. w23.12 28 ¶14-16.

Sondo, September 7

Akadali mnyamata, . . . anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide kholo lake.​—2 Mbiri 34:3.

Mfumu Yosiya anayamba kufuna-funa Yehova ali mnyamata. Anali wofunitsitsa kuphunzila za Yehova na kucita cifunilo cake. Komabe, umoyo sunali wopepuka kwa mfumu yacinyamatayi. Anafunika kulimba mtima kuti abwezeletse kulambila koyela panthawi imene kulambila konyenga kunali kofala. Ndipo anatelodi! Asanakwanitse zaka 20, Yosiya anayamba kucotsa kulambila konyenga m’dzikolo. (2 Mbiri 34:1, 2) Ngakhale kuti ndinu wacicepele kwambili, mungathe kutengela Yosiya mwa kufuna-funa Yehova na kuphunzila za makhalidwe ake. Izi zingakulimbikitseni kupatulila moyo wanu kwa iye. Kodi kudzipatulila kumeneku kudzakhudza bwanji umoyo wanu wa tsiku na tsiku? Pa tsiku limene anali kubatizika, ali na zaka 14, Luke anati, “Kuyambila lelo, nidzaika kutumikila Yehova patsogolo mu umoyo wanga, ndipo nidzayesetsa kumukondweletsa.” (Maliko 12:30) Ngati ni zimene nanunso mufuna kucita, mudzadalitsika kwambili! w23.09 11 ¶12-13

Mande, September 8

Muzilemekeza anthu amene akugwila nchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolelani mwa Ambuye.​—1 Ates. 5:12.

Pamene mtumwi Paulo analemba kalatayi, mpingo wa Atesalonika unali usanakwanitse caka. N’kutheka kuti amuna apaudindo mumpingowo anali acatsopano, ndipo anali kulakwitsa zina. Ngakhale n’telo, anayenela kulemekezedwa. Pamene cisautso cacikulu cikuyandikila, tidzafunika kudalila kwambili citsogozo ca akulu kuposa kale lonse. Nthawi zina sizingatheke kulandila malangizo ocokela ku likulu lathu kapena ku ofesi ya nthambi. Conco, m’pofunika kwambili palipano kuphunzila kuwakonda akulu na kuwalemekeza. Kaya pacitike zotani, tiyeni tikhalebe oganiza bwino, na kupewa kuyang’ana zophophonya zawo. M’malo mwake, tiziika maganizo athu pa mfundo yakuti Yehova kudzela mwa Khristu, akutsogolela amuna okhulupilika amenewa. Monga mmene cisoti cimatetezela mutu wa msilikali, naconso ciyembekezo cathu cacipulumutso cimateteza maganizo athu. Timaona kuti zimene dzikoli limapeleka n’zopanda phindu. (Afil. 3:8) Cimatithandizanso kukhala odekha komanso osasunthika. w23.06 11-12 ¶11-12

Ciŵili, September 9

Mkazi wopusa amakhala wolongolola. Iye ndi wopelewela nzelu.​—Miy. 9:13.

Amene amamva ciitano ca “mkazi wopusa,” amafunika kusankha kaya kulabadila ciitanoco kapena ayi. Tili na zifukwa zomveka zopewela khalidwe laciwelewele. “Mkazi wopusa” akunena kuti: “Madzi akuba amatsekemela.”(Miy. 9:17) Kodi “madzi akuba” n’ciyani? Baibo imayelekezela kugonana pakati pa mwamuna na mkazi wake na madzi otsitsimula. (Miy. 5:15-18) Kugonana kumasangalatsa ngati kucitika pakati pa mwamuna na mkazi okwatilana mwalamulo. Komabe, izi n’zosiyana kutalitali na “madzi akuba,” omwe angatanthauze ciwelewele. Nthawi zambili, ciwelewele cimacitika usiku, monga mbala imene kambili imaba usiku. “Madzi akuba” angaoneke otsekemela maka-maka ngati ocita ciwelewele cimeneco amaona kuti palibe adzadziŵa. Ati kudzinamiza kwake ŵati! Yehova amaona zonse. Ndipo palibe coŵaŵa kwambili kuposa kutaya ciyanjo cake. Conco, palibenso ‘cotsekemela’ ngakhale pang’ono.​—1 Akor. 6:9, 10. w23.06 22 ¶7-9

Citatu, September 10

Ngakhale nditacita mokakamizika, ndinebe woyangʼanila mogwilizana ndi udindo umene ndinapatsidwa.​—1 Akor. 9:17.

Nanga bwanji ngati mwaona kuti mapemphelo anu komanso utumiki wanu zikungocitika mwa mwambo cabe? Ngati zaconco zakucitikilani pambuyo pa ubatizo, musaganize kuti basi mzimu wa Yehova wakucokelani. Ndinu wopanda ungwilo, ndipo nthawi zina mungamamve conco. Ngati cangu canu cayamba kucepa, muzisinkhasinkha citsanzo ca mtumwi Paulo. Ngakhale kuti anali kuyesetsa kutengela citsanzo ca Yesu, iye anadziŵa kuti nthawi zina sangakhale na cikhumbo cofuna kucita zimenezo. Paulo anali wotsimikiza mtima kukwanilitsa utumiki wake mosasamala kanthu za mmene anali kumvela pa nthawiyo. Mofananamo, musadalile maganizo anu opanda ungwilo popanga zisankho. Khalani otsimikiza kucita zoyenela mosasamala kanthu za mmene mukumvela.​—1 Akor. 9:16. w24.03 11-12 ¶12-13

Cinayi, September 11

Asonyezeni kuti mumawakonda.​—2 Akor. 8:24.

Tingawaonetse cikondi abale na alongo athu pokhala nawo pa ubwenzi. (2 Akor. 6:11-13) Ambili tili m’mipingo muli abale na alongo a zikhalidwe zosiyana-siyana, komanso zibadwa zosiyana-siyana. Tingakulitse cikondi cathu kwa onsewo mwa kuyang’ana kwambili pa makhalidwe awo abwino. Tikamaona ena mmene Yehova amawaonela, timaonetsa kuti timawakonda. Pa cisautso cacikulu, cikondi cidzakhala cofunika kwambili. Kodi n’kuti kumene tidzapeza citetezo cisautsoco cikadzayamba? Onani malangizo amene Yehova anauza atumiki ake Babulo wakale ataukilidwa. Iye anawauza kuti: “Inu anthu anga, pitani mukaloŵe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Zioneka kuti malangizo amenewa adzagwilanso nchito kwa ife pa cisautso cacikulu. w23.07 6-7 ¶14-16

Cisanu, September 12

Zocitika zapadzikoli zikusintha.​—1 Akor. 7:31.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu amanidziŵa kuti ndine munthu wololela? Kapena amanidziŵa kuti ndine woumitsa zinthu, wokhwimitsa zinthu, kapena wa zimene ndanena-ndanena? Kodi nimamvako za ena na kulolela kuti zinthu zicitike mmene iwo afunila ngati n’kotheka?’ Tikamaonetsa kwambili kulolela, timaonetsanso kuti tikutengela kwambili Yehova na Yesu. Munthu wololela amakhala wokonzeka kusintha pamene mikhalidwe yasintha. Zinthu zikasintha, tingakumane na mavuto amene sitinawayembekezele. Mwacitsanzo, tingadwale mwadzidzidzi. Mwina kusintha mosayembekezela kwa zacuma kapena zandale, kungapangitse umoyo wathu kukhala wovuta kwadzaoneni. (Mlal. 9:11) Ngakhale kusinthidwa pa udindo, utumiki, kapena malo otumikilako kungatiike pa mayeso. Tikhoza kusintha mogwilizana na mikhalidwe yathu yatsopano ngati tatsatila masitepe anayi otsatilawa: (1) civomelezeni kuti zinthu zasintha, (2) yang’anani kutsogolo, (3) muziika maganizo anu pa zinthu zolimbikitsa, komanso (4) muzithandiza ena. w23.07 21-22 ¶7-8

Ciŵelu, September 13

Ndiwe munthu wokondedwa kwambili.​—Dan. 9:23.

Mneneli Danieli anali wacinyamata pamene Ababulo anam’tengela kutali na kwawo monga mkaidi. Koma Ababulowo anacita naye cidwi Danieli. Iwo anaona kuti iye ‘analibe cilema ciliconse, anali wooneka bwino,’ komanso kuti anacokela m’banja lolemekezeka. (1 Sam. 16:7) Pa zifukwa zimenezi, Ababulowo anam’phunzitsa kuti akatumikile m’nyumba yacifumu. (Dan. 1:3, 4, 6) Yehova anali kum’konda Danieli, cifukwa ca khalidwe lake labwino. Ndipo Danieli ayenela kuti anali na zaka za m’ma 20 pamene Yehova anam’chula kuti wolungama pamodzi na Nowa komanso Yobu​—amuna amene anapanga mbili yabwino na Mulungu kwa zaka zambili. (Gen. 5:32; 6:9, 10; Yobu 42:16, 17; Ezek. 14:14) Yehova sanaleke kum’konda Danieli pa umoyo wake wonse.​—Dan. 10:11, 19. w23.08 2 ¶1-2

Sondo, September 14

Muthe kumvetsa bwino m’lifupi ndi m’litali, kukwela ndi kuzama kwa coonadi.​—Aef. 3:18.

Mukafuna kugula nyumba mungafune kudzionela nokha nyumbayo, kuizungulila na kuona milingo yake yonse. Tiyenela kucita cimodzi-modzi poŵelenga na kuphunzila Baibo. Mukamaŵelenga mothamanga, mungadziŵe mfundo zocepa cabe​—“mfundo zoyambilila za m’mawu opatulika a Mulungu.” (Aheb. 5:12) M’malo mwake, monga mmene mungacitile na nyumba, “fufuzani” kuti mumvetse mfundo zamtengo wapatali. Njila yabwino koposa yoŵelengela mawu a Mulungu ni kuyesa kuona mmene mfundo zosiyana-siyana zikugwilizanila. Muziyesetsa kumvetsa zimene mumakhulupilila komanso cifukwa cake mumazikhulupilila. Kuti timvetse Mawu a Mulungu, tiyenela kuŵelenga mfundo zozama za coonadi. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti ayenela kuŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama ‘kuti athe kudziŵa bwino m’lifupi ndi m’litali ndi kukwela ndi kuzama’ kwa coonadi. Kucita zimenezi kunawathandiza ‘kuti azike mizu mokhazikika’ pa cikhulupililo. (Aef. 3:14-19) Ifenso tiyenela kucita cimodzi-modzi. w23.10 18 ¶1-3

Mande, September 15

Abale, pa nkhani ya kumva zowawa ndi kuleza mtima, tengelani citsanzo ca aneneli amene analankhula mʼdzina la Yehova.​—Yak. 5:10.

M’Baibo, muli zitsanzo zambili za anthu amene anali oleza mtima. Conco, mungadziikile colinga coŵelenga zitsanzo zimenezo pa phunzilo la inu mwini. Mwacitsanzo, ngakhale kuti Davide anadzozedwa akali wacicepele kukhala mfumu yam’tsogolo ya Isiraeli, anayembekezela kwa zaka zambili kuti ayambe kulamulila. Nayenso Simiyoni komanso Anna anatumikila Yehova mokhulupilika poyembekezela Mesiya wolonjezedwayo. (Luka 2:25, 36-38) Mukamaŵelenga nkhani ngati zimenezi, muziyesa kupeza mayankho pa mafunso awa: N’ciyani cinathandiza munthu ameneyu kukhala woleza mtima? Kodi kuleza mtima kunam’pindulila motani? Nanga ningatengele bwanji citsanzo cake? Tingatengenso cenjezo pa zitsanzo za anthu amene sanali oleza mtima. (1 Sam. 13:8-14) Mungadzifunse kuti: ‘N’ciyani cinapangitsa kuti asakhale oleza mtima? Nanga anakumana na mavuto otani?’ w23.08 25 ¶15

Ciŵili, September 16

Ife takhulupilila ndipo tadziŵa kuti inu ndinu Woyela amene Mulungu anamutumiza.​—Yoh. 6:69.

Mtumwi Petulo anali wokhulupilika, ndipo sanalole ciliconse kumulepheletsa kutsatila Yesu. Pa nthawi ina, anaonetsa kukhulupilika kwake pamene Yesu anakamba zinthu zimene ophunzila ake sanadzimvetse. (Yoh. 6:68) M’malo mopempha Yesu kuti awafotokozele tanthauzo lake, anthu ambili analeka kum’tsatila. Koma Petulo sanatelo. Iye anazindikila kuti Yesu yekhayo ndiye ali na “mawu amoyo wosatha.” Yesu anadziŵa kuti Petulo na atumwi ena adzam’thaŵa. Ngakhale n’telo, anali na cidalilo mwa Petulo cakuti iye adzabwelela na kukhalabe wokhulupilika. (Luka 22:31, 32) Yesu anamvetsa kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Maliko 14:38) Ngakhale kuti Petulo anam’kana, Yesu sanam’taye mtumwi wake ameneyu. Ndipo iye ataukitsidwa, anaonekela kwa Petulo, amene mwacionekele anali yekha. (Maliko 16:7; Luka 24:34; 1 Akor. 15:5) Tangoganizilani mmene zinam’limbikitsila mtumwi wacisoniyo! w23.09 22 ¶9-10

Citatu, September 17

Osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zocita zawo zosamvela malamulo ndipo macimo awo akhululukidwa.​—Aroma 4:7.

Mulungu amakhululuka, kapena kuti kuphimba macimo, a anthu oika cikhulupililo cawo mwa iye. Amawakhululukila kothelatu, ndipo sawapatsa cilango kaamba ka macimo amenewo. (Sal. 32:1, 2) Amaona anthu amenewo kukhala osalakwa komanso olungama cifukwa ca cikhulupililo cawo. Ngakhale kuti Abulahamu, Davide, komanso alambili ena a Mulungu okhulupilika anaonedwa olungama, iwo anali ocimwabe. Koma cifukwa ca cikhulupililo cawo, Mulungu anawaona kukhala osalakwa, maka-maka powayelekezela na anthu ena omwe sanali kumulambila. (Aef. 2:12) Mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino m’kalata yake kuti cikhulupililo n’cofunika kuti munthu akhale paubwenzi na Mulungu. Umu ni mmene zinalili kwa Abulahamu na Davide, ndipo n’cimodzi-modzinso kwa ife. w23.12 3 ¶6-7

Cinayi, September 18

Nthawi zonse tizitamanda Mulungu kudzela mwa Yesu. Kucita zimenezi kuli ngati nsembe imene tikupeleka kwa Mulungu ndipo timagwilitsa nchito milomo yathu polengeza dzina lake.​—Aheb. 13:15.

Masiku ano Akhristu onse ali na mwayi wopeleka nsembe kwa Yehova mwa kuseŵenzetsa nthawi yawo, mphamvu zawo, komanso cuma cawo, popititsa patsogolo ucifumu wa Mulungu. Tingaonetse kuti timayamikila mwayi wathu wolambila Yehova mwa kum’patsa nsembe zabwino koposa. Mtumwi Paulo, anachula zinthu zina zimene sitifunika kunyalanyaza pa kulambila kwathu. (Aheb. 10:22-25) Zimenezi ziphatikizapo kumufikila Yehova m’pemphelo, kulengeza poyela ciyembekezo cathu, kusonkhana pamodzi monga mpingo, komanso kulimbikitsana ‘makamaka pamene tikuona kuti tsiku la [Yehova] likuyandikila.’ Cakumapeto kwa buku la Chivumbulutso, mngelo wa Yehova anachula mawu akuti: “Lambilani Mulungu” kaŵili konse pofuna kuwagogomezela! (Chiv. 19:10; 22:9) Tiyeni ticite zonse zotheka kuti tisaiŵale mfundo yozama ya coonadi yonena za kacisi wauzimu wa Yehova, komanso mwayi wamtengo wapatali umene tili nawo wolambila Mulungu wathu wamkulu! w23.10 29 ¶17-18

Cisanu, September 19

[Pitilizani] kukondana.​—1 Yoh. 4:7.

Tonse timafuna kuti “tipitilize kukondana.” Komabe, m’pofunika kwambili kukumbukila cenjezo la Yesu lakuti “cikondi ca anthu ambili cidzazilala.” (Mat. 24:12) Yesu sanatanthauze kuti izi zidzacitika pa mlingo waukulu pakati pa ophunzila ake. Ngakhale n’telo, tiyenela kukhala osamala kuti tisasoceletsedwe na kupanda cikondi kwa m’dzikoli. Tili na mfundo imeneyi m’maganizo, tiyeni tione funso lofunika kwambili ili: Kodi pali njila imene tingadziŵile ngati cikondi cathu pa abale cikali colimba? Njila imodzi imene tingadziŵile ngati cikondi cathu cikali colimba, ni kuona mmene timasamalila zocitika zina mu umoyo wathu. (2 Akor. 8:8) Cocitika cimodzi cinachulidwa na mtumwi Petulo. Iye anati: “Koposa zonse, khalani okondana kwambili, pakuti cikondi cimakwilila macimo oculuka.” (1 Pet. 4:8) Conco, zifooko komanso kupanda ungwilo kwa ena zingatithandize kudziŵa ngati cikondi cathu pa iwo cikali colimba. w23.11 10-11 ¶12-13

Ciŵelu, September 20

Muzikondana.​—Yoh. 13:34.

Sitingamvele lamulo la Yesu lakuti tizikondana ngati timakonda ena mu mpingo na kupewa kukonda ena. Monga mmene zinalili kwa Yesu, nafenso sitingakhale omasuka kwa onse. (Yoh. 13:23; 20:2) Koma mtumwi Petulo akutikumbutsa kuti tiyenela kuyesetsa ‘kukonda gulu lonse la abale,’ cifukwa ni mbali ya banja lathu. (1 Pet. 2:17) Petulo anatilimbikitsa kuti tiyenela ‘kukondana kwambili kucokela mu mtima.’ (1 Pet. 1:22) Palembali, mawu akuti kukonda “kwambili” aphatikizapo kuonetsa cikondi kwa munthu wina ngakhale kuti zingakhale zovuta kucita zimenezo. Mwacitsanzo, ngati m’bale watikhumudwitsa m’njila ina yake, mwacibadwa tingafune kubwezela m’malo moonetsa cikondi. Komabe, Petulo anaphunzila kuti kubwezela sikukondweletsa Mulungu. (Yoh. 18:10, 11) Petulo analemba kuti: “Osabwezela coipa pa coipa kapena cipongwe pa cipongwe, koma m’malomwake muzidalitsa.” (1 Pet. 3:9) Lolani cikondi kukusonkhezelani kukhala okoma mtima komanso oganizila ena. w23.09 28-29 ¶9-11

Sondo, September 21

Nawonso akazi akhale . . . ocita zinthu mosapitilila malile, okhulupilika m’zinthu zonse.​—1 Tim. 3:11.

Timacita cidwi kuona mmene mwana amakulila mwamsanga kukhala wamkulu. Kukula kumeneku kumacitika pakokha. Komabe, kukhala Mkhristu wokhwima sikucitika pakokha. (1 Akor. 13:11; Aheb. 6:1) Kuti tikwanilitse colinga cimeneci, tiyenela kukhala paubwenzi wa thithithi na Yehova. Tifunikilanso mzimu wake woyela pokulitsa makhalidwe aumulungu, kukulitsa maluso othandiza komanso kukonzekela maudindo a m’tsogolo. (Miy. 1:5) Yehova ndiye analenga amuna na akazi. (Gen. 1:27) N’zoonekelatu kuti amuna na akazi amasiyana m’maonekedwe. Ndipo amasiyananso m’njila zina. Mwacitsanzo, Yehova analenga amuna na akazi kuti azigwila nchito zosiyana. Conco, onse ayenela kukhala na makhalidwe komanso maluso amene angawathandize kukwanilitsa maudindo awo.​—Gen. 2:18. w23.12 18 ¶1-2

Mande, September 22

Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza mʼdzina la Atate, ndi la Mwana.​—Mat. 28:19.

Mosakayikila, Yesu anafuna kuti ena aziseŵenzetsa dzina lenileni la Atate wake. Atsogoleli ena a cipembedzo a m’nthawi imeneyo anali kunena kuti dzina la Mulungu ni lolemekezeka kwambili moti siliyenela kuchulidwa. Koma Yesu sanalole kuti miyambo yosazikika m’Malemba imeneyo imulepheletse kulemekeza dzina la Atate wake. Ganizilani zimene zinacitika atacilitsa munthu wogwidwa na ziŵanda m’cigawo ca Agerasa. Anthu anacita mantha kwambili, ndipo anacondelela Yesu kuti acoke. Conco, iye sanakhalitse m’cigawo cimeneco. (Maliko 5:16, 17) Ngakhale n’telo, iye anafunabe kuti anthu adziŵe dzina la Yehova m’cigawo cimeneci. Conco, anauza wocilitsidwayo kuti aziuza anthu zimene Yehova anam’citila, osati zimene Yesu anacita. (Maliko 5:19) N’zimenenso amafuna masiku ano​—kuti tidziŵikitse dzina la Atate ake pa dziko lonse lapansi! (Mat. 24:14; 28:20) Tikacita zimenezi, timakondweletsa Mfumu yathu, Yesu. w24.02 10 ¶10

Ciŵili, September 23

Walimbana ndi mavuto osiyanasiyana cifukwa ca dzina langa.​—Chiv. 2:3.

Ndife odalitsika cotani nanga kukhala m’gulu la Yehova pa nthawi ino yovuta ya masiku otsiliza! Pomwe mavuto a m’dzikoli akuwonjezeleka, Yehova watipatsa banja lauzimu la abale na alongo ogwilizana. (Sal. 133:1) Amatithandiza kukhala na mabanja ogwilizana. (Aef. 5:33–6:1) Amatipatsanso nzelu na kuzindikila kuti tikhale na mtendele wa mumtima. Komabe, tiyenela kulimbikila kuti tipitilize kutumikila Yehova mokhulupilika. Cifukwa ciyani? Cifukwa nthawi zina tingakhumudwe na zophophonya za ena. Cina, tingakhumudwe na zophophonya zathu, maka-maka ngati talakwitsa cina cake mobweleza-bweleza. Komabe, tiyenela kulimbikilabe kutumikila Yehova (1) ngati Mkhristu mnzathu watikhumudwitsa, (2) ngati tagwilitsidwa mwala mu ukwati wathu, komanso (3) ngati takhumudwa na zophophonya zathu. w24.03 14 ¶1-2

Citatu, September 24

Mulimonse mmene tapitila patsogolo, tiyeni tipitilize kupita patsogolo pocita zomwe tikucitazo.​—Afil. 3:16.

Nthawi na nthawi, mumamva zocitika za abale na alongo amene adzipeleka kuti awonjezele utumiki wawo wopatulika. Mwina analoŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu, kapena anasamukila ku malo osoŵa. Ngati mungathe kudziikila zolinga ngati zimenezi, teloni. Anthu a Yehova ni ofunitsitsa kuwonjezela utumiki wawo. (Mac. 16:9) Nanga bwanji ngati pali pano simungakwanitse kucita zimenezi? Musamadzione kuti ndinu wolephela podziyelekezela na amene angakwanitse. Cofunika kwambili kwa Akhristu ni kupitilizabe kutumikila mokhulupilika. (Mat. 10:22) Musaiŵale kuti Yehova amakondwela ngako ngati mum’patsa zonse zimene mungathe malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wanu. Iyi ndiyo njila yabwino kwambili imene mungapitilizile kutsatila Yesu pambuyo pa ubatizo wanu.​—Sal. 26:1. w24.03 10 ¶11

Cinayi, September 25

Mokoma mtima anatikhululukila macimo athu onse.​—Akol. 2:13.

Atate wathu wa kumwamba analonjeza kutikhululukila macimo athu tikalapa. (Sal. 86:5) Conco ngati talapa macimo athu, tizikhulupilila mawu ake, na kukhala otsimikiza kuti watikhululukila. Kumbukilani kuti Yehova si wokhwimitsa zinthu. Satiyembekezela kucita zoculuka kuposa zimene tingakwanitse. Amayamikila zilizonse zimene timam’patsa, malinga n’zimene tingakwanitse. Komanso, muziganizila zitsanzo za anthu ochulidwa m’Baibo amene anatumikila Yehova na mtima wawo wonse. Ganizilani za Mtumwi Paulo. Iye anatumikila mokangalika kwa zaka, anayenda mitunda itali-itali, ndipo anakhazikitsa mipingo. Koma zinthu zinasintha pa umoyo wake, ndipo sanathenso kulalikila monga kale. Kodi Mulungu analeka kukondwela naye? Ayi. Iye anapitiliza kucita zonse zimene akanatha, ndipo Yehova anamudalitsa. (Mac. 28:30, 31) Mofananamo, zimene timapatsa Yehova sizingafanane nthawi zonse. Nthawi zina zingaculuke, nthawi zina zingacepe. Koma cofunika kwambili kwa iye, ni cimene timacitila zimenezo. w24.03 27 ¶7, 9

Cisanu, September 26

Mʼmawa kwambili kudakali mdima, [Yesu] anapita kumalo kopanda anthu. Kumeneko anayamba kupemphela.​—Maliko 1:35.

Mwa mapemphelo ake kwa Yehova, Yesu anapeleka citsanzo kwa ophunzila ake. Pa utumiki wake wonse, iye anali kupemphela kaŵili-kaŵili. Kambili, anali kukhala pakati pa anthu, ndipo anali kukhala wotangwanika. Conco anali kucita kupatula nthawi yoti apemphele. (Maliko 6:31, 45, 46) Iye anali kuuka m’mamaŵa kuti akhale na nthawi yopemphela payekha. Panthawi ina, anapemphela usiku wonse kuti apange cisankho cofunika kwambili. (Luka 6:12, 13) Panthawi inanso, Yesu anaika maganizo ake pa kukwanilitsa mbali yovuta ya utumiki wake wa padziko lapansi. Conco anapemphela mobweleza-bweleza usiku woti maŵa lake aphedwa. (Mat. 26:39, 42, 44) Citsanzo ca Yesu citiphunzitsa kuti ngakhale titangwanike bwanji, tiyenela kupatula nthawi yopemphela. Monga Yesu, tingafunike kucita kuipatula nthawi yopemphela. Mwina tingafunike kuuka m’mawa kwambili, kapena kugona mocedwako usiku kuti tipemphele. Tikatelo, timaonetsa Yehova kuti timayamikila mphatso yapadela imeneyi. w23.05 3 ¶4-5

Ciŵelu, September 27

Mulungu wadzaza cikondi cake m’mitima yathu kudzela mwa mzimu woyela umene tinapatsidwa.​—Aroma 5:5, bi12-CN.

Onani mawu akuti ‘Mulungu wadzaza mitima yawo na cikondi cake’ mu lemba la lelo. Buku lina lofotokozela Baibo linanena kuti cikondi ca Mulungu “cili monga mtsinje wa madzi.” Mawu amenewa aonetsa kuculuka kwa cikondi cimene Yehova ali naco pa odzozedwa! Ndipo odzozedwa amadziŵa kuti ni “okondedwa ndi Mulungu.” (Yuda 1) Mtumwi Yohane anafotokoza mmene iwo amamvela pomwe analemba kuti: “Taganizilani za cikondi cacikulu cimene Atate watisonyeza. Watichula kuti ndife ana a Mulungu!” (1 Yoh. 3:1) Kodi ni Akhristu odzozedwa okha amene amakondedwa na Yehova? Ayi, Yehova waonetsa cikondi cake kwa tonsefe. Kodi n’ciyani cimatsimikizila kuti Yehova amatikondadi? Ni dipo. Ndiwo mcitidwe woonetsa cikondi copambana m’cilengedwe conse!​—Yoh. 3:16; Aroma 5:8. w24.01 28 ¶9-10

Sondo, September 28

Pa tsiku limene ndidzapemphe kuti mundithandize, adani anga adzathawa. Mulungu ali kumbali yanga. Sindikukaikila zimenezi.​—Sal. 56:9.

Vesi lili pamwambali lionetsa njila imene Davide anagonjetsela mantha ake. Ngakhale kuti moyo wa Davide unali pa ciopsezo, iye anali kusinkhasinkha pa zinthu zimene Yehova anali kudzamucitila. Anali kudziŵa kuti Yehova adzamupulumutsa pa nthawi yoyenela. Ndi iko komwe, Yehova anali atanena kuti Davide adzakhala mfumu yotsatila ya Isiraeli. (1 Sam. 16:1, 13) Kwa Davide, zimene Yehova analonjeza zinali ngati zakwanilitsika kale. Kodi Yehova walonjeza kuti adzakucitilani ciyani? Sitiyembekezela Yehova kutiikila chinga ku mavuto onse. Ngakhale n’telo, mavuto alionse omwe amatigwela pali pano, Yehova adzawathetsa m’dziko latsopano likubwelalo. (Yes. 25:7-9) Ndife otsimikiza kuti Mlengi wathu ali nazo mphamvu zoukitsa akufa, kuticilitsa, komanso kucotsa anthu onse otsutsa.​—1 Yoh. 4:4. w24.01 6 ¶12-13

Mande, September 29

Wosangalala ndi munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene macimo ake akhululukidwa.​—Sal. 32:1.

Ganizilani cifukwa cake munadzipatulila na kubatizika. Munatenga masitepe amenewa pofuna kukhala kumbali ya Yehova. Kumbukilani cimene cinakukhutilitsani kuti mwapeza coonadi. Munaphunzila coonadi ponena za Yehova, ndipo munayamba kukonda Atate wanu wakumwamba, na kum’lemekeza. Cina, munakhala na cikhulupililo ndipo cinakusonkhezelani kulapa. Kenako, munaleka makhalidwe oipa, n’kuyamba kucita zinthu zokondweletsa Mulungu. Mtima wanu unakhala m’malo mutazindikila kuti Mulungu wakukhululukilani. (Sal. 32:2) Kuwonjezela apo, munayamba kupezeka pa misonkhano yacikhristu, na kuuzako ena zinthu zosangalatsa zimene munali kuphunzila. Tsopano monga Mkhristu wobatizika, mukuyenda pa msewu wopita kumoyo, ndipo ndinu wofunitsitsa kuyendabe pa msewuwo. (Mat. 7:13, 14) Khalanibe olimba, pa kudzipeleka kwanu kwa Yehova komanso osasunthika pomvela malamulo ake. w23.07 17 ¶14; 19 ¶19

Ciŵili, September 30

Mulungu ndi wokhulupilika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile, koma pamene mukukumana ndi mayeselowo iye adzapeleka njila yopulumukila kuti muthe kuwapilila.​—1 Akor. 10:13.

Kusinkhasinkha pemphelo limene munapeleka podzipatulila kwa Yehova, kudzakuthandizani kugonjetsa mayeselo alionse amene mungakumane nawo. Mwacitsanzo, kodi mungayambe kuceza mokopana na mkazi wa mwini kapena mwamuna wa mwini? M’pang’ono pomwe! Cifukwa munasankhilatu kuti simungacite za mtundu umenewu. Ngati simulola zilakolako zoipa kuzika mizu mwa inu, simudzafunika kulimbana nazo mtsogolo. Ndipo mudzapewa kuyenda “panjila yoipa.” (Miy. 4:14, 15) Kuganizila citsanzo ca Yesu kungakuthandizeni. Iye anali wofunitsitsa kukondweletsa Atate ake. Nanunso muyenela kukana nthawi yomweyo komanso mosasunthika ciliconse cimene cingakhumudwitse Mulungu amene munadzipatulila kwa Iye. (Mat. 4:10; Yoh. 8:29) Kwenikweni, mayeso na mayeselo amakupatsani mpata woonetsa kuti ndinu wofunitsitsa kum’tsatilabe Yesu. Mwa kutelo, dziŵani kuti Yehova adzakuthandizani. w24.03 9-10 ¶8-10

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani