August
Cisanu, August 1
Mavuto a munthu wolungama ndi ambili, koma Yehova amamupulumutsa ku mavuto onsewo.—Sal. 34:19.
Onani mfundo ziŵili izi zimene zili pa salimo lili pamwambapa: (1) Anthu olungama amakumana na mavuto. (2) Yehova amatipulumutsa ku mavutowo. Kodi amatipulumutsa bwanji? Njila imodzi ni kutithandiza kuona umoyo moyenela m’dzikoli. N’zoona kuti Yehova anatilonjeza kuti tidzakhala acimwemwe pom’tumikila. Koma sanatiuze kuti palipano tidzakhala na umoyo wopanda mavuto. (Yes. 66:14) Iye amatilimbikitsa kuganizila za tsogolo lathu, pamene tidzasangalala na moyo kwamuyaya. (2 Akor. 4:16-18) Koma pakali pano, iye amatithandiza kuti tisaleke kum’tumikila. (Maliro 3:22-24) Tiphunzilapo ciyani pa zitsanzo za alambili a Yehova okhulupilika ochulidwa m’Baibo, komanso amakono? Tingakumane na mavuto mosayembekezela. Koma tikam’dalila Yehova, sadzalephela kutithandiza.—Sal. 55:22. w23.04 14-15 ¶3-4
Ciŵelu, August 2
[Muzimvela] olamulila akulu-akulu.—Aroma 13:1.
Tingatengele citsanzo ca Yosefe na Mariya amene anali okonzeka kumvela olamulila ngakhale pamene cinali covuta kutelo. (Luka 2:1-6) Mariya atatsala pang’ono kubeleka, boma linapeleka lamulo limene likanapangitsa kuti zikhale zovuta kwa iye na Yosefe kulitsatila. Bwanamkubwa waciroma, dzina Augusito, analamula kuti nzika zonse za ufumuwo zipite ku mizinda yakwawo kukalembetsa m’kaundula. Yosefe na Mariya anafunika kupita ku Betelehemu, ulendo wodutsa m’mapili wa makilomita 150. Ulendowu unali wosautsa maka-maka kwa Mariya. N’kutheka kuti iwo analinso kudela nkhawa za umoyo wa Mariya komanso za mwana wosabadwayo. Mwina iwo anadzifunsa kuti, bwanji ngati nthawi yobeleka yakwana pamene tikali paulendowu? Nkhawa yawo inali yomveka cifukwa mwana wobadwayo anali kudzakhala Mesiya wolonjezedwa na Yehova. Kodi zifukwa zimenezi zinawacititsa kuti asamvele lamulo la boma? Yosefe na Mariya sanalole kuti zimenezo ziwalepheletse kutsatila lamulo la boma. Yehova anawadalitsa cifukwa ca kumvela kwawo. Mariya anafika bwino ku Betelehemu, anabeleka mwana wathanzi, ndipo anathandiza kukwanilitsa ulosi wa m’Baibo.—Mika 5:2. w23.10 8 ¶9; 9 ¶11-12
Sondo, August 3
Tiyeni tilimbikitsane.—Aheb. 10:25.
Koma bwanji ngati mumacita mantha kupelekapo ndemanga pa misonkhano? Mungapindule kwambili mukamakonzekela bwino. (Miy. 21:5) Mukaimvetsa bwino nkhani imene mudzaphunzila, cidzakhala cosavuta kukapelekapo ndemanga pamsonkhano. Cina, mayankho anu azikhala aafupi. (Miy. 15:23; 17:27) Yankho lanu likakhala lalifupi simudzadodoma kwambili. Mukapeleka ndemanga yaifupi m’mawu anu-anu, zidzaonetsa kuti munakonzekela bwino, komanso kuti munaimvetsa bwino nkhaniyo. Bwanji ngati mwayesa kutsatila malingalilo amenewa, koma mukucitabe mantha kupelekapo ndemanga kaŵili kapena kuposapo? Dziŵani kuti Yehova amayamikila kwambili kuyesetsa kwanu. (Luka 21:1-4) Iye satipempha kucita zimene sitingakwanitse. (Afil. 4:5) Conco, dziŵani zimene mungathe kucita, dziikileni colinga cocita zimenezo, ndipo pemphelani kuti mukhale wodekha. Colingaco cingakhale kukapeleka ndemanga imodzi yaifupi. w23.04 21 ¶6-8
Mande, August 4
Tivale codzitetezela pacifuwa . . . [komanso] . . . cipewa.—1 Ates. 5:8.
Mtumwi Paulo anatiyelekezela na asilikali amene ali chelu komanso okonzeka kumenya nkhondo. Msilikali amene ali pa nchito amakhala wokonzeka nthawi iliyonse kumenya nkhondo. Nafenso n’cimodzimodzi. Timakhalabe okonzekela tsiku la Yehova mwa kuvala codzitetezela pacifuwa cacikhulupililo na cikondi, komanso cisoti cimene n’ciyembekezo. Codzitetezela pacifuwa cinali kuteteza mtima wa msilikali. Mofananamo, cikhulupililo na cikondi zimateteza mtima wathu wophiphilitsa. Zimatithandiza kupitiliza kutumikila Mulungu na kutsatila Yesu. Cikhulupililo cimatitsimikizila kuti Yehova amapeleka mphoto kwa anthu omufuna-funa na mtima wonse. (Aheb. 11:6) Ndipo cimatilimbikitsa kukhalabe okhulupilika kwa Mtsogoleli wathu Yesu, ngakhale tikumane na mavuto. Cikhulupililo cathu cimeneco tingacilimbitse mwa kuphunzila ku zitsanzo zamakono za anthu amene akhalabe okhulupilika, mosasamala kanthu za mazunzo kapena mavuto azacuma. Ndipo tingapewe msampha wokonda zinthu zakuthupi mwa kutengela aja amene anasankha kukhala umoyo wosalila zambili kuti aike zinthu za Ufumu patsogolo. w23.06 10 ¶8-9
Ciŵili, August 5
Amene amayangʼana mitambo sadzakolola.—Mlal. 11:4.
Kudziletsa ni khalidwe limene limathandiza munthu kupewa kucita zoipa, kapena kudzigwila. Kudziletsa n’kofunikanso kuti tikwanilitse zolinga zathu, maka-maka ngati cilingaco n’covuta kapena ngati tilibe cikhumbo cofuna kukwalitsa colingaco. Kumbukilani kuti kudziletsa ni cipatso ca mzimu. Conco, pemphani mzimu woyela kwa Yehova kuti ukuthandizeni kukulitsa khalidwe lofunika limeneli. (Luka 11:13; Agal. 5:22, 23) Musayembekezele kuti mpaka zinthu zikakhale bwino. M’dziko lino, n’zosatheka kukhala na umoyo wopanda mavuto. Tikayembekezela kuti mpaka zinthu zikhale bwino, sitingakwanilitse colinga cathu. Ngati colinga cathu cikuoneka kuti n’covuta kucikwanilitsa, cingatithyole m’nkhongono. Ngati ni mmene zilili kwa inu, bwanji colinga canuco osacigaŵa m’zolinga zing’ono-zing’ono? Mwacitsanzo, ngati colinga canu ni kukulitsa khalidwe lina lake, bwanji osayamba kuonetsa khalidwelo m’njila zing’ono-zing’ono? Ngati colinga canu ni kuŵelenga Baibo yonse, bwanji osayamba mwa kuŵelengako mavesi ocepa? w23.05 29 ¶11-13
Citatu, August 6
Njila ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kwa mʼmawa kumene kumawonjezeleka mpaka kunja kutawala kwambili.—Miy. 4:18.
M’masiku otsiliza ano, Yehova akuseŵenzetsa gulu lake popeleka cakudya cauzimu ca mwana alilenji, kuti tonsefe tisaleke kuyenda pa “Msewu wa Ciyelo.” (Yes. 35:8; 48:17; 60:17) Munthu akavomela kuphunzila Baibo, amakhala na mwayi woyenda pa “Msewu wa Ciyelo.” Ena amaleka kuyenda pa msewuwo. Koma ena amakhala ofunitsitsa kuyendabe pa msewuwo mpaka akafike kumalo kumene akupita. Kodi malowo n’ciyani? Amene ali na ciyembekezo codzapita kumwamba, “Msewu wa Ciyelo” udzawafikitsa “m’paradaiso wa Mulungu” kumwamba. (Chiv. 2:7) Koma amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi, msewu waukuluwo udzawafikitsa kumoyo wangwilo kumapeto kwa zaka 1,000. Ngati mukuyenda pa msewu waukulu umenewo, conde musachokove na kuyang’ana zakumbuyo. Musacokemo mu msewuwo mpaka mukafike m’dziko latsopano. w23.05 17 ¶15; 19 ¶16-18
Cinayi, August 7
Ife timasonyeza cikondi, cifukwa Mulungu ndi amene anayamba kutikonda.—1 Yoh. 4:19.
Cisankho codzipatulila kwa Yehova sicikhala covuta kupanga mukaganizila pa zonse zimene wakucitilani. (Sal 116:12-14) Moyenela Baibo imacha Yehova Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.” (Yak. 1:17) Mphatso yaikulu pa zonse ni nsembe ya Mwana wake, Yesu. Tangoganizani, dipo limapangitsa kuti cikhale cotheka kukhala pa ubale wabwino na Yehova. Ndipo wakupatsani ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya. (1 Yoh. 4:9, 10) Kudzipatulila kwanu kwa Yehova ni njila yabwino zedi yoonetsela kuyamikila kwanu cikondi copambana cimene iye anakuonetsani, kuphatikizaponso madalitso ena amene iye wakukonzelani.—Deut. 16:17; 2 Akor. 5:15. w24.03 5 ¶8
Cisanu, August 8
Munthu amene amacita zabwino amaopa Yehova.—Miy. 14:2.
Tikamaona makhalidwe oipa m’dzikoli, timamva monga mmene Loti anamvela. Iye “anavutika mtima kwambili ndi kulowelela kwa anthu ophwanya malamulo mu khalidwe lawo lotayilila,” podziŵa kuti Atate wathu wakumwamba amadana na makhalidwe oipa. (2 Pet. 2:7, 8) Kuopa Mulungu komanso kum’konda kunalimbikitsa Loti kupewa makhalidwe oipa a anthu a m’nthawi yake. Nafenso masiku ano, tili pakati pa anthu amene salemekeza malamulo a Yehova. Ngakhale n’telo, n’zotheka kukhalabe oyela ngati timam’konda Mulungu na kumuopa. Yehova amatithandiza kucita zimenezo kupyolela m’buku la Miyambo. Akhristu onse, amuna, akazi, ana, komanso okalamba, angapindule na uphungu wanzelu wa m’bukuli. Kuopa Yehova kumatithandiza kupewa kugwilizana na anthu a makhalidwe oipa. w23.06 20 ¶1-2; 21 ¶5
Ciŵelu, August 9
Ngati munthu akufuna kunditsatila, adzikane yekha ndipo anyamule mtengo wake wozunzikilapo nʼkupitiliza kunditsatila tsiku ndi tsiku.—Luka 9:23.
Mwina acibale anu akukutsutsani, kapena munasiya zolinga zanu za kuthupi kuti muike za Ufumu patsogolo pa umoyo wanu. (Mat. 6:33) Ngati n’telo, dziŵani kuti Yehova amaona nchito za kukhulupilika kwanu. (Aheb. 6:10) Mwacionekele, mwapeza madalitso amene Yesu anachula ponena kuti: “Palibe amene anasiya nyumba, abale, alongo, amayi, abambo, ana kapena minda cifukwa ca ine, ndi cifukwa ca uthenga wabwino, amene panopa sadzapeza zoculuka kuwilikiza maulendo 100 m’nthawi ino. Iye adzapeza nyumba, abale, alongo, amayi, ana na minda, pamodzi na mazunzo, ndipo m’nthawi imene ikubwelayo, adzapeza moyo wosatha.” (Maliko 10:29, 30) Madalitso amene mwapezawo ni oculuka kwambili kuposa zimene munasiya.—Sal. 37:4. w24.03 9 ¶5
Sondo, August 10
Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.—Miy. 17:17.
Pamene Akhristu ku Yudeya anali pa njala yadzaoneni. Abale mu mpingo wa ku Antiokeya “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo kwa abale a ku Yudeya, aliyense mogwilizana ndi zimene akanakwanitsa.” (Mac. 11:27-30) Ngakhale kuti okhudzidwa na njala anali kukhala kutali kwambili na ku Antiyokeya, Akhristu a ku Antiyokeya anapelekabe thandizo kwa abale awo. (1 Yoh. 3:17, 18) Nafenso tingawacitile cifundo alambili anzathu tikamva kuti tsoka lawagwela. Timacitapo kanthu mwamsanga, mwina mwa kufunsa akulu ngati tingadzipeleke kukathandizila. Cina, timapanga zopeleka pa nchito ya padziko lonse, kapena timapemphelela omwe akumana na tsokalo. Abale na alongo athu angadzafunikile thandizo kuti apeze zofunikila pa umoyo. Mfumu yathu Khristu Yesu akadzabwela kudzaweluza anthu, tikufuna adzatipeze tikuonetsa cifundo, na kutiuza kuti “lowani mu Ufumu.”—Mat. 25:34-40. w23.07 4 ¶9-10; 6 ¶12
Mande, August 11
Anthu onse adziŵe kuti ndinu ololela.—Afil. 4:5.
Yesu anatengela citsanzo ca Yehova ca kulolela. Iye anatumidwa padziko lapansi kudzalalikila “kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” Koma anaonetsa kulolela pocita utumiki wakewo. Panthawi ina, mayi wina amene sanali Mwisiraeli anam’condelela kuti acilitse mwana wake wamkazi, amene anali ‘atagwidwa ndi ciwanda mocititsa mantha.’ Mwacifundo, Yesu anacita zimene mayiyo anam’pempha ndipo anam’cilitsa mwanayo. (Mat. 15:21-28) Naci citsanzo cina. Ca kumayambililo kwa utumiki wake, Yesu ananena kuti: “Aliyense amene adzandikane . . . , inenso ndidzamukana.” (Mat. 10:33) Iye anakanidwa katatu na Petulo. Koma kodi Yesu anam’kana Petulo? Ayi. Yesu anaona kulapa na cikhulupililo ca Petulo. Pambuyo poukitsidwa, Yesu anaonekela kwa Petulo. Ndipo mwacionekele, anam’tsimikizila kuti anam’khululukila komanso kuti anali kum’kondabe. (Luka 24:33, 34) Yehova Mulungu na Yesu Khristu ni ololela. Nanga bwanji ife? Yehova amafuna kuti nafenso tikhale ololela. w23.07 21 ¶6-7
Ciŵili, August 12
Imfa sidzakhalaponso.—Chiv. 21:4.
Kodi ni zitsimikizo ziti zimene tingauzeko aja amene amakaikila zakuti lonjezo la Mulungu la Paradaiso lidzakwanilitsidwa? Coyamba, Yehova iye mwini ndiye anapeleka lonjezolo. Buku la Chivumbulutso limati: “Wokhala pampando wacifumu anati: ‘Taonani! Ndikupanga zinthu zonse kukhala zatsopano.’” Iye ali na nzelu, mphamvu, komanso cifuno cokwanilitsa lonjezo lake limeneli. Caciŵili, kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli ni kodalilika, moti malinga na kaonedwe ka Yehova, kwa iye zili ngati zakwanilitsika kale. Ndiye cifukwa cake anati: “Mawu awa ndi odalilika ndi oona. . . . Zakwanilitsidwa!” Cacitatu, Yehova akayamba kucita cina cake, amacicitabe mpaka atacikwanilitsa, ndiye cifukwa cake anati: “Ine ndine Alefa ndi Omega.” (Chiv. 21:6) Yehova adzaonetsa poyela kuti Satana ni wabodza komanso wolephela. Conco, wina akadzanena kuti, “N’zosatheka kucitika,” mukaŵelenge na kumufotokozela Chivumbulutso 21:5, 6. Muonetseni mmene Yehova watsimikizila lonjezo lake limeneli mwa kulisainila iye mwini, titelo kunena kwake.—Yes. 65:16. w23.11 7 ¶18-19
Citatu, August 13
Ndidzakupangitsa kuti ukhale mtundu waukulu.—Gen. 12:2.
Yehova ananena lonjezo limeneli kwa Abulahamu amene anali na zaka 75 ndipo analibe mwana. Kodi Abulahamu anaona kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli? Osati kwathunthu. Atawoloka Mtsinje wa Firate, anayembekezela zaka 25 kuti mozizwitsa akhale na mwana Isaki. Ndipo anayembekezelanso zaka zina 60 kuti adzukulu ake Esau na Yakobo abadwe. (Aheb. 6:15) Koma Abulahamu sanaone mbadwa zake zikukhala mtundu waukulu na kulandila Dziko Lolonjezedwa. Ngakhale n’telo, munthu wokhulupilika ameneyu anali pa ubwenzi wolimba na Mlengi wake. (Yak. 2:23) Abulahamu akadzaukitsidwa, adzakondwela kwambili kudziŵa kuti cikhulupililo na kuleza mtima kwake zinabweletsa madalitso ku mtundu wonse wa anthu. (Gen. 22:18) Kodi tiphunzilapo ciyani? Si malonjezo onse a Yehova amene adzakwanilitsidwa ife tili moyo. Komabe, tikaleza mtima monga Abulahamu, tidzakhala otsimikiza kuti Yehova adzatifupa pali pano, komanso m’dziko latsopano tidzalandila madalitso oculuka.—Maliko 10:29, 30. w23.08 24 ¶14
Cinayi, August 14
Pa nthawi imene iye ankafunafuna Yehova, Mulungu woonayo anacititsa kuti zinthu zizimuyendela bwino.—2 Mbiri 26:5.
Ali wacicepele, Mfumu Uziya anali wodzicepetsa. Iye anaphunzila ‘kuopa Mulungu woona.’ Uziya anakhala na moyo kwa zaka 68, ndipo kwa zaka zambili pa umoyo wake Yehova anamudalitsa. (2 Mbiri 26:1-4) Uziya anagonjetsa adani ambili a Yuda, ndipo anakhwimitsa citetezo ca Yerusalemu. (2 Mbiri 26:6-15) Mosakaika, Uziya anakondwela ngako cifukwa ca zimene Mulungu anam’thandiza kucita. (Mlal. 3:12, 13) Mfumu Uziya anali atazoloŵela kuuza ena zoyenela kucita. N’kutheka kuti izi zinam’pangitsa kuona kuti angacite ciliconse cimene afuna. Tsiku lina, Uziya analoŵa m’kacisi wa Yehova, ndipo modzikuza anayamba kufukiza nsembe, cinthu cimene mafumu sanali kuloledwa kucita. (2 Mbiri 26:16-18) Mkulu wa Ansembe Azariya anayesa kumuwongolela, koma Uziya anakwiya zedi. N’zacisoni kuti Uziya anawononga mbili yake yokhulupilika, ndipo anakanthidwa na khate. (2 Mbiri 26:19-21) Akanakhalabe wodzicepetsa, moyo wake ukanakhala wabwino ngako! w23.09 10 ¶9-10
Cisanu, August 15
Iye . . . anadzipatula, cifukwa ankaopa anthu odulidwawo.—Agal. 2:12.
Ngakhale pambuyo pokhala Mkhristu wodzozedwa, mtumwi Petulo anali kulimbanabe na zifooko zake. Mu 36 C.E, Petulo anaona kamaso pamene Koneliyo, munthu wosadulidwa, anadzozedwa na mzimu woyela. Uwu unali umboni woonekelatu wakuti “Mulungu alibe tsankho,” komanso kuti anthu amitundu ina angakhale mu mpingo wacikhristu. (Mac. 10:34, 44, 45) Pambuyo pa izi, Petulo anali womasuka kudyela pamodzi na anthu a mitundu ina, zimene kumbuyoku sakanacita. Komabe, Akhristu ena aciyuda anali kuona kuti Ayuda na anthu amitundu ina sayenela kudyela pamodzi. Ayuda ena atafika ku Antiokeya, Petulo analeka kudya na Akhristu a mitundu ina, mwina poopa kukhumudwitsa Akhristu aciyuda. Mtumwi Paulo anaona kuti cimeneco n’cinyengo. Conco, anam’dzudzula pamaso pa anthu. (Agal. 2:13, 14) Ngakhale kuti Petulo anaphonyetsanso, sanabwelele m’mbuyo. w23.09 22 ¶8
Ciŵelu, August 16
Adzakulimbitsani.—1 Pet. 5:10.
Kudziunika moona mtima kungakuthandizeni kuti muone pamene muyenela kuongolela, koma musalefuke. “Ambuye ndi wokoma mtima,” ndipo adzakuthandizani kuti muongolele. (1 Pet. 2:3) Mtumwi Petulo anatitsimikizila kuti “Mulungu . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani.” Panthawi ina, Petulo anaziona wosayenela kukhala pamodzi na Mwana wa Mulungu. (Luka 5:8) Koma cifukwa ca thandizo la Yehova komanso la Yesu, anakwanitsa kutsatila Khristu mokhulupilika. Zotsatila zake zinali zakuti Yehova ‘anam’tsegulila khomo kuti aloŵe mwaulemelelo mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.’ (2 Pet. 1:11) Mphoto yosangalatsa zedi! Ngati mwaikilapo mtima mmene Petulo anacitila komanso kulola Yehova kuti akuphunzitseni, inunso mudzalandila mphoto ya moyo wosatha. Ndipo “cikhulupililo canu cidzacititsa kuti miyoyo yanu ipulumuke.”—1 Pet. 1:9. w23.09 31 ¶16-17
Sondo, August 17
Lambilani Iye amene anapanga kumwamba, [ndi] dziko lapansi.—Chiv. 14:7.
Cihema cinali na bwalo lomwe linali locingidwa na mpanda mmene ansembe anali kucitila utumiki wawo. Guwa lansembe lamkuwa lofukizilapo nsembe linali m’bwalo limeneli pamodzi na beseni lamkuwa lomwe ansembe anali kuseŵenzetsa podziyeletsa asanayambe kugwila nchito yawo yopatulika. (Eks. 30:17-20; 40:6-8) Masiku ano, otsalila odzodzedwa a Khristu amatumikila mokhulupilika padziko lapansi m’bwalo lamkati la kacisi wauzimu asanapite kukatumikila monga ansembe na Yesu kumwamba. Beseni la madzi lomwe linali pacihema limakumbutsa odzodzedwa komanso Akhristu onse kuti ayenela kukhala oyela m’makhalidwe komanso mwauzimu. Koma kodi “a khamu lalikulu”, amalambilila kuti? Mtumwi Yohane anawaona “ataimilila pamaso pa mpando wacifumu,” limene ni bwalo lakunja la kacisi wa Yehova, komwe “akumucitila utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kacisi wake.” (Chiv. 7:9, 13-15) Ndife oyamikila ngako kuti tili na malo m’makozedwa a Yehova akulambila koyela! w23.10 28 ¶15-16
Mande, August 18
Cifukwa ca lonjezo la Mulungu, . . . cikhulupililo cakeco cinamupatsa mphamvu.—Aroma 4:20.
Njila imodzi imene Yehova amatipatsila mphamvu ni kupitila mwa akulu. (Yes. 32:1, 2) Conco, mukakhala na nkhawa afotokozeleni akulu. Muzilandila thandizo lawo moyamikila. Yehova angakulimbikitseni kupitila mwa iwo. Ciyembekezo cathu cozikika pa Baibo codzakhala m’paradiso pano pa dziko lapansi, kapena cokakhala kumwamba cingatipatse mphamvu. (Aroma 4:3, 18, 19) Ciyembekezo cathu cimeneci cimatilimbikitsa kupilila mavuto, kulalikila uthenga wabwino, komanso kucita mautumiki osiyani-siyani mu mpingo. (1 Ates. 1:3) Ciyembekezo cimeneci n’cimene cinalimbikitsa mtumwi Paulo. Iye ‘anapanikizidwa,’ ‘kuthedwa nzelu,’ ‘kuzunzidwa,’ komanso ‘kugwetsedwa pansi.’ Ndipo moyo wake weniweniwo unali paciopsezo. (2 Akor. 4:8-10) Paulo anapeza mphamvu zopilila mwakuika maganizo pa ciyembekezo cake. (2 Akor. 4:16-18) Iye anaika maganizo ake pa ciyembekezo ca moyo wosafa kumwamba. Paulo anali kusinkhasinkha za ciyembekezo cimeneco. Conco anayamba kudziona kuti “akucititsidwa kukhala watsopano tsiku ndi tsiku.” w23.10 15-16 ¶14-17
Ciŵili, August 19
Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu. Yehova adzadalitsa anthu ake powapatsa mtendele.—Sal. 29:11.
Mukamapemphela, muyenela kuganizila ngati ni nthawi yoyenela kuti Yehova ayankhe pemphelo lanu. Nthawi zina tingaone kuti tifunikila yankho lam’mangu-m’mangu pa pemphelo lathu. Koma Yehova ndiye amadziŵa bwino nthawi yoyenela kutiyankha. (Aheb. 4:16) Ngati nthawi yomweyo sitinalandile zimene tapempha, tingaganize kuti yankho la Yehova n’lakuti ‘Iyai.’ Koma yankho lake m’ceni-ceni lingakhale lakuti ‘Osati pali pano.’ Mwacitsanzo, m’bale wacinyamata wina anapempha kuti acilitsidwe matenda ake. Koma sanacile. Ngati Yehova mozizwitsa akanam’cilitsa m’baleyo, Satana akanati m’baleyo anapitiliza kutumikila Yehova cifukwa cakuti anam’cilitsa. (Yobu 1:9-11; 2:4) Kuwonjezela apo, Yehova anaikilatu kale nthawi pamene adzacotselatu matenda onse. (Yes. 33:24; Chiv. 21:3, 4) Koma pakali pano, tisayembekezele kucilitsidwa mozizwitsa. Conco m’baleyo angapemphe Yehova kuti am’patse mphamvu komanso mtendele wa mumtima, kuti apilile matendawo na kupitiliza kumutumikila mokhulupilika. w23.11 24 ¶13
Citatu, August 20
Sanaticitile mogwilizana ndi macimo athu, kapena kutipatsa cilango cogwilizana ndi zolakwa zathu.—Sal. 103:10.
Ngakhale kuti Samisoni anapanga colakwa cacikulu, sanafooke. Iye anali kufuna-funa mpata kuti akwanilitse nchito imene Mulungu anamupatsa yogonjetsa Afilisiti. (Ower. 16:28-30) Iye anacondelela Yehova kuti: “Ndiloleni ndiwabwezele Afilisitiwa.” Mulungu woona anayankha pemphelo la Samisoni pobwezeletsa mphamvu zake zapadela. Conco pa tsikulo Samisoni anapha Afilisiti ambili kuposa amene anawapha mu umoyo wake wonse. Ngakhale kuti Samisoni anakumana na mavuto aakulu cifukwa ca colakwa cake, iye sanaleke kuyesetsa kucita cifunilo ca Yehova. Nafenso tikalakwitsa zina zake, kenako n’kudzudzulidwa kapena kucotsedwa paudindo, sitiyenela kuleka kuyesetsa kucita cifunilo ca Yehova. Musaiŵale kuti Yehova ni okonzeka kutikhululukila. (Sal. 103:8, 9) Monga zinalili kwa Samisoni, nafenso Yehova angadzapitilize kutigwilitsa nchito ngakhale titalakwitsa zina zake. w23.09 6 ¶15-16
Cinayi, August 21
Kupilila kumacititsa kuti tikhale ovomelezeka kwa Mulungu ndipo kukhala ovomelezeka kwa Mulungu kumacititsa kuti tikhale ndi ciyembekezo.—Aroma 5:4.
Kupilila kwanu kungacititse kuti mukhale ovomelezeka kwa Yehova. Izi sizitanthauza kuti Yehova amakondwela mukamakumana na mavuto ayi. M’malo mwake amakondwela kuti mwakwanitsa kupilila mokhulupilika. N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti tikapilila timakondweletsa Yehova! (Sal. 5:12) Kumbukilani kuti Abulahamu anapilila mayeso, ndipo pothela pake anayanjidwa na Mulungu. Anakhala bwenzi la Yehova, ndipo anaonedwa wolungama. (Gen. 15:6; Aroma 4:13, 22) Zingakhalenso cimodzi-modzi kwa ife. Mulungu satiyanja cifukwa ca kuculuka kwa nchito zimene timacita mu utumiki wake, kapena maudindo amene tili nawo. M’malo mwake, amatiyanja cifukwa ca kupilila kwathu mokhulupilika. Tonsefe tingakwanitse kupilila mosasamala kanthu za msinkhu wathu, mikhalidwe yathu, na maluso athu. Kodi mukupilila mokhulupilika mayeso ena ake pali pano? Ngati n’telo, pezani citonthozo podziŵa kuti Mulungu akusangalala nanu. Kudziŵa zimenezi kumalimbikitsa ciyembekezo cathu. w23.12 11 ¶13-14
Cisanu, August 22
Iweyo ucite zinthu mwamphamvu.—1 Maf. 2:2.
Mwamuna wacikhristu ayenela kuphunzila kukamba bwino na ena. Mwamuna amene amakamba bwino na ena amamvetsela zimene ena akunena ndipo amazindikila mmene akumvela. (Miy. 20:5) Amamvetsa mmene ena akumvela poona mmene akulankhulila, komanso magesica amene akupanga polankhula. Simungakwanitse kucita zimenezi ngati simupatula nthawi yoceza na anthu. Ngati nthawi zambili mumaceza na anthu pa mameseji, simungakulitse luso lanu lokambilana na anthu pamaso-m’pamaso. Conco, muzipeza mipata yokambilana na anthu pamaso-m’pamaso. (2 Yoh. 12) Mkhristu wokhwima ayenela kudzisamalila komanso kusamalila a m’banja lake. (1 Tim. 5:8) M’pofunikila kuphunzila luso lina lake limene lingakuthandizeni kupeza nchito. (Mac. 18:2, 3; 20:34; Aef. 4:28) Muzidziŵika kuti ndinu munthu wakhama pa nchito, amene amayamba nchito na kuimalizitsa. Mukatelo, mudzapeza nchito na kukhalitsa pa nchitoyo. w23.12 27 ¶12-13
Ciŵelu, August 23
Tsiku la Yehova lidzabwela ndendende ngati wakuba usiku.—1 Ates. 5:2.
M’Baibo mawu akuti “tsiku la Yehova” amakamba za nthawi pamene Yehova adzawononga adani ake na kupulumutsa anthu ake. Kalelo, Yehova anaonetsapo zakuda mitundu ina. (Yes. 13:1, 6; Ezek. 13:5; Zef. 1:8) M’masiku athu ano, “tsiku la Yehova” lidzayamba na kuukilidwa kwa Babulo Wamkulu, ndipo lidzatha na nkhondo ya Aramagedo. Kuti tikapulumuke pa ‘tsikulo,’ tiyenela kukonzekela palipano. Yesu anati “khalani okonzeka” kaamba ka “cisautso cacikulu.” Izi zitanthauza kuti tiyenela kukhalabe okonzeka. (Mat. 24:21; Luka 12:40) M’kalata yake yoyamba youzilidwa yopita kwa Atesalonika, mtumwi Paulo anagwilitsa nchito mafanizo angapo pothandiza Akhristu kukhalabe okonzeka tsiku lalikulu la Yehova laciweluzo. Paulo anadziŵa kuti tsiku la Yehova silidzafika panthawi imeneyo. (2 Ates. 2:1-3) Ngakhale n’telo, iye analimbikitsa Akhristu anzake kukonzekela tsikulo ngati kuti lidzabwela maŵa. Nafenso tiyenela kuseŵenzetsa uphungu umenewo. w23.06 8 ¶1-2
Sondo, August 24
Abale anga okondedwa, khalani olimba, ndiponso osasunthika.—1 Akor. 15:58.
Mu 1978, nyumba yaitali ya nsanjika 60 inamangidwa mu mzinda wa Tokyo, ku Japan. Anthu anali kudzifunsa ngati nyumbayo idzapilila zivomezi zimene zinali kucitika pafupi-pafupi mu mzindawo. Kodi cinsinsi cake cinali ciyani? Akatswili anaimanga m’njila yakuti ikhale yolimba, koma panthawi imodzimodzi kuti ikhale yofeŵa kukacitika civomezi. Akhristu ali monga nyumba ya nsanjika imeneyo. Motani? Mkhristu ayenela kukhala wosasunthika. Koma ayenelanso kukhala wofeŵa kapena kuti wokonzeka kusintha. Ayenela kukhala wolimba komanso wosasunthika pa kumvela malamulo na miyeso ya Yehova. Iye ni ‘wokonzeka kumvela’ nthawi zonse. Kumbali ina, ayenela kukhala ‘wololela’ kapena kuti wokonzeka kusintha pakafunika kutelo. (Yak. 3:17) Mkhristu amene amaona zinthu mwa njila imeneyi amapewa kukhwimitsa kwambili zinthu, kapena kukhala wololela mopitilila malile. w23.07 14 ¶1-2
Mande, August 25
Ngakhale kuti Khristuyo simunamuonepo, mumamukonda.—1 Pet. 1:8.
Yesu analimbana na mayeselo osiyanasiyana ocokela kwa Satana, kuphatikizapo ciyeso comuuza mwacindunji kuti aleke kukhala wokhulupilika kwa Mulungu. (Mat. 4:1-11) Satana anali wotsimikiza mtima kucimwitsa Yesu kuti asathe kupeleka dipo. Yesu anakumananso na mayeso ena pocita utumiki wake pa dziko lapansi. Anazunzidwa, ndipo moyo wake unali paciopsezo. (Luka 4:28, 29; 13:31) Anali kupililanso zophophonya za otsatila ake. (Maliko 9:33, 34) Pozengedwa mlandu kuti aphedwe, anazunzidwa na kunyozedwa. Ndipo anaphedwa m’njila yoŵaŵa komanso yonyazitsa kwambili. (Aheb. 12:1-3) Anapilila yekha mavuto othela popanda Yehova kum’teteza. (Mat. 27:46) Kunena zoona, Yesu anavutika zedi kuti apeleke dipo. Ndipo tikaganizila zinthu zimene Yesu anapitamo modzipeleka kaamba ka ife, cikondi cathu pa iye cimakula. w24.01 10-11 ¶7-9
Ciŵili, August 26
Onse amene amacita zinthu mopupuluma amasauka.—Miy. 21:5.
Kuleza mtima kumatithandiza pocita zinthu na anthu ena. Kumatithandiza kumvetsela modekha ena akamalankhula. (Yak. 1:19) Kuleza mtima kumalimbikitsanso mtendele. Kumatiteteza kuti tisacite zinthu mopupuluma, na kukamba zinthu zosayenela tikapanikizika maganizo. Ndipo tikakhala oleza mtima, sitidzakwiya msanga wina akatikhumudwitsa. M’malo mobwezela, ‘tidzapitiliza kulolelana na kukhululukilana ndi mtima wonse.’ (Akol. 3:12, 13) Kuleza mtima kungatithandizenso kupanga zisankho zabwino. M’malo modya mfulumila, tidzapatula nthawi yofufuza na kusanthula zisankhozo kuti tione zimene zili zabwino koposa. Mwacitsanzo, tikamafuna-funa nchito, tingafulumile kuvomela nchito iliyonse imene yapezeka. Komabe, tikakhala oleza mtima, tidzakhala pansi na kuganizila mmene idzakhudzila banja lathu na umoyo wathu wauzimu. Tikakhala oleza mtima, tidzapewa kupanga zisankho zoipa. w23.08 22 ¶8-9
Citatu, August 27
Ndimaona lamulo lina mʼthupi langa likumenyana ndi malamulo amʼmaganizo mwanga nʼkundicititsa kukhala kapolo wa lamulo la ucimo limene lili mʼthupi langa.—Aroma 7:23.
Ngati mungalefuke poona kuti mumakhala na zilakolako zoipa, kuganizila lonjezo limene munapeleka kwa Yehova podzipatulila kudzakuthandizani kutsimikiza mtima kugonjetsa mayeselo. Ndipo zoona zake n’zakuti lumbilo lanu la kudzipatulila lidzakuthandizani kugonjetsa mayeselo. Motani? Mukadzipatulila kwa Yehova mumadzikana nokha. Izi zikutanthauza kunena kuti toto ku zikhumbo zanu, na zolinga zanu zimene sizingakondweletse Yehova. (Mat. 16:24) Conco, mukakumana na mayeso simudzacedwa na kuganizilapo zimene muyenela kucita. Mudzakhala mutadziwilatu zocita, zomwe ni kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Mudzakhalabe wosasunthika pa kukondweletsa Yehova. Mudzakhala ngati Yobu amene ngakhale pambuyo pokumana na mavuto aakulu ananena motsimikiza kuti: “Sindidzasiya kukhala wokhulupilika.”—Yobu 27:5. w24.03 9 ¶6-7
Cinayi, August 28
Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana, onse amene amamuitana mʼcoonadi.—Sal. 145:18.
Yehova, “Mulungu amene ndi wacikondi,” ali nafe! (2 Akor. 13:11) Iye amationetsa cidwi aliyense payekha-payekha. Ndife otsimikiza kuti ndife ‘otetezeka ndi cikondi Cake cokhulupilika.’ (Sal. 32:10) Tikapitiliza kusinkhasinkha za mmene iye waonetsela cikondi cake pa ife, m’pamene iyenso amakhala weniweni kwa ife. Ndipo timamva kuti tikuyandikana naye. Tingamufikile momasuka na kumuuza kufunika kwa cikondi cake kwa ife. Tingamufotokozele nkhawa zathu zonse tili na cidalilo kuti amatimvetsa, komanso kuti ni wofunitsitsa kutithandiza. (Sal. 145:19) Monga mmene timafunila moto kukazizila, tifunikilanso cikondi ca Yehova. Ngakhale kuti cikondi ca Yehova n’camphamvu, cimapelekedwa mokoma mtima. Conco muzikhala wosangalala podziŵa kuti Yehova amakukondani kwambili. Ndipo tonsefe tiyeni tinene mofuula za cikondi cake kuti: “Ndimakonda Yehova”!—Sal. 116:1. w24.01 31 ¶19-20
Cisanu, August 29
Ine ndacititsa kuti iwo adziŵe dzina lanu.—Yoh. 17:26
Yesu anacita zambili kuposa kungouza anthu kuti dzina la Mulungu ni Yehova. Ayuda omwe Yesu anali kuphunzitsa anali kulidziŵa kale dzina la Mulungu. Koma Yesu anakhala patsogolo ‘kuwafotokozela za Mulungu.’ (Yoh. 1:17, 18) Mwa citsanzo, Malemba a Ciheberi amaonetsa kuti Yehova ni wacifundo, komanso wacisomo. (Eks. 34:5-7) Yesu anafotokoza coonadi cimeneci momveka bwino pomwe anakamba za fanizo la mwana woloŵelela. Bambo wa m’fanizoli ataona mwana wake wolapa “ali capatali ndithu,” anathamangila mwanayo, kumukumbatila na kum’khululukila na mtima wonse. Zimenezi zimatithandiza kumvetsa bwino cifundo ca Yehova na cisomo cake. (Luka 15:11-32) Yesu anathandiza ena kumvetsa kuti Yehova ni Tate wotani kwenikweni. w24.02 10 ¶8-9
Ciŵelu, August 30
[Tonthozani ena] . . . cifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.—2 Akor. 1:4.
Yehova amatsitsimula komanso kutonthoza opsinjika maganizo. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova ca kumvela ena cifundo komanso kuwatonthoza? Njila imodzi imene tingacitile zimenezi ni kukulitsa makhalidwe abwino mu mtima mwathu amene angatithandize kutonthoza ena. Kodi ena mwa makhalidwe amenewa ni ati? N’ciyani cingatithandize kukhalabe na cikondi kuti “tipitilize kutonthozana” tsiku na tsiku? (1 Ates. 4:18)Tiyenela kukhala na makhalidwe monga kumvela ena cisoni, kukonda abale, komanso kukhala okoma mtima. (Akol. 3:12; 1 Pet. 3:8) Kodi makhalidwewa adzatithandiza bwanji? Ngati tipanga cifundo na makhalidwe ena otelo kukhala mbali ya umunthu wathu, sicidzakhala covuta kutonthoza amene akuvutika. Yesu anakamba kuti, “pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’cuma cake cabwino.” (Mat. 12:34, 35) Kutonthoza abale na alongo amene akukumana na zovuta ni njila yaikulu imene timaonetsela kuti timawakonda. w23.11 10 ¶10-11
Sondo, August 31
Anthu ozindikila adzawamvetsetsa.—Dan. 12:10.
Tiyenela kupempha thandizo kuti timvetse maulosi a m’Baibo. Nali fanizo. Yelekezani kuti mwapita ku malo acilendo, koma mnzanu amene mwapita naye amawadziŵa bwino malowo. Akudziŵa bwino pamene muli komanso kumene misewu ikupita. Mosakayika konse, mudzakondwela kwambili kuti mnzanuyo wakupelekezani. Inde, paja amati kuyenda aŵili si mantha! Mofananamo, Yehova akudziŵa bwino pomwe tafika na kumene tikupita. Conco, kuti timvetse maulosi a m’Baibo tiyenela kupempha thandizo la Yehova modzicepetsa. (Dan. 2:28; 2 Pet. 1:19, 20) Molingana na kholo lililonse labwino, Yehova amafuna kuti ana ake akhale na tsogolo lacimwemwe. (Yer. 29:11) Koma mosiyana na makolo aumunthu, Yehova amakambilatu zakutsogolo, ndipo saphonyetsa ngakhale pang’ono. Iye anaikamo maulosi m’Baibo kuti tidziŵiletu pasadakhale zocitika zofunika kwambili.—Yes. 46:10. w23.08 8 ¶3-4