Cisanu, September 5
Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pangʼono kugwa ndipo amadzutsa onse amene aŵelama cifukwa ca mavuto.—Sal. 145:14.
Ngakhale titakhala na cikhumbo kapena odziletsa, nthawi zina tingalepheleko ndithu. Mwacitsanzo, “zinthu zosayembekezeleka” zingatilande nthawi yokwanilitsa zolinga zathu. (Mlal. 9:11) Tingakumane na vuto lalikulu limene lingatilefule na kutilanda mphamvu. (Miy. 24:10) Ndipo cifukwa ca kupanda ungwilo, tingalakwitse zinazake. Izi zingatilepheletse kukwanilitsa colinga cathu. (Aroma 7:23) Cina, tingafike potopa nazo. (Mat. 26:43) N’ciyani cingatithandize kugonjetsa zobweza kumbuyo zimenezi? Kumbukilani kuti dzedzele-dzedzele si kugwa. Baibo imati tingakumane na mavuto mobweleza-bweleza. Koma imakambanso kuti tinganyamukenso. Inde, mukamayesetsa kukwanilitsa zolinga zanu olo kuti mumalephelako nthawi zina, mumaonetsa Yehova kuti mukufuna kum’kondweletsa. Yehova amakondwela kwambili akakuonani mukuyesetsa kukwanilitsa colinga canu. w23.05 30 ¶14-15
Ciŵelu, September 6
Muzipeleka citsanzo cabwino kwa gulu la nkhosa.—1 Pet. 5:3.
Upainiya umathandiza wacinyamata kuphunzila kuseŵenza bwino na anthu osiyana-siyana. Umam’thandizanso kupanga bajeti yabwino na kuitsatila. (Afil. 4:11-13) Ciyambi cabwino coyamba utumiki wa nthawi zonse ni kucita upainiya wothandiza umene umawathandiza kuti ayambe upainiya wa nthawi zonse. Upainiya wa nthawi zonse umatsegula mipata ku mautumiki ena a nthawi zonse osiyana-siyana, monga kutumikila m’dipatimenti ya zamamangidwe kapena pa Beteli. Amuna acikhristu ayenela kukhala na colinga cokwanilitsa ziyeneletso kuti atumikile abale na alongo awo mu mpingo monga akulu. Baibo imati amuna amene akuyesetsa kuti akhale oyang’anila “akufuna nchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Coyamba, m’bale afunika kuyenelela kukhala mtumiki wothandiza. Atumiki othandiza amathandiza akulu m’njila zosiyana-siyana. Akulu na atumiki othandiza amatumikila abale na alongo awo modzicepetsa ndipo amalalikila mokangalika. w23.12 28 ¶14-16.
Sondo, September 7
Akadali mnyamata, . . . anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide kholo lake.—2 Mbiri 34:3.
Mfumu Yosiya anayamba kufuna-funa Yehova ali mnyamata. Anali wofunitsitsa kuphunzila za Yehova na kucita cifunilo cake. Komabe, umoyo sunali wopepuka kwa mfumu yacinyamatayi. Anafunika kulimba mtima kuti abwezeletse kulambila koyela panthawi imene kulambila konyenga kunali kofala. Ndipo anatelodi! Asanakwanitse zaka 20, Yosiya anayamba kucotsa kulambila konyenga m’dzikolo. (2 Mbiri 34:1, 2) Ngakhale kuti ndinu wacicepele kwambili, mungathe kutengela Yosiya mwa kufuna-funa Yehova na kuphunzila za makhalidwe ake. Izi zingakulimbikitseni kupatulila moyo wanu kwa iye. Kodi kudzipatulila kumeneku kudzakhudza bwanji umoyo wanu wa tsiku na tsiku? Pa tsiku limene anali kubatizika, ali na zaka 14, Luke anati, “Kuyambila lelo, nidzaika kutumikila Yehova patsogolo mu umoyo wanga, ndipo nidzayesetsa kumukondweletsa.” (Maliko 12:30) Ngati ni zimene nanunso mufuna kucita, mudzadalitsika kwambili! w23.09 11 ¶12-13