Cinayi, September 4
Kumeneko kudzakhala msewu waukulu inde msewu umene udzachedwa Msewu Wopatulika.—Yes. 35:8.
Ayuda obwelela kwawo anali kudzakhala “anthu oyela” kwa Mulungu wawo. (Deut. 7:6) Komabe, izi sizinatanthauze kuti sanafunike kupanga masinthidwe kuti Yehova awayanje. Ayuda ambili anabadwila ku Babulo, ndipo n’kutheka kuti anatengela maganizo na cikhalidwe ca Ababulo. Patapita zaka zambili Ayuda oyamba atabwelela ku Isiraeli, Bwanamkubwa Nehemiya anadabwa ataona kuti ana obadwila ku Isiraeli sanali kudziŵa cinenelo ca Ayuda. (Deut. 6:6, 7; Neh. 13:23, 24) Popeza mbali yaikulu ya Mawu a Mulungu inali m’Ciheberi, kodi anawo akanaphunzila bwanji kukonda Yehova na kum’lambila? (Ezara 10:3, 44) Conco, Ayudawo anafunika kupanga masinthidwe aakulu. Koma cikanakhala copepuka kwa iwo kucita zimenezo ku Isiraeli komwe kulambila koona kunali kubwezeletsedwa mwapang’ono-pang’ono.—Neh. 8:8, 9. w23.05 15 ¶6-7
Cisanu, September 5
Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pangʼono kugwa ndipo amadzutsa onse amene aŵelama cifukwa ca mavuto.—Sal. 145:14.
Ngakhale titakhala na cikhumbo kapena odziletsa, nthawi zina tingalepheleko ndithu. Mwacitsanzo, “zinthu zosayembekezeleka” zingatilande nthawi yokwanilitsa zolinga zathu. (Mlal. 9:11) Tingakumane na vuto lalikulu limene lingatilefule na kutilanda mphamvu. (Miy. 24:10) Ndipo cifukwa ca kupanda ungwilo, tingalakwitse zinazake. Izi zingatilepheletse kukwanilitsa colinga cathu. (Aroma 7:23) Cina, tingafike potopa nazo. (Mat. 26:43) N’ciyani cingatithandize kugonjetsa zobweza kumbuyo zimenezi? Kumbukilani kuti dzedzele-dzedzele si kugwa. Baibo imati tingakumane na mavuto mobweleza-bweleza. Koma imakambanso kuti tinganyamukenso. Inde, mukamayesetsa kukwanilitsa zolinga zanu olo kuti mumalephelako nthawi zina, mumaonetsa Yehova kuti mukufuna kum’kondweletsa. Yehova amakondwela kwambili akakuonani mukuyesetsa kukwanilitsa colinga canu. w23.05 30 ¶14-15
Ciŵelu, September 6
Muzipeleka citsanzo cabwino kwa gulu la nkhosa.—1 Pet. 5:3.
Upainiya umathandiza wacinyamata kuphunzila kuseŵenza bwino na anthu osiyana-siyana. Umam’thandizanso kupanga bajeti yabwino na kuitsatila. (Afil. 4:11-13) Ciyambi cabwino coyamba utumiki wa nthawi zonse ni kucita upainiya wothandiza umene umawathandiza kuti ayambe upainiya wa nthawi zonse. Upainiya wa nthawi zonse umatsegula mipata ku mautumiki ena a nthawi zonse osiyana-siyana, monga kutumikila m’dipatimenti ya zamamangidwe kapena pa Beteli. Amuna acikhristu ayenela kukhala na colinga cokwanilitsa ziyeneletso kuti atumikile abale na alongo awo mu mpingo monga akulu. Baibo imati amuna amene akuyesetsa kuti akhale oyang’anila “akufuna nchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Coyamba, m’bale afunika kuyenelela kukhala mtumiki wothandiza. Atumiki othandiza amathandiza akulu m’njila zosiyana-siyana. Akulu na atumiki othandiza amatumikila abale na alongo awo modzicepetsa ndipo amalalikila mokangalika. w23.12 28 ¶14-16.