Citatu, September 3
Yosefe . . . [anacita] mogwilizana ndi zimene mngelo wa Yehova anamuuza. Anatenga mkazi wake nʼkupita naye kunyumba.—Mat. 1:24.
Mofunitsitsa Yosefe anatsatila citsogozo ca Yehova. Mwa ici, anakhala mwamuna wabwino. Katatu konse, Mulungu anam’patsa malangizo okhudza banja lake. Pa nthawi zonsezo, anatsatila malangizowo ngakhale pamene zinali zovuta kutelo. (Mat. 1:20; 2:13-15, 19-21) Cifukwa cotsatila malangizo a Mulungu, Yosefe anateteza Mariya, kum’thandiza, komanso kum’samalila. Izi zinapangitsa Mariya kuti azim’konda Yosefe na kum’lemekeza. Inu amuna, mungatengele citsanzo ca Yosefe mwa kutsatila ulangizi wa m’Baibo posamalila banja lanu. Mukatelo, ngakhale pamene n’zovuta, mumaonetsa kuti mumam’konda mkazi wanu, ndipo mumalimbitsa ukwati wanu. Mlongo wina ku Vanuatu, amene wakhala m’banja zaka zoposa 20 anati: “Mwamuna wanga akamafufuza na kutsatila malangizo a m’Baibo, nimam’lemekeza kwambili. Nimamva kukhala wotetezeka, ndipo sinimakayikila zisankho zake.” w23.05 21 ¶5
Cinayi, September 4
Kumeneko kudzakhala msewu waukulu inde msewu umene udzachedwa Msewu Wopatulika.—Yes. 35:8.
Ayuda obwelela kwawo anali kudzakhala “anthu oyela” kwa Mulungu wawo. (Deut. 7:6) Komabe, izi sizinatanthauze kuti sanafunike kupanga masinthidwe kuti Yehova awayanje. Ayuda ambili anabadwila ku Babulo, ndipo n’kutheka kuti anatengela maganizo na cikhalidwe ca Ababulo. Patapita zaka zambili Ayuda oyamba atabwelela ku Isiraeli, Bwanamkubwa Nehemiya anadabwa ataona kuti ana obadwila ku Isiraeli sanali kudziŵa cinenelo ca Ayuda. (Deut. 6:6, 7; Neh. 13:23, 24) Popeza mbali yaikulu ya Mawu a Mulungu inali m’Ciheberi, kodi anawo akanaphunzila bwanji kukonda Yehova na kum’lambila? (Ezara 10:3, 44) Conco, Ayudawo anafunika kupanga masinthidwe aakulu. Koma cikanakhala copepuka kwa iwo kucita zimenezo ku Isiraeli komwe kulambila koona kunali kubwezeletsedwa mwapang’ono-pang’ono.—Neh. 8:8, 9. w23.05 15 ¶6-7
Cisanu, September 5
Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pangʼono kugwa ndipo amadzutsa onse amene aŵelama cifukwa ca mavuto.—Sal. 145:14.
Ngakhale titakhala na cikhumbo kapena odziletsa, nthawi zina tingalepheleko ndithu. Mwacitsanzo, “zinthu zosayembekezeleka” zingatilande nthawi yokwanilitsa zolinga zathu. (Mlal. 9:11) Tingakumane na vuto lalikulu limene lingatilefule na kutilanda mphamvu. (Miy. 24:10) Ndipo cifukwa ca kupanda ungwilo, tingalakwitse zinazake. Izi zingatilepheletse kukwanilitsa colinga cathu. (Aroma 7:23) Cina, tingafike potopa nazo. (Mat. 26:43) N’ciyani cingatithandize kugonjetsa zobweza kumbuyo zimenezi? Kumbukilani kuti dzedzele-dzedzele si kugwa. Baibo imati tingakumane na mavuto mobweleza-bweleza. Koma imakambanso kuti tinganyamukenso. Inde, mukamayesetsa kukwanilitsa zolinga zanu olo kuti mumalephelako nthawi zina, mumaonetsa Yehova kuti mukufuna kum’kondweletsa. Yehova amakondwela kwambili akakuonani mukuyesetsa kukwanilitsa colinga canu. w23.05 30 ¶14-15