LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • hf section 5 gao 1-2
  • Mmene Mungakhalile Mwamtendele ndi Acibale Anu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Mungakhalile Mwamtendele ndi Acibale Anu
  • N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • 1 PITILIZANI KUONA MOYENELELA ACIBALE ANU
  • 2 KHALANI OSASUNTHIKA NGATI M’POFUNIKA KUTELO
  • Khalani Okhulupilika kwa Wina ndi Mnzake
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Dalilani Mulungu Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Pambuyo Pa Tsiku La Cikwati
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Mmene Mungathetsele Mavuto
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
Onaninso Zina
N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
hf section 5 gao 1-2
Mai ayang’ana mpongozi wao mokhumudwa kuonetsa kusasangalala ndi maphikidwe ake

GAWO 5

Mmene Mungakhalile Mwamtendele ndi Acibale Anu

“Valani . . . kukoma mtima, kudzicepetsa, kufatsa ndi kuleza mtima.”—Akolose 3:12

Anthu akakwatilana amayamba banja latsopano. Ngakhale kuti mudzapitilizabe kukonda makolo anu ndi kuwalemekeza, munthu wofunika kwambili kwa inu tsopano ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Acibale anu ena zingawavute kuvomeleza zimenezi. Koma mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kucita zinthu bwinobwino kuti mukhale mwamtendele ndi acibale anu pamene mukuyesetsanso kulimbitsa ubale wa banja lanu latsopano.

1 PITILIZANI KUONA MOYENELELA ACIBALE ANU

Mwamuna ndi mkazi wake aceza ndi makolo ao

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Uzilemekeza bambo ako ndi mai ako.” (Aefeso 6:2) Zilibe kanthu kuti muli pa msinkhu uti, muyenela kulemekezabe makolo anu. Dziŵaninso kuti naye mnzanu wa m’cikwati ali ndi makolo, ndipo afunika kuwasamalila. Popeza kuti “cikondi sicicita nsanje,” pewani kukalipa mnzanu wa m’cikwati akamaceza ndi acibale ake.—1 Akorinto 13:4; Agalatiya 5:26.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Pewani kulankhula mau monga akuti, “Acibale ako nthawi zonse sandiŵelengela” kapena “Nthawi zonse amai ako sakonda zimene ndimacita”

  • Yesani kuona zinthu mmene mnzanu wa m’cikwati akuzionela

2 KHALANI OSASUNTHIKA NGATI M’POFUNIKA KUTELO

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mai ake n’kudziphatika kwa mkazi wake ndipo io adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Mukaloŵa m’banja, makolo anu angamaone kuti akali ndi udindo wofunika kukusamalilani, ndipo akhoza kumafuna kuloŵelela kwambili m’cikwati canu.

Zili kwa inu ndi mnzanu wa m’cikwati kugwilizana pamene io angalekezele ndipo mungawadziŵitse mwacikondi. Khalani omasuka pokamba nao ndipo musawapite m’mbali koma kambani mwaulemu osati monyoza. (Miyambo 15:1) Kudzicepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima kudzakuthandizani kukhala paubale wabwino ndi acibale anu ndipo mudzapitiliza “kulolelana m’cikondi.”—Ephesians 4:2.

Mwamuna ndi mkazi akuceza; mwamuna ndi mkazi apatsa makolo ao mphatso

ZIMENE MUNGACITE:

  • Ngati mwakhudzidwa kwambili ndi mmene acibale aloŵelela mu umoyo wanu wabanja, kambilanani ndi mnzanu wa m’cikwati mtima ukakhala pansi

  • Kambilanani mmene mungathetsele mavuto amenewa

YESETSANI KUMVETSELA

Mufunika kumvetsela pamene makolo anu afotokoza mmene akumvela ndiponso mmene akuonela zinthu. Pamene akuuzani zinazake safuna kusokoneza ciliconse. Iwo amakukondani kwambili. Makolo anu angavutike kwambili kuti ayambe kukuonani monga banja lodziimila palokha. Iwo angaone monga mwawalekelela. Koma mwa kutsatila mfundo za m’Baibulo ndi kukambilana nao momasuka, mudzapitilizabe kulemekeza makolo anu popanda kusokoneza banja lanu.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • N’cifukwa ciani n’cibadwa kuti makolo a mnzanga amafuna kuloŵelela m’cikwati cathu?

  • Ndingacite bwanji kuti ndiziona mnzanga wa m’cikwati kukhala wofunika kwambili, koma panthawi imodzimodziyo kulemekeza makolo anga?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani