LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od mutu 10 masa. 105-115
  • Njila Zowonjezela Utumiki Wanu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Njila Zowonjezela Utumiki Wanu
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUTUMIKILA MONGA WOFALITSA MUMPINGO
  • KUTUMIKILA KUMALO OSOŴA
  • KULALIKILA M’CINENELO CINA
  • UPAINIYA
  • UMISHONALE
  • NCHITO YA M’DELA
  • MASUKULU A ZAUMULUNGU
  • UTUMIKI WA PA BETELI
  • NCHITO YA MAMANGIDWE
  • KODI MULI NA ZOLINGA ZAUZIMU ZOTANI?
  • Muzikumbukila Amene Ali mu Utumiki Wanthawi Zonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Oyang’anila Oweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od mutu 10 masa. 105-115

MUTU 10

Njila Zowonjezela Utumiki Wanu

NTHAWI itafika yakuti Yesu atumize ophunzila ake kukalengeza za Ufumu, anawauza kuti: “Zokolola n’zoculuka, koma anchito ndi ocepa.” Nchito inalipo yaikulu, conco Yesu anawonjezela kuti: “Pemphani Mwini zokolola kuti atumize anchito kukakolola.” (Mat. 9:37, 38) Yesu anauza ophunzilawo mocitila utumikiwo. Mawu ake anaonetsa kuti nchitoyo inafunika kuigwila mofulumila. Iye anati: “Simudzamaliza kuzungulila mizinda yonse ya Isiraeli Mwana wa munthu asanafike.”—Mat. 10:23.

2 Masiku anonso, pali nchito yaikulu yolalikila yofunika kuigwila. Uthenga wabwino wa Ufumu uyenela kulalikidwa mapeto asanafike, ndipo nthawi ikutha mofulumila! (Maliko 13:10) Popeza kuti mundawo ni dziko lonse, ifenso masiku ano tili na nchito yaikulu monga zinalili kwa Yesu na ophunzila ake. Ndife ocepa kwambili m’ciŵelengelo poyelekezela na mabiliyoni a anthu padziko lapansi. Koma citsimikizo tili naco cakuti Yehova adzatithandiza. Uthenga wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ndipo pa nthawi ya Yehova yoikika, mapeto adzafika. Kodi tidzaika Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wathu kuti tikwanilitse utumiki wathu? Nanga tingadziikile zolinga zotani zauzimu?

3 Pofotokoza zimene Yehova amafuna kwa atumiki ake odzipatulila, Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Tiyenela kutumikila Mulungu na moyo wathu wonse. Polimbika mu utumiki umene Yehova anatipatsa, timaonetsa kuti kudzipatulila kwathu kwa iye kunalidi kocokela pansi pa mtima. (2 Tim. 2:15) Pali mwayi wotitsegukila wa mautumiki osiyana-siyana, malinga na mikhalidwe komanso maluso athu. Onani ena mwa mautumiki amenewo, ndipo sankhani amene mungafune kukacitako pofuna kuwonjezela utumiki wanu.

KUTUMIKILA MONGA WOFALITSA MUMPINGO

4 Aliyense amene analandila coonadi ali na mwayi wolalikila uthenga wabwino. Iyi ndiyo nchito yofunika ngako imene Yesu anapatsa ophunzila ake. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Wophunzila wa Yesu Khristu akangomvela uthenga wabwino, nthawi yomweyo amayamba kuuzako ena. N’zimene anacita Andireya, Filipo, Koneliyo, komanso ena. (Yoh. 1:40, 41, 43-45; Mac. 10:1, 2, 24; 16:14, 15, 25-34) Kodi izi zitanthauza kuti munthu angayambe kuuzako ena za uthenga wabwino ngakhale asanabatizike? Inde! Munthu akangoyenelezedwa kukhala wofalitsa wosabatizika mumpingo, amakhala na mwayi wotengako mbali mu ulaliki wa kunyumba na nyumba. Komanso, malinga na mikhalidwe na maluso ake, palinso mautumiki ena amene angacite.

5 Wofalitsa akabatizika, mosakayikila amakhala wofunitsitsa kucita zonse zotheka kuti athandize ena kudziŵa uthenga wabwino. Onse amuna na akazi ali na mwayi wotengako mbali m’nchito yolalikila. Limakhala dalitso lathu pothandizila ena kupititsa patsogolo Ufumu wa Mulungu. Aliyense amene angacitenso mbali zina zowonjezela utumiki wake adzakhaladi wacimwemwe.

KUTUMIKILA KUMALO OSOŴA

6 Mwina gawo la mpingo wanu limalalikidwa kaŵili-kaŵili, ndipo ambili amakhala na mwayi womvetsela uthenga wabwino. Ngati n’telo, mwina mungaganizile zowonjezela utumiki wanu mwa kusamukila kumalo osoŵa. (Mac. 16:9) Ngati ndinu mkulu kapena mtumiki wothandiza, pangakhale mpingo umene ungayamikile thandizo lanu. Woyang’anila dela wanu angakuunikileni za mmene mungakathandizile mpingo wina m’dela lanu. Ngati mufuna kukatumikila ku dela lina, ofesi ya nthambi ingakuunikileni zofunikila.

7 Kodi mungakonde kukatumikila ku dziko lina? Ngati n’conco, muyenela kuiganizila mosamala nkhaniyo. Kambilanani za nkhaniyo na akulu a mpingo wanu. Kusamukila ku dziko lina kungasinthe zambili kwa inu, na ena amene mungapite nawo. (Luka 14:28) Koma ngati muona kuti simungathe kukakhalako nthawi yaitali kumeneko, cingakhale bwino kungotumikila m’dziko lanu.

8 M’maiko ena, abale omwe amawaseŵenzetsa pa maudindo a oyang’anila ni acatsopano m’coonadi. Abale odzicepetsa a m’maiko otelo, amayamikila kuti akulu acidziŵitso omwe asamukila mu mpingo wawo azitsogolela zinthu. Ngati ndimwe mkulu ndipo muganiza zosamukila ku dziko lotelo, kumbukilani kuti colinga canu si kukatenga maudindo a abale kumeneko ayi. M’malomwake, katumikileni nawo pamodzi. Alimbikitseni kukalamila na kulandila maudindo mumpingo. (1 Tim. 3:1) Khalani woleza mtima ngati zinthu sizicitika mmene zinali kucitikila kwanu. Monga mkulu wodziŵa zambili, ikani mtima wanu pa kuthandiza abale. Ndipo nthawi ikadzafika yobwelela kwanu, akuluwo adzakhala atadziŵa kusamalila bwino mpingo.

9 Ofesi ya nthambi isanakutumizileni maina a mipingo imene ingapindule na thandizo lanu, Komiti Yautumiki ya Mpingo wanu idzafunika kulemba kalata yokuvomelezani. Kalatayo ni yofunika kaya mukutumikila monga mkulu, mtumiki wothandiza, mpainiya, kapena wofalitsa. Komiti Yautumiki idzatumiza kalata yokuvomelezani, pamodzi na pempho lanu ku ofesi ya nthambi ya kudziko limene mufuna kukatumikilako.

KULALIKILA M’CINENELO CINA

10 Kuti muwonjenzele utumiki wanu, mungaganizile zophunzila cinenelo cina, kuphatikizapo cinenelo ca manja. Ngati mufuna kuphunzila kulalikila m’citundu cina, kambilanani na akulu komanso woyang’anila dela wanu. Iwo angakupatseni malangizo othandiza na kukulimbikitsani. Molangizidwa na ofesi ya nthambi, madela ena amakonza makalasi ophunzitsa cinenelo, pofuna kuthandiza ofalitsa komanso apainiya kuti azilalikila m’citundu cina.

UPAINIYA

11 Ofalitsa onse ayenela kudziŵa bwino ziyenelezo za upainiya wothandiza, upainiya wanthawi zonse, upainiya wapadela, komanso mautumiki ena a nthawi zonse. Mpainiya ayenela kukhala Mkhristu wobatizika wacitsanzo cabwino, amene umoyo wake ungamulole kukwanilitsa mlingo wa maola ofunikila polalikila uthenga wabwino. Komiti ya Utumiki ya Mpingo ndiyo imayeneleza apainiya othandiza kapena anthawi zonse. Koma apainiya apadela amaikidwa na ofesi ya nthambi.

12 Ofalitsa angasankhe kucitako upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi, miyezi ingapo, kapena kucita upainiya wothandiza wopitiliza malinga na mikhalidwe pa umoyo wawo. Ofalitsa a Ufumu ambili amakonda kucitako upainiya wothandiza pa zocitika zapadela, monga pa nyengo ya cikumbutso kapena m’mwezi umene wadela akucezela mpingo wawo. Ena amacita upainiya m’miyezi ya chuthi. Ofalitsa obatizika amene amapita ku sukulu, angasankhe kucita upainiya wothandiza akatsekela masukulu. Ofalitsa angaciteko upainiya wothandiza wa maola ocepa m’miyezi ya March na April, komanso m’mwezi umene wadela akucezela mpingo wawo. Mulimonse mmene zingakhalile, ngati muli na makhalidwe abwino ndipo mungakwanitse maola ofunikila, komanso ngati muona kuti mungacite upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena kuposelapo, akulu adzakhala okondwa kulandila pempho lanu kuti mucite utumiki umenewu.

13 Kuti muyenelezedwe kukhala mpainiya wanthawi zonse, muyenela kukhala wokonzeka kukwanilitsa maola ofunikila pacaka. Monga mpainiya wanthawi zonse, muyenela kumalalikila pamodzi na mpingo wanu. Apainiya okangalika amakhala dalitso ku mpingo. Iwo amathandiza ena kukonda utumiki wakumunda, komanso kuwalimbikitsa kucita upainiya. Kuti mufunsile upainiya wanthawi zonse, muyenela kukhala wofalitsa wacitsanzo cabwino, komanso wobatizika kwa miyezi yosacepela 6.

14 Nthawi zambili apainiya apadela amasankhidwa pakati pa apainiya a nthawi zonse, amene ni akhama pa nchito yolalikila. Ayenela kukhala okonzeka kukatumikila kulikonse kumene ofesi ya nthambi ingawatumize. Kambili amawatumiza kumalo akutali kumene angapeze anthu acidwi na kukhazikitsa mipingo yatsopano. Nthawi zina, apainiya apadela amawatumiza ku mipingo imene siikwanitsa bwino kufola gawo lawo lonse. Apainiya apadela ena amenenso ni akulu, amawatumiza kuti akathandize mipingo ing’ono-ing’ono m’mbali zina, ngakhale kuti imatha bwino kufola gawo lawo. Apainiya apadela amalandila alawansi yocepa yowathandiza kupeza zofunika pa umoyo wawo. Ena amaikidwa kukhala apainiya apadela apakanthawi.

UMISHONALE

15 Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulila ndiyo imaika amishonale. Ndiyeno Komiti ya Nthambi ya m’dziko lawo ndiyo imawatumiza kukatumikila ku madela kumene kuli anthu ambili. Iwo amathandiza kwambili pa nchito yolalikila komanso kulimbitsa mipingo. Nthawi zambili, amishonale amakhala amene analoŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Amalandilako alawansi yocepa yowathandiza kupeza zofunika pa umoyo wawo na malo okhala.

NCHITO YA M’DELA

16 Amene Bungwe Lolamulila limawaika kukhala oyang’anila madela, coyamba amaphunzitsidwa nchitoyo na kutumikila monga oyang’anila dela ogwilizila. Abale amenewa amaikonda ngako nchito yolalikila, ndipo amakondanso abale awo. Amakhalanso apainiya okangalika, akhama pa kuŵelenga Baibo, komanso aluso lokamba nkhani na kuphunzitsa. Alinso zitsanzo zabwino pa kuonetsa makhalidwe amene mzimu woyela umabala, amacita zinthu mwacikatikati, ni ololela, komanso ozindikila. Ngati m’bale ni wokwatila, mkazi wake amenenso ni mpainiya, amakhala wacitsanzo cabwino pa makhalidwe, komanso pocita zinthu na ena. Nayenso amakhala mlaliki wogwila mtima. Amakhalanso mkazi wogonjela, osati wokonda kulankhula motsogolela mwamuna wake, kapena wokonda kupondeleza anzake pamakambilano. Oyang’anila madela pamodzi na akazi awo amakhala na zocita zambili. Conco, amene afuna utumiki umenewu ayenela kukhala a thanzi lolimba. Apainiya sacita kufunsila ku ofesi nchito ya m’dela. Amadziŵitsa woyang’anila dela colinga cawo cofuna kukatumikila m’dela, ndiyeno iye amawalangiza zocita.

MASUKULU A ZAUMULUNGU

17 Sukulu ya Alengezi a Ufumu: Pakufunikila alengezi a Ufumu ambili kuti akafole magawo amene salalikidwa kaŵili-kaŵili, komanso kuti akalimbikitse mipingo kuuzimu. Conco, abale na alongo amene ni mbeta, komanso aja ali pabanja, angafunsile kuloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu kuti akalandile maphunzilo apadela. Akamaliza maphunzilo amenewo, amatumizidwa monga apainiya a nthawi zonse ku madela kumene alaliki ni ocepa m’dziko lawo. Komabe, enanso angapatsidwe mautumiki ena m’dziko lawo kapena ku dziko lina, malinga na kudzipeleka kwawo. Ena ocepa angatumizidwe monga apainiya apadela apakanthawi kapena acikhalile. Apainiya ofuna kuloŵa sukulu imeneyi amauzidwa zofunikila pamiting’i imene imakhalapo pa msonkhano wacigawo.

18 Sukulu ya Giliyadi: Amene amasankhidwa kukaloŵa sukulu imeneyi, amakhala abale na alongo amene ni mbeta, komanso amene ali pabanja, amene amadziŵa Cizungu, komanso amakhala atumiki anthawi zonse apadela. Amakhalanso aja amene ali nako kuthekela kolimbitsa mipingo na kuthandiza kuti nchito ziziyenda bwino pa ofesi ya nthambi. Amakhala ataonetsa kale mtima wokonda kutumikila abale awo, ndipo angathandize ena mokoma mtima kuphunzila na kutsatila mfundo za m’Baibo, na zitsogozo za gulu la Mulungu. Komiti ya Nthambi ndiyo imapempha awo oyenelela kuti alembe fomu yofunsila mwayi wokaloŵa sukulu imeneyi. Otsiliza sukuluyi amatumizidwa kukatumikila ku mipingo kapena pa ofesi ya nthambi ya ku dziko lina, kapena ya m’dziko lawo.

UTUMIKI WA PA BETELI

19 Kutumikila pa Beteli ni mwayi wapadela. Dzina lakuti Beteli limatanthauza kuti “Nyumba ya Mulungu.” Ndipo dzinali n’loyenelela cifukwa malowo ndiwo pa mcombo, kapena kuti malo apakati, a nchito zaumulungu. Abale na alongo otumikila pa Beteli amagwila nchito zofunika ngako, monga kulemba mabuku ophunzitsa Baibo, kuwamasulila, na kuwafalitsa. Utumiki wawo ni wofunika kwambili ku Bungwe Lolamulila, limene limayang’anila na kupeleka citsogozo ku mipingo yonse zungulile dziko lapansi. Atumiki a pa Beteli ambili ogwila nchito yomasulila amakhala kumadela a cinenelo cimene amamasulila. Izi zimawathandiza kumva mmene anthu amacikambila citunduco. Amatha kuonanso ngati anthu amamvetsa bwino mawu amene amalembedwa m’zofalitsa zathu.

20 Nchito zambili pa Beteli zimafuna nyonga. Pa cifukwa cimeneci, ambili amene amaitanidwa kukatumikila pa Beteli amakhala abale acinyamata odzipeleka komanso obatizika, athanzi lolimba komanso anyonga. Ngati ku ofesi yanu ya nthambi kukufunikila anchito, ndipo mufuna kukatumikila pa Beteli, funsani zofunikila kwa akulu mumpingo wanu.

NCHITO YA MAMANGIDWE

21 Nchito yomanga malo olambilila nayonso ni utumiki wopatulika, monga mmene inalili nchito yomanga kacisi wa Solomo. (1 Maf. 8:13-18) Abale na alongo ambili amaonetsa cangu cawo pogwilitsila nchito nthawi yawo na cuma cawo kucilikiza nchito ya mamangidwe.

22 Kodi mmene umoyo wanu ulili mungathandize pa nchito imeneyi? Ngati ndimwe wofalitsa wobatizika ndipo mufuna kutengapo gawo pa utumiki umenewu, abale oyang’anila nchito ya mamangidwe kudela lanu angayamikile thandizo lanu, ndipo ni okonzeka kukuphunzitsani nchitoyo ngakhale kuti mulibe maluso. Ngati cifuno muli naco, bwanji osawadziŵitsa akulu kuti mpata muli nawo wothandiza pa nchito imeneyi? Ofalitsa ena obatizika oyenelela utumiki umenewu adzipeleka kukatumikila ngakhale ku maiko ena pa nchito ya mamangidwe imeneyi.

23 Mipata ilipo yambili yotengako mbali m’nchito ya mamangidwe. Ofalitsa obatizika a citsanzo cabwino odziŵa nchito, angathandizeko pa nchito za mamangidwe kufupi na kwawo. Amenewo angatumikile monga odzipeleka a Dipatimenti ya Mapulani na Mamangidwe (LDC). Ena amasankhidwa na ofesi ya nthambi kukathandiza pa nchito za mamangidwe kutali na kwawo kwa nthawi yocepa, mwina milungu iŵili mpaka miyezi itatu. Amenewa amachedwa othandizila pa nchito ya mamangidwe. Amene amasankhidwa kutumikila kwa nthawi yaitali amachedwa atumiki anchito ya mamangidwe. Mtumiki wa nchito ya mamangidwe amene watumizidwa kukatumikila ku dziko lina amachedwa mtumiki wanchito ya mamangidwe wocokela ku dziko lina. Kagulu ka Mamangidwe kamapangidwa na atumiki anchito ya mamangidwe, komanso othandizila panchito ya mamangidwe. Awa ndiwo amatsogolela panchito ya mamangidwe iliyonse, ndipo amathandizidwa na othandizila a mu Dipatimenti ya Mapulani na Mamangidwe, komanso abale na alongo ocokela m’mipingo yapafupi. Tumagulu twa Mamangidwe tukamaliza cimango tumasamukilanso kunchito ina m’gawo la nthambi yawo.

KODI MULI NA ZOLINGA ZAUZIMU ZOTANI?

24 Ngati munapatulila moyo wanu kwa Yehova, colinga canu n’ca kumutumikila kwamuyaya. Koma kodi zolinga zanu zina zauzimu n’zotani? Kukhala na zolinga zauzimu kudzakuthandizani kuseŵenzetsa mphamvu zanu na cuma canu mwanzelu. (1 Akor. 9:26) Kudziikila zolinga zotelo kudzakuthandizani kukula kuuzimu, komanso kuika maganizo anu pa zinthu zofunika kwambili pamene mukukalamila mautumiki ena owonjezeleka.—Afil. 1:10; 1 Tim. 4:15, 16.

25 Mtumwi Paulo anatisiila citsanzo cabwino cimene tingatengele mu utumiki wathu kwa Mulungu. (1 Akor. 11:1) Iye anadzipeleka molimbika potumikila Yehova. Anazindikila kuti Yehova anam’patsa mwayi wa mautumiki ambili. Kwa abale a ku Korinto, Paulo analemba kuti: “Khomo lalikulu la mwayi wautumiki landitsegukila.” Kodi si zoona kuti ifenso khomo la mwayi wa mautumiki n’lotitsegukila? Inde, pali mwayi wa mautumiki olekana-lekana otumikila Yehova mumpingo, maka-maka m’nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Koma monga zinalili kwa Paulo, kuloŵa “pakhomo lalikulu” limenelo kumafuna kulimbana na “otsutsa ambili.” (1 Akor. 16:9) Paulo anali kumadziwongolela ngakhale iye mwini. N’cifukwa cake anakamba kuti: “Ndikumenya thupi langa.” (1 Akor. 9:24-27) Kodi nafenso timatelo?

Kukhala na zolinga zauzimu kudzakuthandizani kuseŵenzetsa mphamvu zanu na cuma canu mwanzelu

26 Aliyense ayenela kulimbikila kuti akakwanilitse zolinga zake zauzimu malinga na mmene zinthu zili pa umoyo wake. Ambili ali mu utumiki wanthawi zonse cifukwa anadziikila zolinga zauzimu akali acicepele. Pamene anali ana, analimbikitsidwa zimenezo na makolo awo komanso anthu ena. Conco, iwo akusangalala mu utumiki wawo kwa Yehova, ndipo sanadzigwilitse mwala. (Miy. 10:22) Mungadziikilenso zolinga zina monga kumapita mu ulaliki mlungu uliwonse, kupeza phunzilo la Baibo la panyumba, kapena kupatula nthawi yomakonzekela bwino misonkhano. Cacikulu ni kukhala olimbikabe pa utumiki wathu. Tikacita zimenezo, tidzalemekeza Yehova na kukwanilitsa colinga cathu cacikulu kopambana, copitilizabe kutumikila Mulungu mpaka muyaya.—Luka 13:24; 1 Tim. 4:7b, 8.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani