NYIMBO 126
Khalani Maso, Cilimikani, Khalani Amphamvu
Yopulinta
	- 1. Khalani ocilimika, - Ndipo khalani maso. - Mukhale olimba mtima, - Inu mudzapambana. - Timvela lamulo la Yesu; - Timaima ku mbali yake. - (KOLASI) - Tiyeni’fe tikhale maso - Mpaka cabe mapeto! 
- 2. Tetezani maganizo, - Khalanibe omvela. - Tsatilani malangizo - A Yesu Khristu Mfumu. - Mvelani akulu mu mpingo - Amene amatiteteza. - (KOLASI) - Tiyeni’fe tikhale maso - Mpaka cabe mapeto! 
- 3. Tikhale ogalamuka, - Ndipo tigwilizane. - Olo adani atsutse - Tidzalalikilabe. - Timutamande M’lungu wathu; - Tsiku lake layandikila. - (KOLASI) - Tiyeni’fe tikhale maso - Mpaka cabe mapeto! 
(Onaninso Mat. 24:13; Aheb. 13:7, 17; 1 Pet. 5:8.)