NYIMBO 28
Kukhala Bwenzi la Yehova
Yopulinta
	(Salimo 15)
- 1. Ndani angakhale - Bwenzi lanu M’lungu? - Ndani mungakhulupilile? - Angakudziŵeni? - Ni uja amene - Amakumvelani. - Komanso wokhulupilika, - Wokonda co’nadi. 
- 2. Ndani angakhale - Bwenzi lanu M’lungu? - Ndani amene mungakonde - Nakumudalitsa? - Ni uja amene - Amakukwezani. - Iye amanena zoona, - Ni woona mtima. 
- 3. Nkhawa zathu zonse - Timakuuzani. - Ndipo mumatisamalila, - Tsiku lililonse. - Tifuna kukhala - Bwenzi lanu M’lungu. - Palibe bwenzi tingapeze - Monga inu M’lungu. 
(Onaninso Sal. 139:1; 1 Pet. 5:6, 7.)