NYIMBO 106
Kukulitsa Mkhalidwe wa Cikondi
Yopulinta
1. Tithandizeni kuonetsa
Makhalidwe anu abwino.
Koposa zonse tionetse
Cikondi kwa abale athu.
Ngati cikondi cazilala,
Inu Yehova simukondwa.
Tionjezeleni cikondi,
Nthawi zonse ticionetse.
2. Cikondi cimatipangitsa
Kuti tiganizile ena.
Tikhululukila anzathu,
Monga Yesu anakambila.
Cikondi cimatithandiza
Kupilila pamayeselo.
Cikondi cipilila zonse
Cikondi sicidzalephela.
(Onaninso Yoh. 21:17; 1 Akor. 13:13; Agal. 6:2.)