NYIMBO 115
Tiyamikila Kuleza Mtima kwa Mulungu
Yopulinta
(2 Petulo 3:15)
1. O Yehova, wamphamvuzonse,
Mumakonda cilungamo.
Zoipa pano padziko
M’lungu wathu zaculuka.
Koma tidziŵa simucedwa;
Mudzazicotsapo zoipa.
(KOLASI)
Yehova tiyamikila,
Kuti ndinu woleza mtima.
2. Zaka cikwi kwa inu M’lungu
Ni tsiku limodzi cabe.
Tsiku lanu lalikulu;
Posacedwa lidzafika.
Inu simukonda zoipa,
Koma mufuna ‘nthu alape.
(KOLASI)
Yehova tiyamikila,
Kuti ndinu woleza mtima.
(Onaninso Neh. 9:30; Luka 15:7; 2 Pet. 3:8, 9.)