NYIMBO 100
Alandileni na Manja Aŵili
Yopulinta
1. Yehova amatilandila bwino.
Amasamalila mosakondela.
Mvula imagwabe,
dzuŵa imawala;
Amatipatsanso cakudya.
Pamene tithandiza ovutika,
Timatengela citsanzo ca M’lungu.
Ngati tionetsa
cifundo kwa ena,
Yehova adzatidalitsa.
2. Pothandiza ena sitingadziŵe
Zabwino zimene tingalandile.
Ngakhale amene
sitimaŵadziŵa
Tifunika kuŵathandiza.
Monga Lidiya tiziŵalandila,
Akabwela tiziŵatsitsimula.
Atate Yehova
amaona onse
Ocitila ena cifundo.
(Onaninso Mac. 16:14, 15; Aroma 12:13; 1 Tim. 3:2; Aheb. 13:2; 1 Pet. 4:9.)