NYIMBO 47
Pemphela kwa Yehova Tsiku na Tsiku
Yopulinta
(1 Atesalonika 5:17)
1. Pemphelani kwa Yehova M’lungu.
Iye amamvela mapemphelo.
Muuzeni za mumtima mwanu.
Monga bwenzi lathu amamvela.
Pemphelani kwa M’lungu.
2. Tipemphele kwa Yehova M’lungu,
Tiyamikile mphatso ya moyo.
Timupemphe cikhululukilo.
Adziŵa kuti ndise ofo’ka.
Pemphelani kwa M’lungu.
3. Pemphelani kwa Yehova M’lungu,
Pamene imwe muli na vuto.
Ni Atate wathu wacifundo.
Iye adzakusamalilani.
Pemphelani kwa M’lungu.
(Onaninso Sal. 65:5; Mat. 6:9-13; 26:41; Luka 18:1)