NYIMBO 39
Tipange Dzina Labwino na Mulungu
Yopulinta
(Mlaliki 7:1)
1. Timayesetsa tsiku lililonse,
Kupanga dzina labwino na M’lungu.
Tikapitiliza kumvela Yehova,
Tikondweletsa mtima wake.
2. Kukondetsetsa zinthu za m’dzikoli,
Kufunitsitsa kuti tilemele,
Kulibe ubwino, tingasiye M’lungu.
Sangatipatse madalitso.
3. Tifuna M’lungu atilembe dzina,
Kuti tikhale mu buku la moyo.
Lomba ndiye nthawi yakuti tipange
Dzina labwino na Yehova.
(Onaninso Gen. 11:4; Miy. 22:1; Mal. 3:16; Chiv. 20:15.)