LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Kuŵaŵa Kwa Imfa
    Galamuka!—2018 | No. 3
    • Mwamuna wofedwa wakhala payekha mu lesitilanti

      THANDIZO KWA OFEDWA

      Kuŵaŵa Kwa Imfa

      “Tinali titakhala m’cikwati kwa zaka zopitilila 39, pamene mkazi wanga Sophiaa anamwalila pambuyo podwala kwa nthawi yaitali. Anzanga ananithandiza kwambili, ndipo n’nali kudzitangwanitsa na zocita zambili. Koma kwa caka conse, n’navutika kwambili na cisoni. N’nali kuti nikakhalako bwino kwa kanthawi, cisoni n’kunibwelelanso. Ngakhale kuti papita zaka pafupi-fupi zitatu kucokela pamene anamwalila, nthawi zina nimagwidwa na cisoni kwambili.”—Kostas.

      Kodi munataikilidwapo wokondedwa wanu mu imfa? Ngati munataikilidwapo, mungavomeleze zimene Kostas anakamba. Imfa ya mnzako wa m’cikwati, m’bululu wako, kapena mnzako wapamtima, imavutitsa kwambili maganizo na kuŵaŵitsa mtima. Ngakhale akatswili ofufuza za anthu ofedwa amavomeleza mfundo imeneyi. Nkhani ya m’magazini yakuti, The American Journal of Psychiatry, imati “imfa ni yoŵaŵa kwambili ndipo imabweletsa cisoni cosathelapo.” Cifukwa ca cisoni cacikulu ca imfa, munthu wofedwa angafunse kuti: ‘Kodi cisoni cimeneci cidzatha liti? Kodi nidzakhalanso wacimwemwe? Kodi ningapeze kuti citonthozo?’

      Mudzapeza mayankho pa mafunso amenewa m’magazini ino ya Galamuka! Nkhani yotsatila idzafotokoza zimene mungayembekezele ngati posacedwa wokondedwa wanu anamwalila. Ndipo nkhani zina zokonkhapo zidzafotokoza njila zimene zingakuthandizeni kucepetsako cisoni mukafedwa.

      Tikhulupilila kuti nkhani zotsatila zidzathandiza aliyense amene anataikilidwa wokondedwa wake mu imfa.

      a Maina ena m’nkhani za m’magazini ino asinthidwa.

  • Zimene Mungayembekezele
    Galamuka!—2018 | No. 3
    • Makolo ofedwa

      THANDIZO KWA OFEDWA

      Zimene Mungayembekezele

      Ngakhale kuti akatswili ena amati pali njila imodzi yolilila malilo, m’ceni-ceni anthu amalila mosiyana-siyana. Kodi izi zitanthauza kuti ena sakhudzidwa kwambili na imfa, kapena “amabisa” mmene amamvelela? Osati kweni-kweni. Ngakhale kuti kuivomeleza imfa komanso kulila n’kothandiza, palinso zina zothandiza zimene mungacite. Kweni-kweni zimadalila cikhalidwe ca munthu, umunthu wake, zom’citikila mu umoyo, komanso mmene wakhudzidwila na imfa imeneyo.

      KODI CISONI CINGAKHALE CACIKULU BWANJI?

      Ofedwa sangadziŵe zoyembekezela munthu amene amam’konda akamwalila. Komabe, mmene angamvelele komanso zovuta zina zimene zingakhalepo, nthawi zambili zimakhala zodziŵikilatu. Ganizilani zitsanzo izi:

      Kuthedwa nzelu. Munthu wofedwa amalila cifundo cikamugwila, kuyewa wokondedwa wake, kapenanso kukhumudwa-khumudwa. Ndipo kulota zocitika zokhudza wokondedwa wake komanso kum’ganizila kwambili kungawonjezelenso cisoni cake. Koma cinthu coyamba cingakhale kudabwa na kusakhulupilila. Tiina akumbukila mmene zinalili pamene mwamuna wake Timo, anamwalila mwadzidzidzi. Iye anati: “N’nadabwa. Poyamba n’nalephela ngakhale kulila. N’navutika kwambili maganizo cakuti nthawi zina n’nali kulephela kufuza bwino-bwino. Sin’nakhulupilile zimene zinacitika.”

      Nkhawa, ukali, na kudziimba mlandu. Ivani anati: “Kwa nthawi ndithu, mwana wathu wamwamuna Eric wa zaka 24 atamwalila, ine na mkazi wanga Yolanda, tinali kukhala okwiya kwambili! Izi zinatidabwitsa, cifukwa kumbuyo konseko sitinakhalepo okwiya conco. Tinalinso kudziimba mlandu, cifukwa tinali kukaikila ngati tinacita zonse zotheka kuti tithandize mwana wathu.” Nayenso Alejandro, amene mkazi wake anamwalila pambuyo podwala kwa nthawi yaitali, anali kudziimba mlandu. Iye anati: “Poyamba n’naganiza kuti ngati Mulungu walola kuti nivutike conco, ndiye kuti ndine munthu woipa m’maso mwake. N’nadziimbanso mlandu cifukwa coona monga nipatsa mlandu Mulungu pa zimene zinacitika.” Kostas amene tam’gwila mawu m’nkhani yapita, anati: “Nthawi zina n’nali kukwiila Sophia cifukwa comwalila. Ndiyeno n’nadziimbanso mlandu cifukwa cokhala na maganizo amenewo. Sanacite kufuna kuti amwalile.”

      Maganizo ovutitsa. Nthawi zina maganizo a munthu wofedwa sakhadzikika, amangoyenda-yenda. Mwacitsanzo, wofedwa angayambe kuganiza kuti wokondedwa wake amene anamwalila ca posacedwa, angamvetsele, kukhudzika mtima, komanso kuona. Mwina wofedwayo angavutike kuika maganizo pa cinthu cimodzi kapena kukumbukila zinthu. Tiina anakamba kuti: “Nthawi zina, nili mkati mokambilana na munthu, maganizo anga anali kucoka pa nkhaniyo! N’nali kuyamba kuganizila zimene zinacitika pa kumwalila kwa a Timo. Zimenezi zinali kunisautsa kwambili.”

      Kufuna kukhala kwa yekha. Munthu wofedwa angakhale wokhumudwa-khumudwa komanso angamaipidwe kukhala pakati pa anthu. Kostas anati: “Nikakhala pakati pa okwatilana, n’nali kudzimva kuti nili nekha. Ndipo nikakhala pakati pa osakwatila n’nali kudzimvanso wosayenelela.” Nayenso Yolanda mkazi wa Ivan, amakumbukila mmene zinalili. Iye anati: “Zinali zovuta kukhala pakati pa anthu amene anali kudandaula za mavuto awo amene anali kuoneka ocepa poyelekezela na athu! Ndiyeno panalinso ena amene anali kutiuza mmene ana awo acitila bwino. N’nali kukondwela nawo, koma panthawi imodzi-modzi, sin’nali kufuna kumvela zimenezo. Ine na mwamuna wanga tinali kumvetsa kuti umoyo ndiye mmene ulili, koma tinali kufuna kukhala patekha cifukwa ca makambilano otelo.”

      Mavuto okhudza thanzi. Mavuto ena odziŵikilatu amakhala kusafuna kudya, kuyonda, komanso kusoŵa tulo. Aaron amakumbukila mmene zinthu zinalili caka cotsatila kucokela pamene atate ake anamwalila. Iye anati: “N’nali kuvutika kugona. Nthawi zonse usiku, n’nali kuuka panthawi imodzi-modzi kuganizila za imfa ya atate.”

      Alejandro akumbukila kuti anayamba kudwala matenda osadziŵika bwino. Iye anati: “Kangapo konse adokota ananipima, koma ananiuza kuti nili bwino-bwino. N’nayamba kuona kuti cisoni ndiye cinali kupangitsa zimenezo.” M’kupita kwa nthawi n’nayamba kumvelako bwino. Koma Alejandro anacitabe bwino kukaonana na adokota. Cisoni cikakula kwambili cingacepetse mphamvu yacitetezo ca m’thupi, cingakulitse matenda, kapena kuyambitsanso matenda ena.

      Kulephela kucita zinthu zofunika. Ivan anati: “Eric atamwalila tinadziŵitsa abululu athu, mabwenzi, abwana ake, komanso a landilodi ake. Panalinso mapepa ambili a ku boma amene tinafunika kusaina, komanso kuona zinthu zaumwini za Eric. Kuti zonsezo zitheke, tinafunika kuika maganizo pa zimene tinali kucitazo. Koma panthawi imodzi-modzi, tinali olefuka maganizo komanso thupi.”

      Koma kwa ena, vuto imadzabwela pakapita nthawi, pofuna kucita zinthu zimene mnzawo anali kucita. Ni mmenenso zinalili kwa Tiina. Iye anafotokoza kuti: “Nthawi zonse a Timo ndiye anali kusamalila za kasungidwe ka ndalama kubanki, komanso kucita zinthu zina zokhudza bizinesi. Tsopano zonsezi zinakhala udindo wanga, ndipo zinangowonjezela kupanikizika kwanga maganizo. N’nadzifunsa kuti, kodi nidzakwanitsa kucita zonsezi popanda kusokoneza?”

      Mavuto amene tafotokoza pamwambapa, aonetsa kuti kupilila cisoni cobwela na imfa, kumakhala kovuta kwambili. Ndipo kukamba zoona, cisoni cimene cimakhalapo tikatayikidwa munthu amene tinali kum’konda, cingakhale cacikulu kwambili. Kudziŵilatu zimenezi, kungathandize amene anafedwa caposacedwa kupilila cisoni. Komanso kumbukilani kuti si onse ofedwa amene amakhudzidwa na zovuta zonse zimene zimabwela cifukwa ca imfa. Kuwonjezela apo, ofedwa angatonthozedwe kudziŵa kuti kumva cisoni cifukwa ca imfa n’cibadwa.

      KODI NIDZAKHALANSO WACIMWEMWE?

      Zimene mungayembekezele: Munthu akafedwa cisoni cimakhala cacikulu poyamba. Koma m’kupita kwa nthawi cimayamba kucepako. Izi sizitanthauza kuti cisonico “cimasililatu,” kapena munthuyo amaiŵalilatu za wokondedwa wake ayi. Nthawi zina cisoni cingabwelenso mwadzidzidzi pokumbukila zocitika zina, monga pa tsiku limene anakwatilana kapena limene wokondedwa wawo anamwalila. Koma m’kupita kwa nthawi, ambili amafika pokhazikika maganizo na kuyambanso kuika maganizo pa zocitika za tsiku na tsiku za mu umoyo. Izi zimatheka maka-maka ngati wofedwayo athandizidwa na acibululu, mabwenzi, komanso ngati acita zinthu zom’thandiza kupilila.

      Kodi cisoni cingakhale kwa nthawi yaitali bwanji? Kwa ena, cisoni cimeneci cimakhala kwa miyezi cabe. Koma kwa ambili, caka cimodzi kapena ziŵili zingapitepo asanayambe kumvelako bwino. Ndipo ena zingatenge nthawi yaitali.a Alejandro anati: “Ine cisoni canga cinakhala pafupi-fupi zaka zitatu.”

      Dzilezeleni mtima. Muzicita zimene mungakwanitse patsiku osati modzikakamiza, ndipo dziŵani kuti kumvela cisoni cifukwa ca imfa si kwa muyaya. Koma ngakhale n’conco, kodi pali zimene mungacite kuti mucepetse cisoni palipano, na kuti cisakhale kwa nthawi yaitali?

      a Anthu ena ocepa angakhale na cisoni cacikulu kwambili ndipo cingatenge nthawi yaitali. Cisoni cimeneci cimachedwa cisoni “cocolowana” kapena “cokhalitsa.” Anthu aconco angafunikile kukaonana na madokota opeleka cithandizo kwa anthu ovutika maganizo.

      Kumva cisoni cifukwa ca imfa n’cibadwa

  • Zimene Mungacite Palipano Mukafedwa
    Galamuka!—2018 | No. 3
    • Anthu ali kumbali kwa nyanja aulutsa kaiti na kukopa masinapu

      THANDIZO KWA OFEDWA

      Zimene Mungacite Palipano Mukafedwa

      Ngati mungafufuze malangizo a mmene mungapililile cisoni, mwacionekele mudzapeza mfundo zambili-mbili, zina zothandiza kwambili kuposa zina. Ndipo zili conco cifukwa anthu amalila malilo mosiyana-siyana, monga mmene takambila kale. Zimene zingakhale zothandiza kwa munthu wina sizingakhale zothandiza kwa wina.

      Ngakhale n’conco, pali mfundo zina zimene zakhala zothandiza kwa anthu ambili. Kaŵili-kaŵili, alangizi a anthu ofedwa amalimbikitsa mfundo zimenezi, ndipo zimagwilizana na mfundo zimene sizisintha, zopezeka m’buku yakale ya nzelu, Baibo.

      1: LANDILANI THANDIZO KWA ACIBULULU NA MABWENZI

      • Anthu ali kumbali kwa nyanja aulutsa kaiti na kukopa masinapu

        Akatswili ena amaona kuti njila imeneyi ni yothandiza kwambili kuti munthu apilile cisoni. Koma nthawi zina, mungafune kukhala pamwekha. Mwina mungafike pokwiila amene akuyesa kukuthandizani. Izi zisakudabwitseni. Nthawi zambili ndiye mmene zimakhalila.

      • Musaganize kuti nthawi zonse mufunika kukhala pakati pa anthu, komanso musawaletse kukufikilani. Ndipo mwina mukhoza kukafuna thandizo lawo kutsogolo. Mokoma mtima, adziŵitseni zimene mufuna palipano, komanso zimene simufuna.

      • Malinga na zimene mufunikila, gaŵani bwino nthawi yokhala na anthu ena komanso yokhala pamwekha.

      MFUNDO YAKE: “Aŵili amaposa mmodzi . . . Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.”—Mlaliki 4:9, 10.

      2 Muzidya Zakudya Zopatsa Thanzi, Komanso Muzicita Maseŵela Olimbitsa Thupi

      • Kudya zakudya zopatsa thanzi kudzakuthandizani kugonjetsa nkhawa imene imakhalapo popilila cisoni. Muzidya zipatso zosiyana-siyana, ndiyo zamasamba, komanso zakudya zopanda mafuta kwambili.

      • Muzimwa madzi kwambili komanso zakumwa zina zopatsa thanzi.

      • Ngati mulibe cifuno cakudya mokwanila, mungamadye cakudya cocepa pafupi-fupi. Mungafunsenso adokota zakudya zina zopatsa thanzi.a

      • Kuyenda ndawala na kucita maseŵela ena olimbitsa thupi, kungakuthandizeni kucepetsa maganizo olefula. Kwa ena, maseŵela olimbitsa thupi amawathandiza kuvomeleza kusintha kwa zinthu mu umoyo wawo. Koma kwa ena amawathandiza kuti asamangoganizila za imfa ya wokondedwa wawo.

      MFUNDO YAKE: “Pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.”—Aefeso 5:29.

      3: MUZIGONA MOKWANILA

      • Bedi

        Kugona n’kofunika kwambili, maka-maka kwa ofedwa, popeza cisoni cimalefula kwambili.

      • Pewani kumwa zakumwa za caffeine monga khofi, komanso kumwa moŵa kwambili. Cifukwa izi zingakusonezeni tulo.

        MFUNDO YAKE: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwila nchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 4:6.

      4: SEŴENZETSANI NJILA ZOTHANDIZA KWA IMWE

      • Mkazi wofedwa afotokozelako mnzake za kukhosi

        Kumbukilani kuti anthu amalila malilo mosiyana-siyana. Conco, mudzafunika kusankha mfundo zimene zingakhale zothandiza kwa imwe.

      • Ambili amaona kuti kufotokozela anzawo mmene amvelela, kumawathandiza kupilila imfa. Koma ena amaona kuti ni bwino kusafotokozela anzawo. Akatswili ali na maganizo osiyana-siyana pa nkhani imeneyi. Akatswili ena amakhulupilila kuti kufotokozela ena mmene umvelela n’kothandiza, pamene ena amati n’kosathandiza. Ngati mufuna kufotokozelako wina mmene mumvelela, koma musoŵa poyambila, mwina mungayambe kuuzako bwenzi lanu lapamtima zinthu zocepa.

      • Anthu ena amaona kuti kulila kumawathandiza kupilila cisoni. Koma ena amapilila ngakhale kuti salila kwambili.

      MFUNDO YAKE: “Mtima umadziŵa kuŵaŵa kwa moyo wa munthu.”—Miyambo 14:10.

      5: PEWANI ZIZOLOŴEZI ZOKUWONONGANI

      • Mwamuna akumwa moŵa

        Ofedwa ena pofuna kucepetsako cisoni, amamwa moŵa mopitilila malile kapena kuseŵenzetsa amkola bongo. “Kuiŵalako” mavuto mwa njila imeneyi n’kudziwononga. Ndipo kumvelako bwino kumene munthu angapeze n’kwa kanthawi. Koma zotulukapo zake zingabweletse mavuto aakulu. Conco, pofuna kucepetsako cisoni seŵenzetsani njila zimene sizingakuwonongeni.

      MFUNDO YAKE: “Tiyeni tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi.”—2 Akorinto 7:1.

      6: MUZISEŴENZETSA BWINO NTHAWI YANU

      • Ambili amapeza kuti kucita zinthu zina kumawathandiza kucepetseko cisoni cawo.

      • Mungapezeko citonthozo mwa kupanga mabwenzi atsopano kapena kulimbitsa maubwenzi amene alipo kale, kuphunzila maluso atsopano, kapena kucitako zosangalatsa.

      • M’kupita kwa nthawi zinthu zingasinthe. Mudzaona kuti pang’ono-m’pang’ono mudzayamba kutenga nthawi yaitali simukuganizila za imfa ya wokondedwa wanu. Umu ni mmene munthu amafikila pocila ku cisoni.

      MFUNDO YAKE: “Ciliconse cili ndi nthawi yake, . . . nthawi yolila ndi nthawi yoseka. Nthawi yolila mofuula ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.”—Mlaliki 3:1, 4.

      7: PITILIZANI KUTSATILA PULOGILAMU YANU YA ZOCITA

      • Mkazi aseŵenzetsa kalenda popanga pulogilamu yake ya zocita

        Mwamsanga, yambaninso kucita zinthu zimene munali kucita tsiku na tsiku.

      • Ngati mutsatila pulogilamu yanu monga kugwila nchito, nthawi yogona, na zocita zina, mwacionekele zinthu zidzakhalanso m’malo mwake.

      • Kukhala wotangwanika na zinthu zabwino kudzakuthandizani kucepetsa cisoni canu.

      MFUNDO YAKE: “Zoŵaŵa za pamoyo wake waufupi sazizikumbukila kaŵilikaŵili, cifukwa Mulungu woona akucititsa kuti mtima wake uzisangalala.” —Mlaliki 5:20.

      8: PEWANI KUPANGA ZOSANKHA ZIKULU-ZIKULU MWAMSANGA

      • Ambili amene amapanga zosankha zikulu-zikulu mwamsanga pambuyo pakuti wokondedwa wawo wamwalila, amadziimba mlandu pambuyo pake.

      • Ngati n’kotheka, yembekezelani kwa kanthawi musanapange cosankha cokuka, kusintha nchito, kapena kutaya zinthu zina za wokondedwa wanu.

      MFUNDO YAKE: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulila, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.”—Miyambo 21:5.

      9: MUZIM’KUMBUKILA WOKONDEDWA WANU

      • Mwamuna aonetsa anzake masinapu a mkazi wake amene anamwalila

        Ofedwa ambili apeza kuti n’kothandiza kucita zinthu zimene zimapangitsa kuti azikumbukila wokondedwa wawo amene anamwalila.

      • Mungapeze citonthozo mwa kusunga masinapu, kapena zinthu zina zokukumbutsani wokondedwa wanu. Mungakhalenso na kabuku kolembamo zocitika na nkhani zina zimene mungafune kuti muzizikumbukila.

      • Sungani zinthu zimene zingakukumbutseni zocitika zosangalatsa, kuti muziziona mukafuna kutelo.

      MFUNDO YAKE: “Kumbukilani masiku akale.”—Deuteronomo 32:7.

      10: PEZANI NTHAWI YOCITA ZOSANGALATSA

      • Mwina mungatenge chuti.

      • Ngati n’zosatheka kutenga chuti ca nthawi yaitali, mwina mungaciteko zinthu zina zosangalatsa kwa tsiku limodzi kapena aŵili. Mwacitsanzo, mungapite kokayenda, kukaona malo osungilako zinthu zakale, kapena kuyendetsa motoka.

      • Kucita zinthu zina zosiyanako na zimene mumacita tsiku na tsiku, olo mwacidule, kungakuthandizeni kupilila cisoni.

      MFUNDO YAKE: “Inuyo bwelani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.”—Maliko 6:31.

      11: MUZITHANDIZA ENA

      • Mzimayi wacitsikana athandiza mzimayi wacikulile kugula zinthu

        Kumbukilani kuti nthawi iliyonse imene mungapatule kuthandiza ena, na imwe ingakuthandizeni kuti mumveleko bwino.

      • Mungayambe mwa kuthandiza amene akhudzidwa na imfa ya wokondedwa wanu, monga mabwenzi, kapena acibululu amene angafune wolila naye

      • Kuthandiza ena na kuwatonthoza kungakupangitseni kukhalanso wacimwemwe, komanso kuona kuti moyo wanu uli na phindu.

      MFUNDO YAKE: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” —Machitidwe 20:35.

      12: YANG’ANANINSO ZOCITA ZANU KUTI MUONE ZOFUNIKA KWENI-KWENI

      • Nthawi yolila ingakuthandizeni kuzindikila zinthu zofunika kwambili.

      • Tengelamponi mwayi wodzifufuza kuti muone mmene museŵenzetsela umoyo wanu.

      • Sinthani zina mwa zimene mumacita ngati m’pofunika kutelo.

      MFUNDO YAKE: “Ndi bwino kupita kunyumba yamalilo kusiyana ndi kupita kunyumba yamadyelelo, cifukwa amenewo ndiwo mapeto a anthu onse. Cotelo munthu amene ali moyo aziganizila zimenezi mumtima mwake.”—Mlaliki 7:2.

      ZIMENE MUNGACITE PALIPANO MUKAFEDWA | CIDULE CAKE

      • 1: LANDILANI THANDIZO KWA ACIBULULU NA MABWENZI

        Malinga na zimene mufunikila, gaŵani bwino nthawi yokhala na ena komanso yokhala pamwekha.

      • 2: MUZIDYA ZAKUDYA ZOPATSA THANZI, KOMANSO MUZICITA MASEŴELA OLIMBITSA THUPI

        Muzidya zakudya zopatsa thanzi, kumwa madzi kwambili komanso kucitako maseŵela olimbitsa thupi mwa saizi.

      • 3: MUZIGONA MOKWANILA

        Dziŵani kuti kugona n’kofunika kwambili kuti mulimbane na maganizo olefula, obwela cifukwa ca cisoni.

      • 4: SEŴENZETSANI NJILA ZOTHANDIZA KWA IMWE

        Popeza kuti anthu amalila malilo mosiyana-siyana, sankhani mfundo zimene zingakhale zothandiza kwa imwe.

      • 5: PEWANI ZIZOLOŴEZI ZOKUWONONGANI

        Pewani kumwa moŵa mopitilila malile komanso kuseŵenzetsa amkola bongo. Cifukwa izi zingakuonjezeleni mavuto.

      • 6: MUZISEŴENZETSA BWINO NTHAWI YANU

        Muzipezako nthawi yoceza na ena komanso yocita zosangalatsa.

      • 7: PITILIZANI KUTSATILA PULOGILAMU YANU YA ZOCITA

        Zinthu zingakhalenso bwino ngati mutsatila pulogilamu ya zocita zanu za tsiku na tsiku.

      • 8: PEWANI KUPANGA ZOSANKHA ZIKULU-ZIKULU MWAMSANGA

        Ngati n’kotheka, yembekezelani kwa caka cimodzi kapena kuposelapo musanapange zosankha zikulu-zikulu zimene pambuyo pake mungadziimbe nazo mlandu.

      • 9: MUZIM’KUMBUKILA WOKONDEDWA WANU

        Sungani masinapu na zinthu zina zokukumbutsani wokondedwa wanu amene anamwalila, kapena kukhala na kabuku kolembamo zocitika zimene mungafune kuti muzim’kumbukila nazo.

      • 10: PEZANI NTHAWI YOCITA ZOSANGALATSA

        Pezani nthawi yocita zinthu zina zosiyanako na zimene mumacita tsiku na tsiku, olo kwa tsiku limodzi kapena kwa maawazi ocepa cabe.

      • 11: MUZITHANDIZA ENA

        Pangani umoyo wanu kukhala wa phindu mwa kuthandiza anthu amene afunikila citonthozo, kuphatikizapo ena amene akhudzidwa na imfa ya wokondedwa wanu.

      • 12: YANG’ANANINSO ZOCITA ZANU KUTI MUONE ZOFUNIKA KWENI-KWENI

        Seŵenzetsani nthawi imeneyi kuti muone zimene n’zofunika kwambili. Ndipo ngati m’pofunika, sinthani zina mwa zimene mumacita.

      Kukamba zoona, palibe cimene cingatsiliziletu cisoni cobwela na imfa. Komabe, ambili amene anataikilidwa okondedwa awo, aona kuti kucita zimene tafotokoza m’nkhani ino, kwaŵathandiza kupeza citonthozo. Koma sikuti tapeleka njila zonse zocepetsela cisoni. Mukayesa kuseŵenzetsa zina mwa njila zimenezi, mudzaona kuti zidzakuthandizani kucepetsa cisoni.

      a Galamuka! siiuza anthu zocita pa nkhani ya zakudya

  • Thandizo Lodalilika Kwambili Kwa Ofedwa
    Galamuka!—2018 | No. 3
    • Anthu ali m’Paradaiso ndipo ni okonzeka kulandila okondedwa awo amene aukitsidwa

      THANDIZO KWA OFEDWA

      Thandizo Lodalilika Kwambili Kwa Ofedwa

      M’ZAKA ZAPITA, PACITIKA AKAFUKU-FUKU AMBILI POFUNA KUPEZA MALANGIZO OTHANDIZA KWA AMENE ATAIKILIDWA MUNTHU AMENE AMAM’KONDA. Koma monga tafotokozela m’nkhani yapita, malangizo amene akatswili amapeleka, kambili amagwilizana na nzelu zakale zopezeka m’Baibo. Izi zionetsa bwino kuti malangizo a m’Baibo ni odalilika nthawi zonse. Baibo siipeleka cabe malangizo odalilika. Koma imapelekanso malangizo amene sapezeka kwina kulikonse ndipo amapeleka citonthozo cabwino koposa kwa ofedwa.

      • Citsimikizo cakuti okondedwa athu amene anamwalila sakuzunzika

        Pa Mlaliki 9:5 Baibo imakamba kuti: “Akufa sadziwa ciliconse.” Imakambanso kuti, “zonse zimene anali kuganiza zimathelatu.” (Salimo 146:4) Mogwilizana na zimenezi, Baibo imayelekezela imfa na kugona mwamtendele.—Yohane 11:11.

      • Kukhala na cikhulupililo colimba mwa Mulungu wacikondi kumatonthoza

        Baibo pa Salimo 34:15 imakamba kuti: “Maso a Yehovaa ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.” Kuonjezela pa kuuzako wina mmene timvelela, kufotokozela Mulungu m’pemphelo ndiye kothandiza kwambili kuti tipeze citonthozo. Ndipo kumatithandiza kukhala pa ubwenzi na Mlengi wathu, amene angaseŵenzetse mphamvu zake kutitonthoza.

      • Tsogolo labwino kwambili limene mungayembekezele

        Ganizilani za nthawi pamene ali m’manda adzaukitsidwa kukhalanso na moyo pano padziko lapansi! Baibo imakamba za nthawi imeneyo mobweleza-bweleza. Pofotokoza za mmene umoyo udzakhalila panthawiyo, Baibo imati, Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

      Ambili amene amakhulupilila Yehova, Mulungu wa Baibo, amapeza mphamvu zoculuka zowathandiza kupilila cisoni, cifukwa anaphunzila za ciyembekezo cakuti adzaonananso na okondedwa awo amene anamwalila. Mwacitsanzo, Ann amene mwamuna wake anamwalila pambuyo pokhala naye m’cikwati kwa zaka 65 anati: “Baibo imanitsimikizila kuti okondedwa athu amene anamwalila sakuzunzika, ndipo Mulungu adzaukitsa onse amene akuwakumbukila. Nthawi iliyonse nikamvela cisoni, nimakumbukila mfundo imeneyi. Zotulukapo zake n’zakuti, nakwanitsa kupilila vuto lalikulu kwambili limene n’nali nisanakumanepo nalo mu umoyo wanga!”

      Tiina amene tam’chula m’magazini ino anati: “Kucokela pamene a Timo anamwalila, Mulungu wakhala akunithandiza. Nakhala nikuona dzanja la Yehova m’nthawi zovuta. Ndipo lonjezo ya m’Baibo ya ciukililo ni yeni-yeni kwa ine. Imanilimbikitsa kuti nipitilize kupilila mpaka pa tsiku limene nidzaonananso na a Timo.”

      Izi n’zimenenso angakambe anthu ofika mamiliyoni amene amakhulupilila Baibo. Ngati mumaona kuti zimene Baibo imakamba si zeni-zeni kapena ni maloto cabe, mungacite bwino kuiphunzila mozama kuti mupeze umboni wakuti malangizo na malonjezo ake ni othandiza maningi. Mukacita zimenezo, mudzapeza kuti Baibo ni imene ingathandize kwambili anthu ofedwa.

      DZIŴANI ZAMBILI ZA CIYEMBEKEZO CA KUUKA KWA AKUFA

      Tambani mavidiyo ogwilizana na nkhani imeneyi, pa webusaiti yathu ya jw.org.

      Anthu ali m’Paradaiso ndipo ni okonzeka kulandila okondedwa awo amene aukitsidwa

      Baibo inalonjeza za nthawi pamene tidzalandilanso okondedwa athu amene anamwalila

      KODI AKUFA ALI MU MKHALIDWE WANJI?

      Kodi Akufa Ali mu Mkhalidwe Wabwanji?

      Kodi cimacitika n’ciani munthu akamwalila? Yankho yomveka bwino imene Baibo imapeleka pa funso iyi ni yotonthoza komanso yodalilika

      Yendani polemba kuti MABUKU > MAVIDIYO (Yendani pa Mbali Yakuti Mavidiyo: Baibo > Ziphunzitso za m’Baibulo)

      KODI MUNGAKONDE KUMVELAKO UTHENGA WABWINO?

      Kodi Mungakonde Kumvelako Uthenga Wabwino?

      M’dziko lodzala mauthenga oipa, kodi mungaupeze kuti uthenga wabwino? Vidiyo imeneyi ifotokoza za kabuku kakuti, Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu.

      Yendani polemba kuti MABUKU > MAVIDIYO (Yendani pa Mbali Yakuti Mavidiyo: Misonkhano na Utumiki wathu > Zida Zosewenzetsa mu Ulaliki)

      a Yehova ni dzina la Mulungu lopezeka m’Baibo.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani