LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 11/12 tsa. 2
  • Mungakwanitse—Musadzidelele

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mungakwanitse—Musadzidelele
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mungathandize pa Nchito Yopanga Ophunzila?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mungakwanitse—Ngakhale Muli ndi Zocita Zambili
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Kodi Mumakwanilitsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kodi Mumaona Kufunika Kophunzitsa Ena?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
km 11/12 tsa. 2

Mungakwanitse—Musadzidelele

1. N’cifukwa ninji anthu ena amadodoma kuyambitsa phunzilo la Baibo?

1 Kodi mumaopa kuyambitsa phunzilo poganiza kuti mulibe luso lophunzitsa? Panthawi zina atumiki okhulupilika akale, monga Mose ndi Yeremiya, naonso anadziona kukhala osayenelela maudindo ao. (Eks. 3:10, 11; 4:10; Yer. 1:4-6) Motelo, nkhawa imeneyo si yacilendo. Nanga tingaithetse bwanji?

2. N’cifukwa ciani sitiyenela kumangolalikila khomo ndi khomo, n’kusiila ena nchito yotsogoza maphunzilo a Baibo?

2 Tizikumbuka kuti Yehova sangatipemphe kucita zimene sitingakwanitse. (Sal. 103:14) Mwa ici, Mulungu potipatsa nchito ‘yopanga ophunzila ndi kuwaphunzitsa,’ adziŵa kuti tingaikwanitse. (Mat. 28:19, 20) Conco, mwai umenewu Yehova sanaupeleke kokha kwa anthu acidziŵitso kwambili, kapena aja aluso lapamwamba ai. (1 Akor. 1:26, 27) N’cifukwa cake, sitiyenela kumangolalikila khomo ndi khomo cabe, ndi kusiila ena nchito yotsogoza maphunzilo a Baibo.

3. Kodi Yehova watiyeneletsa motani kuti tizigwila nchito yotsogoza maphunzilo a Baibo?

3 Yehova Ndiye Amatiyeneletsa: Ziyeneletso zathu kuti tizipanga ophunzila zimacokela kwa Yehova. (2 Akor. 3:5) Kupyolela m’gulu lake iye watiphunzitsa mfundo za coonadi ca m’Baibo, zimene ngakhale anthu omwa maphunzilo apamwamba a m’dzikoli sazidziŵa. (1 Akor. 2:7, 8) Njila zophunzitsila zimene Mphunzitsi Wamkulu, Yesu, anagwilitsila nchito pophunzitsa, zinasungidwa m’Mau a Mulungu kuti tizitsatile. Ndipo Mulungu akupitiliza kutiphunzitsa kupyolela mu mpingo. Komanso, Yehova sanatilekelele kuti tidzipezele tokha zogwilitsila nchito pophunzitsa Baibo. Iye watipatsa zida monga buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa, zimene zimalongosola coonadi m’njila yotsatilika ndi yosavuta kumva. Zoonadi, kutsogoza phunzilo n’kosavuta, musamaope.

4. N’cifukwa ciani tiyenela kukhulupilila kuti Yehova adzatithandiza?

4 Mose ndi Yeremiya anakwanitsa kusamalila maudindo ao ndi thandizo la Yehova. (Eks. 4:11, 12; Yer. 1:7, 8) Ifenso tingapemphe Yehova kuti atithandize. Ndi iko komwe, tikamaphunzitsa munthu Baibo, timakhala tikum’phunzitsa coonadi conena za Yehova, ndipo Mulungu amakondwela nazo. (1 Yoh. 3:22) Motelo, khalani n’colinga cogwila nao nchito yotsogoza maphunzilo a Baibo. Imeneyi ndiyo mbali yosangalatsa ndi yopindulitsa koposa ya ulaliki.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani