“Ndidzatenga Mabuku Anu Mukatenga Anga”
Umu ndi mmene eni nyumba ena amayankhila. Popeza kuti sitimasinthanitsa mabuku athu ophunzilila Baibo ndi mabuku amene amafalitsa zinthu zolakwika, kodi anthu tingawayankhe bwanji mwaluso? (Aroma 1:25) Tinganene kuti: “Zikomo kwambili pondipatsa mabuku anu. Kodi bukuli limakamba kuti n’ciani cidzathetsa mavuto a anthu? [Yembekezani yankho. Akakuuzani kuti mukaŵelenge mabuku ake kuti mupeze yankho, muuzeni kuti simugaŵila mabuku popanda kumuuza zimene mabukuwo amanena. Ndiyeno ŵelengani kapena gwilani mau a Lemba la Mateyu 6:9, 10.] Yesu ananena kuti Ufumu wa Mulungu udzacititsa kuti cifunilo ca Mulungu cicitike padziko lapansi. Conco, mabuku okha a cipembedzo amene ndimaŵelenga ndi aja amene amafotokoza kwambili za Ufumu wa Mulungu. Kodi ndingakuonetseni m’Baibo zinthu zina zimene Ufumu wa Mulungu udzacita?”